Saturday, March 25, 2023

 

LAMULUNGU LA 05 MU NYENGO YA LENTI – CHAKA A

“Woukitsa anthu kwa akufa ndine.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI EZEKIELE; EZEKIELE 37: 12 – 14 (Ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo).

 

Ine Ambuye Chauta ndikuti, “inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo. Ndidzakubwezerani ku dziko la Israele. Motero Mudzadziwa kuti ine ndine Chauta, ndikadzafukula manda anu ndi kukutulutsanimo, inu anthu anga. Tsono ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo, pambuyo pake ndidzakukhazikani m’dziko lanu. Choncho Mudzadziwa kuti ine Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero ine Chauta.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 130: 01 – 04. 05 – 08.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Ndikulirira Inu Chauta, ndili m’dzenje lozama lamavuto,

Ambuye imvani liwu langa,

Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga.          

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Inu Chauta, mukadawerengera machimo,

Ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye?

Koma inu mumakhululukira,

Nchifukwa chake timakulemekezani.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta,

Ndimayembekeza ndi mtima wonse ndipo ndimakhulupirira mau ake,

Mtima wanga umayembekeza Chauta,

Kupambana m’mene alonda amayembekeza mbandakucha, Iwe Israele, khulupirira Chauta.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika,

Ndi wokonzeka kupulumutsa,

Adzaombola Israele ku machimo ake onse.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 08: 08 – 11 (Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu).

 

Abale, anthu oipa mtima pa khalidwe limenelo, sangathe kukondweretsa Mulungu. Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufawa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 11: 25a, 26.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Ine Ndine kuuka ndinso moyo, aliyense wokhulupirira Ine sadzafa. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 11: 01 – 45 (Ine Ndine kuuka ndinso moyo).

 

Panali munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadwala. Anali wa ku mudzi wa Betaniya, kwao kwa Maria ndi mbale wake Marita. Mariayo ndi yemwe uja amene adaadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira, nkupukuta mapazi ao ndi tsitsi lake. Lazaro ankadwala yo anali ndi mlongo wake. Tsono alongo ake aja adatumiza thenga kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, bwenzi lanu uja akudwala.” Pamene Yesu adamva zimenezi adati, “kudwalako safanako ai, koma zatero kuti Mulungu alemekezedwe, ndipo kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.” Ndiye kuti Yesu ankakonda Marita ndi mng’ono wake Maria ndiponso Lazaro. Komabe pamene adamva za matendawo, Yesu adaswera masiku awiri pamalo pomwe adaaliripo. Pambuyo pake adawuza ophunzira ake kuti, “tiyeni tipitenso ku Yudeya.” Ophunzira akewo adati, “Aphunzitsi, tsopano apa Ayuda ankafuna kukuponyani miyala, ndiye mukuti mupitenso komweko?”  Yesu adati, “kodi suja usana uli ndi maora khumi ndi awiri? Munthu akayenda masana, sakhumudwa, chifukwa amaona kuwala kwa dzikoku. Koma akayenda usiku, amakhumudwa chifukwa kuwalako alibe.” Atatero adawauza kuti, “Lazaro bwezi lathu, wagona tulo, koma ndipite kuti ndikamudzutse ku tulo taketo.” Apo ophunzira ake adati, “Ambuye, ngati wagona tulo, achira.” Iwo ankayesa kuti akunena za tulo teniteni, koma Yesu ankanena za imfa yake ya Lazaro. Tsono Yesu adawauza mosabisa kuti, “Lazaro wamwalira, komabe chifukwa cha inu ndikukondwera kuti ine kunalibe kumeneko, kuti choncho mukakhulupirire. Tiyeni tipiteko.” Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, adauza ophunzira anzake kuti, “tiyeni ifenso tipite nao kuti tikafe naye pamodzi.”

