Saturday, April 27, 2024

LAMULUNGU LA 05 MU NYENGO YA PASAKA– B

LAMULUNGU LA 05 MU NYENGO YA PASAKA– B.

“Khalani mwa Ine, ndipo mudzabala zipatso zambiri.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 09: 26 – 31. (Barnabasi adawafotokozera za m’mene Saulo adaaonera Ambuye panjira paja.)

 

Saulo atafika ku Yerusalemu, adayesa kulowa m’gulu la ophunzira aja. Koma onse adachita naye mantha, osakhulupirira kuti nayenso ndi wophunzira. Pamenepo munthu wina, dzina lake Barnabasi, adamtenga napita naye kwa atumwi. Iye adawafotokozera za m’mene Saulo adaaonera Ambuye panjira paja, ndipo kuti Ambuye adalankhula naye. Adawasimbiranso za m’mene Saulo ku Damasiko ankalankhulira molimba mtima m’dzina la Yesu. Tsono Saulo adakhala nawo, nayendera Yerusalemu yense akulalika molimba mtima m’dzina la Ambuye. Ankalankhulanso ndi kumatsutsana ndi Ayuda olankhula Chigriki, koma iwowo ankafunafuna kumupha. Pamene abale adamva zimenezi, adaapita naye ku Kesareya namtumiza ku Tariso. Pamenepo Mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unali pa Mtendere. Udakhazikika, ndipo anthu ochuluka adalowamo chifukwa anthu ankayenda mooopa Ambuye, ndipo Mzimu Woyera ankawalimbikitsa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO  21: 26 – 28, 30 – 32.

 

Inu, Chauta, ndidzakutamandani pa gulu la anthu.

 

Zimene ndidalonjeza ndidzachita pamaso pa onse okumverani,

Ozunzika adzadya ndi kukhuta,

Ofunafuna Chauta adzamtamanda,

Mitima yanu ikhale ndi moyo nthawi zonse.

 

Inu, Chauta, ndidzakutamandani pa gulu la anthu.

 

Anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi,

Adzakumbukira nadzatembenukira kwa Chauta,

Mabanja a mitundu ina ya anthu adzampembedza,

Pakuti ulamuliro ndi wake wa Chauta,

Iye amalamula anthu a mitundu yonse.

 

Inu, Chauta, ndidzakutamandani pa gulu la anthu.

 

Zidzukulu za m’tsogolo zidzatumikira Ambuye,

Anthu adzauza mbadwo umene ukudzawo za Iye,

Adzalalika za chipulumutso chake kwa anthu,

Amene mpaka tsopano sanabadwe.

 

Inu, Chauta, ndidzakutamandani pa gulu la anthu.

 

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE: 03: 18 – 24. (Chimene Mulungu amalamula nchakuti: tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira).

 

Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu. Apo tidzadziwa kuti tili pa choona, ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu nthawi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziwa zonse. Inu okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, titha kuima mopanda mantha pamaso pa Mulungu. Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa. Chimene Mulungu amalamula nchakuti tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira. Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timamdziwa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 15: 04a, 05b.

Alleluia – Khalani mwa Ine, ndipo Inenso ndidzakhala mwa inu. Munthu wokhala mwa Ine, amabereka zipatso zambiri. – Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 15: 01 – 08. (Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa Iye, amabereka zipatso zambiri).

 

Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndi mlimi. Iwo amadula nthambi iliyonse mwa Ine imene siibala zipatso. Ndipo nthambi iliyonse yobala zipatso, amaitengulira kuti ibale zipatso zambiri koposa kale. Inu mwayera kale chifukwa cha mau amene ndakuuzani. Khalani mwa Ine, ndipo Inenso ndidzakhala mwa inu. Nthambi siingathe kubala zipatso payokha ngati siikhala mwa inu. Nthambi siingathe kubala zipatso payokha ngati siikhala pa mtengo wake. Momwemonso inu ngati simukhala mwa Ine. Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu. Ngati munthu sakhala mwa Ine, amamtaya kunja monga nthambi yodulidwa, ndipo amauma. Nthambi zotere amazitola, naziponya pa moto ndipo zimapsa. Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi. Atate anga amalemekezedwa pamene mubereka zipatso zambiri, ndipo pakutero mumaonetsa kuti ndinu ophunzira anga enieni.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Yesu amakhala mwa ife, tingathe kupempha chilichonse ndipo tidzachilandira. Tsono tiyeni, tipemphe Atate kuti agawireko anthu onse zaulere zowathandiza kupulumuka:

 

1.     Atate, mulimbitse chikhulupiriro cha atsogoleri a Mpingo kuti alalike Mthenga Wabwino wa Yesu Khristu mosaopa ndi mosakaika.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, mulunzitse akhristu ogawikana m’mipingo yosiyanasiyana kuti asaleke kufunafuna umodzi uja umene Yesu adafunira Mpingo wake.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, mulimbitse chikondi chanu m’mitima ya anthu anu okhala m’zipani, kuti abereke zipatso zambiri zokometsera Mpingo wanu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, muwamvere chifundo ana anu osokera ndi ofooka, kuti alumikizanenso ndi Yesu Khristu ndi kuwonetsa zipatso za chilungamo.
Tikupemphani, mutivomereze.