 

Pamene Yesu adafika ku Betaniya, adapeza Lazaro atagona m’manda masiku anai. Ku Betaniya kunali kufupi ndi ku Yerusalemu, mtunda wokwanira pafupi makilomita atatu. Panali anthu ambiri amene adaabwera kwa Marita ndi Maria kudzawapepesa chifukwa cha imfa ya mlongo wao. Pamene Marita adamva kuti Yesu akubwera, adapita kukamchingamira. Koma Maria adaatsalira m’nyumba. Tsono Marita adauza Yesu kuti, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira. Koma ngakhale tsopano, ndikudziwa kuti Mulungu adzakupatsani zilizonse mungapemphe.” Yesu adamuuza kuti, “Mlongo wako adzauka.”  Marita adati, “ndikudziwa kuti adzauka podzauka anthu kwa akufa pa tsiku lomaliza.” Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso wowapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?” Iye adati, “Inde Ambuye, ndikukhulupirira kuti inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, mwana wa Mulungu, amene adayenera kubwera pansi pano.” Marita atanena zimenezi, adaitanira paseri Maria mng’ono wake namuuza kuti, “afika Aphunzitsi, akukuitana.” Maria atamva zimenezi, adanyamuka msangamsanga, nadza kwa Yesu. Pamenepo nkuti Yesu asanafike kumudziko, koma anali chikhalire pamalo pomwe Marita adaakumana naye. Anthu amene anali m’nyumba akupepesa Mariayo, ataona kuti wanyamuka msangamsanga ndikutuluka, adamtsatira. Ankayesa kuti akupita kumanda kukhalira kumeneko.

 

Maria atafika pamene panali Yesu, namuona, adadzigwetsa kumapazi kwake nati, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira.” Yesu ataona Maria akulira, ndiponso anthu amene adadza naye iwonso akulira, zidamukhudza kwambiri ndipo adavutika mu mtima. Tsono adawafunsa kuti, “mudamuika kuti?” Iwo adati, “Ambuye, tiyeni mukaone.” Yesu adayamba kulira. Pamenepo anthu aja adati, “Onani, ankamukonda zedi.” Koma ena mwa iwo adati “Munthu uyu suja adapenyetsa munthu wosapenya uja? Monga sakadatha kuchitapo kanthu kuti Lazaro asafe?” Yesu adavutikanso mu mtima, nakafika ku manda amene anali phanga. Pakhomo pake panali chimwala. Tsono adati, “tachotsani chimwalacho.” Marita, mlongo wa womwalirayo, adamuuza kuti, “pepani Ambuye, wayamba kale kununkha, pakuti wagonamo masiku anai.” Yesu adamufunsa kuti, “kodi sindinakuuze kuti ukakhulupirira uwona ulemerero wa Mulungu?” Tsono anthu adachotsa chimwala chija. Yesu adayang’ana kumwamba nati, “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimvera. Ndikudziwa kuti mumandimvera nthawi zonse. Koma ndanena zimenezi chifukwa cha khamu la anthu amene ali panowa, kuti akhulupirire kuti ndinu mudandituma.” Atatero adaitana mokweza mau kuti, “Lazaro, tuluka.” Pomwepo munthu amene adaamwalirayo adatuluka, miyendo yake ndi manja ake zili zomangidwa ndi nsalu zamaliro. Nkhope yake inali yokutidwa ndi nsalu. Yesu adawauza kuti, “mmasuleni, ndipo mlekeni azipita.” Ambiri mwa anthu amene adaabwera kwa Maria, adaona zimene Yesu adachita, ndipo adakhulupirira.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, popeza kuti Mzimu wake wa Khristu akhala mwa ife, tiyeni tipemphere ndi chikhulupiriro, podziwa kuti Mulungu adzatipatsa zili zonse zimene tingamupemphe:

 

1.     Atsogoleri olalika mau a Mulungu apitirire kulimbitsa mitima ya anthu, powalalikira za kuuka kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Adokotala ndi anamwino ogwira ntchito m’zipatala, aonetse anthu odwala mtima wachifundo powasamalira bwino.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Anthu amene ali pafupi kufa ndinso onse amene ali ofedwa, aike chikhulupiriro chao mwa Yesu Khristu, kuti Iyeyo awalimbikitse.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tomwe tili muno, Mzimu Woyera apititize ntchito yake mwa ife potiwongolera m’njira ya ungwiro ndi ya chikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, tikukuyamikani chifukwa mwa Mzimu Woyera wanu mwatipatsa chiyembekezo cha kukondwera pamodzi nanu mpaka muyaya. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, March 18, 2023

LAMULUNGU LA 04 MU NYENGO YA LENTI – CHAKA A

“Tiyende m’kuwala kwa Yesu Khristu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA SAMUELE; 01 SAMUELE 16: 01b, 06 – 07, 10 – 13a (Davide adzozedwa kukhala mfumu).