5.     Atate, mutidalitse ife tonse tili muno, kuti chikondi chathu chiwonekere pa ntchito zabwino zotumikira anzathu.
Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, mwa chifundo chanu, mverani mapemphero athuwa, ndipo mutikhalitse amodzi. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, April 20, 2024

LAMULUNGU LA 04 MU NYENGO YA PASAKA– B

LAMULUNGU LA 04 MU NYENGO YA PASAKA– B.

[LAMULUNGU LA MAITANIDWE – VOCATION SUNDAY]

“Yesu Ndiye Mbusa Wabwino wotiperekeza kwa Atate.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 04: 08 – 12. (Ili ndi dzanja lokhalo, limene lingatipulumutse).

 

Petro, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adawayankha kuti, “Inu atsogoleri ndi akuluakulu muli apa, kodi mukutifunsa ife lero za ntchito yabwino imene idachitika pa munthu wopunduka uja, ndi kuchira kwake? Mudziwetu tsono inu nonse, ndi Aisraele ena onse, kuti munthuyo akuima wamoyo pamaso panu chifukwa cha mphamvu ya dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete. Amene uja inu mudaampachika pa mtanda, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Za Yesuyo mau a Mulungu akuti, Mwala umene inu amisiri omanga nyumba mudaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koopsa. Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 01, 8 – 09, 21 – 23, 26 – 29.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.

 

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino,

Ndipo chikondi chake nchamuyaya,

Kuthawira kwa Chauta nkwabwino,

Kupambana kukhulupirira munthu.

Kuthawira kwa Chauta nkwabwino,

Kupambana kukhulupirira mfumu.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.

 

Ndikuyamikani popeza kuti mwandiyankha,

Ndipo mwasanduka Mpulumutsi wanga,

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,

Womwewo wasanduka mwala wapangodya,

Chauta ndiye amene wachita zimenezi,

Zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.

 

Ngwodala amene alikudza m’dzina la Chauta,

Tikufunirani madalitso ochokera m’nyumba ya Chauta,

Inu ndinu Mulungu wanga ndidzakuthokozani,

Thokozani Chauta pakuti ngwabwino,

Ndipo chikondi chake chosasinthika nchamuyaya.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE: 01 – 02. (Tidzamuwona Mulungu monga momwe aliri).

 

Okondeka anga, onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziwa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziwe. Inu okondedwa, ndife ana a Mulungu tsopano. Mulungu sadatiwonetsebe chimene tidzakhale. Koma tikudziwa kuti Iye akadzaoneka, tidzakhala ofanafana naye, pakuti tidzamuwona monga momwe aliri.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 10: 14.

Alleluia – Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziwa, ndipo izozo Ineyo zimandidziwa. – Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 10: 11 – 18. (Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake).

 

Yesu adati, “Ine ndine Mbusa wabwino. Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake. Koma wolembedwa ntchito chabe akaona mmbulu ulikudza, amazisiya nkhosazo iye nkuthawa. Amatero popeza kuti si mbusa weniweni, ndipo nkhosa sizake ai. Tsono mmbulu uja umagwirapo zina, zina nkumwazikana. Wolembedwa ntchito uja amathawa, chifukwa amangotsata malipiro chabe, ndipo salabadirako za nkhosazo. Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziwa, ndipo izozo Ineyo zimandidziwa, monga momwe Atate amadziwira Ine, nanenso nkuwadziwa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo. Ndili nazo nkhosa zina zimene sizili za m’khola lino. Zimenezonso ndiyenera kuzikusa. Zidzamva mau anga, ndipo padzakhala gulu limodzi mbusa wakenso mmodzi. Nchifukwa chake Atate amandikonda, popeza kuti ndikupereka moyo wanga kuti ndikautengenso. Palibe munthu wondilanda moyo wangawu, koma ndikuupereka ndekha. Ndili nazo mphamvu zoutaya moyo wanga, ndili nazonso mphamvu zoutenganso. Udindo umenewo ndidaulandira kwa Atate anga.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, popeza kuti ndife ana a Mulungu ndithu, tingathe kupemphera mosaopa ndi mosakaika. Tsono tiyeni, tipemphe Mulungu Atate athu kuti atsire madalitso ake pa anthu onse:

 

1.     Atate, mulimbitse Apapa, Aepiskopi, Ansembe onse, kuti azitsogolera akhristu ao ndi kuwasamalira, asaope kutaya moyo wao chifukwa cha nkhosa zao.
Tikukupemphani, Mutivomereze.

2.     Atate muitane anyamata ndi atsikana ku ntchito yofalitsa Mthenga Wabwino, ndipo muwalimbikitse kuti akhale mboni zenizeni za Yesu Khristu.
Tikukupemphani, Mutivomereze.

3.     Atate, muunikire anthu akunja okhala m’maiko osiyanasiyana kuti nawonso amve Mthenga Wabwino ndi kukhulupirira Yesu Khristu Mpulumutsi wao.
Tikukupemphani, Mutivomereze.

4.     Atate mutithandize ife tomwe kuti tisenze mwachangu udindo wathu wachikhristu ndipo mayendedwe athu atsimikize kuti ndifedi anthu ake a Yesu Khristu.
Tikukupemphani, Mutivomereze.

 

Atate, tikudziwa kuti palibe dzina lina loti tipulumuke nalo: nchifukwa chake tikukupemphani zonsezi m’dzina la Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, April 13, 2024

LAMULUNGU LA 03 MU NYENGO YA PASAKA– B.



LAMULUNGU LA 03 MU NYENGO YA PASAKA– B.

“Yesu ndi nsembe yokhululukira machimo athu.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 03: 13 – 15, 17 – 19. (Mudapha wopatsa moyo, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa).

 

Petro adauza anthu kuti, “Inu Aisraele, Mulungu wa makolo athu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, adapereka ulemerero kwa Yesu, mtumiki wake. Inu mudampereka kwa adani ake ndi kumkana pamaso pa Pilato, pamene Pilatoyo adaatsimikiza kuti ammasula. Yesu anali woyera mtima ndi wolungama, koma inu mudamkana, ndipo m’malo mwake mudapempha kuti akumasulireni chigawenga. Mudapha Wopatsa moyo, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi. Ndiponso tsopano abale anga, ndikudziwa kuti inu ndi akuluakulu anu mudachita zimenezi mosadziwa. Koma Mulungu adaaneneratu mwa aneneri onse kuti wodzozedwa wake wolonjezedwa uja adzamva zowawa, ndipo zidachitikadi momwemo. Tsono tembenukani mtima ndi kubwera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthawi ya mpumulo.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 04: 02, 04, 07, 09.

 

Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.

 

Ndikamaitana, mundiyankhe Inu Mulungu, Mtetezi wanga,

Mudabwera pamene ndinali m’mavuto,

Mundichitire chifundo, ndi kumvera pemphero langa.

 

Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.

 

Koma tsono mudziwe kuti Chauta,

Wadzipatulira Iye yemwe anthu olungama,

Chauta amamva ndikamuitana.

 

Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.

 

Ndani angatiwonetse zabwino?

Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.

 

Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.

 

Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,

Pakuti Inu nokha Chauta,

Ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.

 

Mutiyang’ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE 02: 01 – 05. (Yesu Khristu ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati anthu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi).

 

Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama. Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo anthu, ndipo osati athu okha, komanso anthu a pa dziko lonse lapansi. Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziwa. Munthu akamati, Ine ndimadziwa Mulungu, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona. Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 24: 32.

Alleluia – Ambuye Yesu, mutithandize malembo. Mitima yathu iyake mwa ife pamene mumalankhula nafe. – Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 24: 35 – 48. (Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zowawa, nkuuka kwa akufa Patapita masiku atatu).

 

Ophunzira awiri aja adafotokoza zimene zidaachitika panjira, ndiponso m’mene iwo adaamzindikira pamene Iye ankanyema buledi. Iwo akulankhula choncho, Yesu mwiniwake adadzaimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu.” Koma iwo adadzidzimuka, nkuchita mantha poyesa kuti akuwona mzukwa. Tsono Yesu adati, “mukuvutikiranji, mukudzipheranji ndi mafunso a m’mitima mwanu? Onani manja anga ndi mapazi anga, kuti ndine ndithu. Khudzeni muwone, paja mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuwona kuti Ine ndili nazo.” Atanena zimenezi adawaonetsa manja ake ndi mapazi ake. Iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe, ndipo adaathedwa nzeru. Tsono Yesu adawafunsa kuti, “kodi pano muli nako kanthu kakudya?” Adampatsa chidutsu cha nsomba yootcha. Iye atalandira nsombayo, adaidya iwo akuwona. Kenaka adawauza kuti, “nzimenezitu zimene ndinkakuuzani pamene ndinali nanu. Paja ndinkanena kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m’Malamulo a Mose, m’mabuku a aneneri, ndi m’buku la Masalimo.” Tsono adawathandiza kuti amvetse bwino Malembo. Adawauza kuti, “zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zowawa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, kuti m’dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu awakhululukire machimo ao. Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale pakuti tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, imene ili Yesu Khristu, tingathe kupempha kwa Atate mosakaika zabwino zonse zotisowa:

 

1. Akhristu onse amutsire Yesu Khristu umboni pakuyenda m’chikondi chake ndi kusunga malamulo ake.

Tikupemphani, mutivomereze.