 

Chauta adauza Samuele kuti, “kodi udzakhala ukumulirabe Saulo mpaka liti, poti ndamkana kuti akhalenso mfumu yolamulira Aisraele? Dzaza mafuta m’nsupa yakoyi. Upite kwa Yese wa ku Betelehemu, poti ndadzipezera mfumu pakati pa ana ake aamuna.” Onsewo atafika, Samuele adayang’ana Eliyabu namaganiza kuti, “nthithudi amene Chauta adamsankha ndi uyu ali pamaso pakeyu.” Koma Chauta adauza Samuele kuti, “usayang’ane maonekedwe ake, ngakhale kutalika kwa msinkhu wake, poti ndamkana ameneyo. Chauta sapenya monga m’mene apenyera anthu. Anthu amapenya zakunja, koma Chauta amapenya zamumtima.” Tsono Yese adatumiza ana ake aamuna asanu ndi awiri kuti apite kwa Samuele. Koma Samuele yo adati, “Chauta sadawasankhe amenewa.” Tsono adafunsa Yese kuti, “kodi ana ako aamuna ndi okhawa?” Yese yo adati, “alipo wina wamng’ono, mzime, amene watsala, koma iyeyo akuweta nkhosa.” Apo Samuele adauza Yese kuti, “mtumireni munthu, akamtenge, pakuti sitipereka nsembe mpaka iyeyo atabwera pano.” Choncho adatuma munthu kukamutenga, ndipo adabwera naye.  Anali wofiira ndi wamaonekdwe okongola ochititsa kaso. Pamenepo Chauta adati, “ndi ameneyu, mdzoze.” Samuele adatenga nsupa yamafuta, namdzoza pamaso pa abale ake. Ndipo mzimu wa Chauta udamlowa Davide mwamphamvu kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo mwake. Pambuyo pake Samuele adanyamuka napita ku Rama.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 23: 01 – 30a, 03b – 04 – 06.

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu,

Amandigoneka pa busa lamsipu,

Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Amatsitsimutsa moyo wanga,

Amanditsogolera m’njira za chilungamo,

Malinga ndi ulemerero wa dzina lake,

Ngakhale ndiyende m’chigwa chamdima wabii,

Sindidzaopa choipa chilichonse,

Pakuti Inu Ambuye mumakhala nane,

Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona,

Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta,

Mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

 

Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu,

Zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga,

Ndidzakhala m’Nyumba mwanu moyo wanga wonse.

 

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO; AEFESO 05: 08 – 14 (Dzuka wam’tulo iwe, uka kwa akufa.).

 

Abale, inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m’kuwala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m’kuwala. Pajatu pamene pali kuwala, pamapezekanso ubwino wonse, chilungamo chonse ndi choona chonse. Muziyetsa kudziwa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye. Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muwatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi. Koma kuwala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera. Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuwala. Nchifukwa chake amati, “dzuka wamtulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuwalira.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 08: 12.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Ine ndine kuwala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mumdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 09: 01 – 41 (Munthuyo adapitadi, adakasamba, nabwerako akupenya).

 

Pamene Yesu ankayenda, adaona munthu wa Khungu lobadwa nalo. Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi adachimwa ndani kuti munthu ameneyu abadwe wakhungu? Adachimwa ndi iyeyu kapena makolo ake?” Yesu adati, “sikuti iyeyu adachimwa kapena makolo ake ai. Koma adabadwa wakhungu kuti Mulungu aonentse ntchito zake mwa iye. Kukali usana tizigwira ntchito za Atate amene adandituma. Usiku ukudza pamene munthu sangathe kugwira ntchito.

Pamene ndili pansi pano, ndine kuwala kounikira anthu onse.” Atanena zimenezi, Yesu adalavulira malovu pansi, nakanda thope ndi malovuwo. Kenaka adapaka thopelo m’maso mwa munthuyo, namuuza kuti, “pita ukasambe ku dziwe la Siloamu.” (tanthauzo la Siloamu ndiye kuti, wotumidwa). Munthuyo adapitadi, adakasamba, nabwerako akupenya. Pamenepo anzake ndi anthu amene kale ankamuwona akupemphapempha adati, “kodi uyu si uja ankakhala pansi apa nkumangopempha?” Ena adati, “ndiye amene.” Ena nkumati, “iyai, akungofanana naye.” Koma mwini wakeyo adati, “ai ndithu, ndine amene.” Apo anthu aja adamufunsa kuti, “nanga maso ako akupenya bwanji?” Iyeyo adati, “munthu uja amati Yesu yu anakanda thope nalipaka m’maso mwangamu. Kenaka anadiwuza kuti, ‘pita, ukasambe ku Siloamu.’ Ndinapitadi, ndipo nditasamba, ndayamnba kupenya.’ Anthuwo adamfunsa kuti, “iyeyo ali kuti?” Munthu uja adati, “kaya, sindikudziwa.”

 

Tsono munthu uja kale sankapenyayu adapita naye kwa Afarisi. Tsiku limene Yesu adaakanda thope namchiritsalo linali la sabata. Tsono Afarisi nawonso adamufunsa munthu uja kuti, “iwe, wapenya bwanji?” Iye adawauza kuti, “anandipaka thope m’maso mwanga, ine nkukasamba, ndipo tsopano ndikupenya.” Afarisi ena adati, “munthu amene uja ngwosachokera kwa Mulungu, chifukwa satsata lamulo lokhuza tsiku la sabata.” Koma ena adati, “kodi inu, munthu wochimwa nkuchita zizindikiro zozizwitsa zotere?” Choncho panali kutsutsana. Choncho Afarisi aja adamufunsanso munthu uja kale sankapenyayu, adati, “kodi iweyo ukutipo chani za iyeyo, m’mene wakuchiritsamu?” Iye adati, “ndi mneneritu basi.” Koma akulu a Ayuda wo sadakhulupirire kuti munthu yo kale sankapenya ndipo tsopano akupenya, mpaka anaitanitsa makolo ake. Tsono adawafunsa kuti, “kodi inu, uyu ndi mwana wanu? Ndiye mukuti adaabadwadi wosapenya? Nanga zatani kuti tsopano akupenya?” Makolo ake adati, “chimene tikudziwa ife nchakuti ameneyu ndi mwana wathu, ndipo adaabadwadi wosapenya. Koma kuti tsopano akupenya, sitikudziwa m’mene zachitikira. Zoti wamupenyetsa ndani kaya, ife sitikudziwanso. Mufunseni mwiniwakeyo, ngwamkulu, afotokoze yekha.” Makolo akewo adaatero chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Pakuti Ayuda anali atapangana kale kuti, ngati munthu adzavomereza kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzamdula ku mpingo. Nchifukwa chake makolo akewo adati, “ngwamkulu, mufunseni mwiniwakeyo.”

 

Pamenepo Ayuda aja adamuitana kachiwiri munthu uja kale sankapenyayu, namuuza kuti, “Lemekeza Mulungu, ndipo unene zoona. Ife tikudziwa kuti munthu uja ngwochimwa.” Iye adati, “zakuti iye ngwochimwa, ine sindikudziwa. Chinthu chimodzi chokha ndikudziwa, kuti kale ndinali wosapenya, koma tsopano ndikupenya.” Iwo adamufunsa kuti, “kodi anachita chiyani, pamene anakupenyetsa?” Iye adati, “ndakuuzani kale, koma simumasamalako. Nanga chifukwa chani mukufuna kuzimvanso? Kapenatu nanunso mukufuna kukhala ophunzira ake eti?” Pamenepo iwo adayamba kumlalatira, adati, “wophunzira wake ndi iweyo. Ife ndifetu ophunzira a Mose. Tikudziwa kuti Mulungu adalankhula ndi Mose, koma uyu sitikudziwa kumene wachokera.” Munthuyo adati, “pakudabwitsatu mpamenepa: kuti inuyo simukudziwa kumene iye wachokera, komabe wandipenyetsa. Timadziwa kuti Mulungu samvera anthu ochimwa. Koma munthu akasamala za Mulungu, nachita zimene Mulungu akufuna, Mulungu amamumvera. Nkale lomwe sikudamveke konse kuti wina adapenyetsa munthu wakhungu. Munthu ameneyu akadapanda kuchokera kwa Mulungu, sakadatha konse kuchita kanthu.” Iwo adati, “iwe udabadwa m’machimo okhaokha. Ndiye iweyo nkutiphunzitsa ife?” Atatero adamtulutsa nkumudula mu mpingo.