2. Anthu amafuko onse atembenukire kwa Mulungu ndi mtima wolapa pokhulupirira chifundo chake chofuna kuwapulumutsa.

Tikupemphani, mutivomereze.

3. Anthu odwala onse ndi onse amene ali otaya mtima alandire chisangalatso panthawi ino ya Pasaka.

Tikupemphani, mutivomereze.

4. Ife amene tili muno tikhale nawo mtima wokonda kuwerenga mawu a m’Malembo Oyera, kuti tipezemo mphamvu zolimba pa moyo wathu wa chikhristu.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukuyamikani chifukwa mwa Mwana wanu Yesu Khristu mumatikhululukira mobwerezabwereza, kuti tiziyenda pamaso panu ndi mtima womasuka ndi kukhazikika m’chikondi chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, April 6, 2024

LAMULUNGU LA CHIWIRI MU NYENGO YA PASAKA– B

LAMULUNGU LA CHIWIRI MU NYENGO YA PASAKA  – B

(LAMULUNGU LA CHIFUNDO CHA MULUNGU)

“Iwo adakondwa kwambiri poona Ambuye.”

 

MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 04: 32 – 35. (Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi).

 

Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “zimene ndili nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse. Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankawakomera mtima kwambiri. Panalibe munthu wosowa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. Ndipo ndalamazo ankagawira munthu aliyense malinga ndi kusowa kwake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 118: 02 – 04, 15 – 18, 22 – 24.

 

Tamandani Chauta Pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

 

Aisraele anene kuti,

“Chikondi chake nchamuyaya.

Banja la Aroni linene kuti, 

Chikondi chake nchamuyaya.

Anthu oopa Chauta anene kuti,

Chikondi chake nchamuyaya.

 

Tamandani Chauta Pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

 

Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,

Dzanja lamanja la Chauta lapambana,

Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”

Sindidzafa, ndidzakhala moyo,

Ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.

Chauta wandilanga koopsa, koma sadandisiye kuti ndife.

 

Tamandani Chauta Pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

 

Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana

Womwewo wasanduka mwala wapangodya.

Chauta ndiye amene wachita zimenezi,

Zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga.

Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

 

Tamandani Chauta Pakuti Iye ndi wabwino, chikondi chake nchamuyaya.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YOYAMBA YA YOHANE WOYERA: 01 YOHANE 05: 01 – 06. (Aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi).

 

Okondeka anga, munthu aliyense wokhulupirira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, iyeyo ndi mwana wa Mulungu. Ndipo aliyense wokonda nakubala, amakonda ndi mwana wake yemwe. Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nchakuti timakonda Mulungu ndi kutsata malamulo ake. Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa. Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma okhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu. Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amene amachitirapo umboni, pakuti Mzimuyo ndiye choona.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 20: 29.

Alleluia – Yesu adati, wakhulupirira chifukwa wandiona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone. – Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 20: 19 – 31. (Patapita masiku asanu ndi atatu, Yesu adabwera).

 

Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adawaonetsa manja ake ndi m’nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri powaona Ambuyewo. Yesu adatinso, mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi awiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adabwera. Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “ife tawaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “ndikapapanda kuwona mabala a misomali m’manja mwao, ndi kupisa chala changa m’mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m’nthiti mwao, sindingakhulupirire konse.” Patapita masiku ndi atatu, ophunzira aja analinso m’nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere, koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adauza Tomasi kuti, “ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m’nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.”  Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!” Yesu adati, “kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.” Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m’buku muno. Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m’dzina lake.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Yesu Khristu waimirira pakati pathu, tiyeni, pamodzi naye, tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti apitirize ntchito zake zopulumutsa anthu onse:

 

1.     Mzimu Woyera alimbitse chikhulupiriro m’mitima ya akhristu, ndipo awalumikize onse pamodzi m’chikondi choona.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anthu a mafuko onse akhale ogwirizana mwaubale, ndipo a m’maiko okwera ayesetse kuthandiza anzao a m’maiko ena, pakuwagawirako chuma chao.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akatekumeni alimbikire pa maphunziro ao, pozindikira kuwala kwa Yesu Khristu kowatsogolera ku moyo wosatha.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse tikhale a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi, monga akhristu oyamba aja, makamaka pakuthandiza anzathu amene ali m’mavuto.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, tikukuyamikani, chifukwa poukitsa Mwana wanu kwa akufa, mudatitsimikizira chifundo chanu chotipulumutsa. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...