 

Yesu adamva kuti Ayuda amtulutsa ndi kumdula ku mpingo munthu uja. Tsono pamene adampeza, adamfunsa kuti, “kodi ukukhulupirira mwana wa munthu?” Iye adati, “Ambuye, mundiwuzetu ndani iyeyo, kuti ndimkhulupirire.” Yesu adamuuza kuti, “wamuona kale, ndiyemwe akulankhula nawe.” Iye adati, “Ambuye, ndikukhulupirira.” Atatero adamgwadira. Tsono Yesu adati, “ndidabwera pansi pano kudzaweruza, kuti osapenya apenye, ndipo openya achite Khungu.” Afarisi ena amene anali pafupi naye, atamva zimenezi adamufunsa kuti, “kodi monga ifenso ndife akhungu?” Yesu adati, “mukadakhala akhungu, bwezi mulibe mlandu. Koma chifukwa mukuti, ‘tikupenya,’ ndiye kuti mlandu wanu ulipobe.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, lero popempherera anthu onse, tiyeni tipemphe Atate a Kumwamba kuti kuwala kwa Yesu Khristu kuunike m’mitima yathu ndi ya anthu ena:

 

1.     Eklezia wa Mulungu aonetse anthu amafuko onse kuwala kwa Yesu Khristu, pakuwalalikira Mthenga Wabwino, ndi pakuwatumikira modzichepetsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akhristu onse aunikire anzawo pakuyenda molimbika m’njira yaungwiro, ndipo pakuwonetsana mtima waubale pa moyo wao wa tsiku ndi tsiku.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu akhungu, agonthi, odwala, ndi ena onse amene ali m’mavuto, azindikire chifundo cha Mulungu polandira chithandizo chochokera kwa anzao.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tomwe tili muno, Mulungu atiwonjezere chikhulupiriro, tizipenya zinthu ndi maso a mu mtima ndi kufunafuna zimene zingakondweretse Iyeyo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, Inu mumayan’gana mitima ya anthu, osati maonekedwe ao. Tikutula m’manja mwanu mapemphero athuwa potamanda Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, March 11, 2023

LAMULUNGU LA 03 MU NYENGO YA LENTI – CHAKA A

“Ambuye, tipatseni madzi a moyo wosatha.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA EKISODO; EKISODO 17: 03 – 07 (Tipatseni madzi timwe…).

 

Aisraele pa ulendo wao m’chipululu anali ndi ludzu loopsa, ndipo ankangowiringulira Mose, kuti, “chifukwa chiyani mudatitulutsa ku Ejipito kuti mutiphe ndi ludzu, ife pamodzi ndi anthu ndi zoweta zathu?” Apo Mose adapemphera mokweza mau kwa Chauta, adati, “kodi anthu amenewa ndichite nawo chiyani? Iwowo ngokonzeka kundiponya miyala.” Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “tengako atsogoleri ena a Israele, mukakhale patsogolo pa anthuwo. Tsono utenge ndodo udamenya nayo madzi a mutsinje wa Nailo ija, ndipo upite. Ine ndidzakhala patsogolo pako kumeneko pafupi ndi thanthwelo, pa phiri la Horebu. Ukamenye thanthwe, tsono mudzatuluka madzi m’thanthwemo, kuti anthuwo amwe.” Mose adachitadi zimenezo pamaso pa atsogoleri a Aisraele aja. Malowo adawatcha mayeso ndiponso makangano, chifukwa Aisraele adakangana ndi Mose, ndipo adayesa Chauta pofunsa kuti, “kodi Chauta ali nafe, kapena ai?”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 95: 01 – 02, 06 – 09.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja.

                                                                                                                                                           

Bwerani, timuimbire Chauta,

Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa lye, thanthwe lotipulumutsa,

Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze,

Tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja.

 

Bwerani, timpembedze ndi kumlambira.,

Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu,

Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake,

Ndife nkhosa zodyera m’manja mwake.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja.

 

Lero mukadamverako mau ake!

Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja,

Monganso tsiku lija ku Masa m’chipululu muja,

Pamene makolo anu adandiputa mondiyesa ngakhale anali ataona ntchito zanga.

 

Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja.

--------------------------------------

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 05: 01 – 02, 05 – 08 (Mulungu mwa Mzimu Woyera, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake).

 

Abale, popeza kuti pakukhulupirira tapeza kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motere timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake. Pa nthawi imene Mulungu adaikonzeratu, pamene ife tikusowabe pogwira, Khristu adatifera anthu ochimwafe. Nchapatali kuti munthu afere munthu wina, ngakhale winayo akhale wolungama. Kaya kapena mwina munthu nkulimba mtima mpaka kufera munthu wabwino. Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tili ochimwabe, Khristu adatifera.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 04: 42, 15.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Tadziwa kuti ameneyu ndi Mpulumutsidi wa anthu a pa dziko lapansi! Tipatseni madzi amoyo, kuti tisakhalenso ndi njala. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 04: 05 – 42 (Madzi amene ndidzampatsewo azidzatumphukira mwa iye ngati kasupe wa madzi opatsa moyo).

 

Tsiku lina, Yesu adafika ku mudzi wina wa ku Samariya, dzina lake Sikari, pafupi ndi kadziko kamene Yakobe adapatsa Yosefe, mwana wake. Kumeneko kunali chitsime cha Yakobe. Yesu adakhala pansi pambali pa chitsimecho, chifukwa anali atatopa ndi ulendo. Nthawi inali ngati 12 koloko masana. Tsono padafika mai wina wachisamariya kudzatunga madzi. Yesu nkunena mopempha kuti, “zikomo mundipatseko madzi akumwa.” Nthawiyo nkuti ophunzira ake aja atakagula chakudya mu mzinda. Mai wachisamariya uja adayankha nati, “inu amene muli Myuda, bwanji mukupempha madzi kwa ine, mai wachisamariya?” (Pakuti Ayuda sayenderana ndi Asamariya). Yesu adati, “mukadadziwa mphatso ya Mulungu, mukadadziwanso amene akupempha madzi akumwayu, bwezi mutapempha ndi inuyo mai, Iye nakupatsani madzi opatsa moyo.” Maiyo adati, “bambo, mulibe nchotungira chomwe, ndipo chitsimechi nchozama. Nanga madzi opatsa moyowo muwatenga kuti? Yakobe, kholo lathu ndiye adatipatsa chitsimechi, chimene mwiniwakeyo ankamwapo pamodzi ndi ana ake, ndiponso zoweta zake. Kodi inu mungapambane iyeyo?” Yesu adati, “munthu aliyense womwako madzi awa, adzamvanso ludzu. Koma aliyense wodzamwa madzi amene Ine ndidzampatse, sadzamvanso ludzu konse mpaka muyaya. Madzi amene ndidzampatsewo azidzatumphukira mwa iye ngati kasupe wa madzi opatsa moyo, nkumupatsa moyo wosatha.” Maiyo adati, “bambo, patseniko ineyo madzi amenewo kuti ndisamamvenso ludzu kapena kumadzatunganso madzi kuno.” Yesu adati, “pitani mukaitane amuna anu, nkukabweranso kuno.” Maiyo adati, “ndilibe mwamuna.” Yesu adati, “mwanenetsa kuti mulibe mwamuna. Paja mwakwatiwapo kale ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye tsopano si wanunso. Mwanenazi nzoona.” Maiyo adatinso, “bambo, ndadziwa tsopano kuti ndinu mneneri. Makolo athu ankapembedza Mulungu pa phiri ili, koma inu Ayuda mumati ndi ku Yerusalemu kumene anthu ayenera kumakapembedzerako.” Yesu adamuuza kuti, “mai, ndithu ikudza nthawi pamene mudzapembedza Atate, osati pa phiri ili kapenanso ku Yerusalemu ai. Asamariyanu mumapembedza chimene simuchidziwa. Ayudafe timapembedza chimene timachidziwa, pakuti chipulumutso nchochokera mwa Ayuda. Koma ikudza nthawi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza. Mulungu ndi Mzimu, ndipo ompembedza iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.” Maiyo adati, “ndikudziwa kuti akudza mpulumutsi wolonjezedwa uja. Iyeyo akadzafika, adzatifotokozera zonse.” Yesu adamuuza kuti, “Ndine amene, Ineyo amene ndikulankhula nanu, mai.” Nthawi yomweyo ophunzira ake a Yesu adafika, ndipo ankadabwa kuti Iye akucheza ndi mkazi. Komabe panalibe amene adamufunsa kuti, “zakhala bwanji?” kapena kuti, “bwanji mukulankhula naye?” Maiyo adasiya mtsuko wake napita ku mudzi nkukauza anthu kuti, “tiyeni, mukaone munthu amene wandiwuza zonse zimene ine ndidachita. Kodi ameneyu sangakhale mpulumutsi wolonjezedwa uja kapena?” Apo anthuwo adatuluka m’mudzimo kubwera kwa Yesu. Nthawi imeneyo ophunzira ake a Yesu ankamupempha kuti, “Aphunzitsi, idyani.” Koma iye adati, “ine ndili nacho chakudya chimene inu simukuchidziwa.” Pamenepo ophunzirawo adayamba kufunsana kuti, “kodi kapena wina wadzawapatsa kale chakudya?” Koma Yesu adati, “chakudya changa nkuchita zimene afuna Atate amene adandituma, kuti nditsirize ntchito imene iwo adandituma. Paja anthu amati, ‘ikapita miyezi inai, ndiye kuti yafika nyengo yokolola’. Koma ndithu, taonani m’mindamu, kodi simukuona kuti mbeu zacha kale kudikira kholola? Okolola ayamba kale kulandira malipiro, ndipo akututira mbeu ku moyo wosatha, kuti obzala ndiokolola akondwere pamodzi. Paja amanenadi zoona aja amati, ‘wobzala ndi wina, wokolola ndi winanso.’ Ine ndidakutumani kukakolola mbeu zimene simudagwirirepo ntchito. Anthu ena ndiwo adagwira ntchito, inu mwangolandirapo phindu la ntchito yaoyo.” Asamariya ambiri a m’mudzi muja adakhulupilira Yesu chifukwa cha umboni wa mai uja, wakuti, “iye wandiwuza zonse zimene ndidachita.” Tsono pamene Asamariyawo adafika kwa Yesu, adampempha kuti akhale nao kwaoko. Ndipo adakhaladi komweko masiku awiri. Pamenepo anthu enanso ambiri adakhulupirira chifukwa cha mau a Yesu. Mwakuti adauza mai uja kuti, “takhulupirira tsopano, osati chifukwa cha mau ako, koma chifukwa tazimvera tokha. Tadziwa kuti ameneyu ndi mpulumutsidi wa anthu a pa dziko lonse lapansi.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba, kuti adzaze mitima yathu ndi ya anthu onse ndi Mzimu Woyera pa nthawi ino ya Lenti:

 

1.     Ansembe ndi akulu a Mpingo ayesetse kuutsa chikhulupiriro m’mitima ya anthu ao, pakuwalalikira Mthenga Wabwino ndi pakuwapempherera.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Akatekumeni ndi onse amene adayamba kumva za Yesu Khristu aonetse mtima wachidwi pa maphunziro ao, polakalaka zokoma za chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Anthu otsata zipembedzo zosiyanasiyana ndi ena onse amene adakali padera, Mzimu Woyera awaunikire ndi kuwatsogolera m’njira yachilungamo.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tili muno, misonkhano ya nthawi ino ya Lenti itithandize kupembedza Mulungu moonadi, potsata nzeru zija za kulapa.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate achifundo, mverani madandaulo athu, poti mitima yathu ikumva ludzu lokhumba Inu amene muli gwero la zabwino zonse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Saturday, March 4, 2023

LAMULUNGU LA 02 MU NYENGO YA LENTI – CHAKA A

“Ambuye, tiwonetseni kuwala kwa nkhope yanu.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 12: 01 – 04a (Kuyitanidwa kwa Abrahamu, Tate wa anthu a Mulungu).

 

Tsiku lina Chauta adauza Abramu kuti, “choka kudziko kwako kuno. Usiye abale ako ndi banja la bambo wako, ndipo upite ku dziko limene nditi ndikusonyeze. Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena. Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndizatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.” Abramu anali ndi zaka 75 pamene ankachoka ku Harani monga Chauta adaamlamulira, ndipo Loti adapita naye limodzi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 33: 04 – 05, 18 – 22.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Mau a Chauta ndi olungama,

Zochita zake zonse amazichita mokhulupirika,

Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera,

Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Chauta amayang’ana anthu omumvera,

Ndi odalira chikondi chake chosasinthika,

Iye amachita izi kuti awapulumutse ku imfa,

Ndi kuwasungira moyo anthuwo pa nthawi ya njala.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Mitima yathu ikuyembekeza Chauta,

Chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu,

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika,

Chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

 

Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

--------------------------------------

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEYO:  02 TIMOTEYO 01: 08b – 10 (Mulungu anatiitana ndipo amatitsogolera).

 

Wokondeka, usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m’ndende chifukwa cha iye, koma umve nawo zowawa chifukwa cha uthenga wabwino, ndichithandizo cha mphamvu za Mulungu. Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthawi isanayambe. Koma tsopano Mulungu watiwululira zimenezi kudzera m’kuwoneka kwa mpulumutsi wathu, Yesu Khristu. Khristuyo adzathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa uthenga wabwino adaonetsera poyera moyo umene sungafe konse.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 17: 05.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.” – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 17: 01 – 09 (Nkhope yake idawala ngati dzuwa).

 

Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, Yakobe ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuona. Nkhope yake idawala ngati dzuwa, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. Nthawi yomweyo ophunzira aja adaona Mose ndi Eliya akulankhula naye. Petro adauza Yesu kuti, “Ambuye, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Ngati mukufuna, ndimanga misasa itatu pano, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” Akulankhula choncho, kudadza mtambo wowala nuwaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “uyu ndiye mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.” Ophunzira aja atamva zimenezi, adachita mantha kwambiri nadzigwetsa chafufumimba. Koma Yesu adabwera, nawakhudza nkunena kuti, “dzukani, musachite mantha.” Iwo aja poweramuka, adangoona kuti palibe munthu winanso, koma Yesu yekha. Pamene ankatsika phiri lija, Yesu adaawalamula kuti, “zimene mwaona m’masomphenyazi musakauze wina aliyense mpaka mwana wa munthu atauka kwa akufa.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, lero popempherera anthu onse, tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti awaonetseko kuwala kwa nkhope yao, pakuwaninkha zabwino zomwe iwo akuziwona.

 

1.     Eklezia Woyera wa Mulungu akhale chizindikiro chosonyeza kuwala kwa Yesu Khristu kwa anthu a mafuko onse.

Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Anyamata ndi atsikana amene Mulungu awaitana ku ntchito yake, avomere kuitanidwa kwao ndipo alimbikire pa maphunziro ao.

Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Anthu odwala ndi onse amene akuvutika m’mitima mwao, asaleke kukhulupirira Mulungu pakati pa mavuto ao.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Akhristu anzathu amene adaleka kupemphera, azindikire chifundo cha Mulungu chofuna kuwapulumutsa, poona ntchito zathu zowatumikira.

Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, mwa chifundo chanu mverani mapemphero athuwa, ndipo mulimbitse chikhulupiriro chathu, mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...