LAMULUNGU LA 03 MU NYENGO YA LENTI – CHAKA A
“Ambuye, tipatseni madzi a moyo wosatha.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA EKISODO; EKISODO 17: 03 – 07 (Tipatseni madzi timwe…).
Aisraele pa ulendo wao m’chipululu anali ndi ludzu loopsa, ndipo ankangowiringulira Mose, kuti, “chifukwa chiyani mudatitulutsa ku Ejipito kuti mutiphe ndi ludzu, ife pamodzi ndi anthu ndi zoweta zathu?” Apo Mose adapemphera mokweza mau kwa Chauta, adati, “kodi anthu amenewa ndichite nawo chiyani? Iwowo ngokonzeka kundiponya miyala.” Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “tengako atsogoleri ena a Israele, mukakhale patsogolo pa anthuwo. Tsono utenge ndodo udamenya nayo madzi a mutsinje wa Nailo ija, ndipo upite. Ine ndidzakhala patsogolo pako kumeneko pafupi ndi thanthwelo, pa phiri la Horebu. Ukamenye thanthwe, tsono mudzatuluka madzi m’thanthwemo, kuti anthuwo amwe.” Mose adachitadi zimenezo pamaso pa atsogoleri a Aisraele aja. Malowo adawatcha mayeso ndiponso makangano, chifukwa Aisraele adakangana ndi Mose, ndipo adayesa Chauta pofunsa kuti, “kodi Chauta ali nafe, kapena ai?”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 95: 01 – 02, 06 – 09.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja.
Bwerani, timuimbire Chauta,
Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa lye, thanthwe lotipulumutsa,
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze,
Tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja.
Bwerani, timpembedze ndi kumlambira.,
Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu,
Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake,
Ndife nkhosa zodyera m’manja mwake.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja.
Lero mukadamverako mau ake!
Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja,
Monganso tsiku lija ku Masa m’chipululu muja,
Pamene makolo anu adandiputa mondiyesa ngakhale anali ataona ntchito zanga.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 05: 01 – 02, 05 – 08 (Mulungu mwa Mzimu Woyera, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake).
Abale, popeza kuti pakukhulupirira tapeza kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motere timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake. Pa nthawi imene Mulungu adaikonzeratu, pamene ife tikusowabe pogwira, Khristu adatifera anthu ochimwafe. Nchapatali kuti munthu afere munthu wina, ngakhale winayo akhale wolungama. Kaya kapena mwina munthu nkulimba mtima mpaka kufera munthu wabwino. Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tili ochimwabe, Khristu adatifera.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 04: 42, 15.
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Tadziwa kuti ameneyu ndi Mpulumutsidi wa anthu a pa dziko lapansi! Tipatseni madzi amoyo, kuti tisakhalenso ndi njala. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 04: 05 – 42 (Madzi amene ndidzampatsewo azidzatumphukira mwa iye ngati kasupe wa madzi opatsa moyo).
Tsiku lina, Yesu adafika ku mudzi wina wa ku Samariya, dzina lake Sikari, pafupi ndi kadziko kamene Yakobe adapatsa Yosefe, mwana wake. Kumeneko kunali chitsime cha Yakobe. Yesu adakhala pansi pambali pa chitsimecho, chifukwa anali atatopa ndi ulendo. Nthawi inali ngati 12 koloko masana. Tsono padafika mai wina wachisamariya kudzatunga madzi. Yesu nkunena mopempha kuti, “zikomo mundipatseko madzi akumwa.” Nthawiyo nkuti ophunzira ake aja atakagula chakudya mu mzinda. Mai wachisamariya uja adayankha nati, “inu amene muli Myuda, bwanji mukupempha madzi kwa ine, mai wachisamariya?” (Pakuti Ayuda sayenderana ndi Asamariya). Yesu adati, “mukadadziwa mphatso ya Mulungu, mukadadziwanso amene akupempha madzi akumwayu, bwezi mutapempha ndi inuyo mai, Iye nakupatsani madzi opatsa moyo.” Maiyo adati, “bambo, mulibe nchotungira chomwe, ndipo chitsimechi nchozama. Nanga madzi opatsa moyowo muwatenga kuti? Yakobe, kholo lathu ndiye adatipatsa chitsimechi, chimene mwiniwakeyo ankamwapo pamodzi ndi ana ake, ndiponso zoweta zake. Kodi inu mungapambane iyeyo?” Yesu adati, “munthu aliyense womwako madzi awa, adzamvanso ludzu. Koma aliyense wodzamwa madzi amene Ine ndidzampatse, sadzamvanso ludzu konse mpaka muyaya. Madzi amene ndidzampatsewo azidzatumphukira mwa iye ngati kasupe wa madzi opatsa moyo, nkumupatsa moyo wosatha.” Maiyo adati, “bambo, patseniko ineyo madzi amenewo kuti ndisamamvenso ludzu kapena kumadzatunganso madzi kuno.” Yesu adati, “pitani mukaitane amuna anu, nkukabweranso kuno.” Maiyo adati, “ndilibe mwamuna.” Yesu adati, “mwanenetsa kuti mulibe mwamuna. Paja mwakwatiwapo kale ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye tsopano si wanunso. Mwanenazi nzoona.” Maiyo adatinso, “bambo, ndadziwa tsopano kuti ndinu mneneri. Makolo athu ankapembedza Mulungu pa phiri ili, koma inu Ayuda mumati ndi ku Yerusalemu kumene anthu ayenera kumakapembedzerako.” Yesu adamuuza kuti, “mai, ndithu ikudza nthawi pamene mudzapembedza Atate, osati pa phiri ili kapenanso ku Yerusalemu ai. Asamariyanu mumapembedza chimene simuchidziwa. Ayudafe timapembedza chimene timachidziwa, pakuti chipulumutso nchochokera mwa Ayuda. Koma ikudza nthawi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza. Mulungu ndi Mzimu, ndipo ompembedza iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.” Maiyo adati, “ndikudziwa kuti akudza mpulumutsi wolonjezedwa uja. Iyeyo akadzafika, adzatifotokozera zonse.” Yesu adamuuza kuti, “Ndine amene, Ineyo amene ndikulankhula nanu, mai.” Nthawi yomweyo ophunzira ake a Yesu adafika, ndipo ankadabwa kuti Iye akucheza ndi mkazi. Komabe panalibe amene adamufunsa kuti, “zakhala bwanji?” kapena kuti, “bwanji mukulankhula naye?” Maiyo adasiya mtsuko wake napita ku mudzi nkukauza anthu kuti, “tiyeni, mukaone munthu amene wandiwuza zonse zimene ine ndidachita. Kodi ameneyu sangakhale mpulumutsi wolonjezedwa uja kapena?” Apo anthuwo adatuluka m’mudzimo kubwera kwa Yesu. Nthawi imeneyo ophunzira ake a Yesu ankamupempha kuti, “Aphunzitsi, idyani.” Koma iye adati, “ine ndili nacho chakudya chimene inu simukuchidziwa.” Pamenepo ophunzirawo adayamba kufunsana kuti, “kodi kapena wina wadzawapatsa kale chakudya?” Koma Yesu adati, “chakudya changa nkuchita zimene afuna Atate amene adandituma, kuti nditsirize ntchito imene iwo adandituma. Paja anthu amati, ‘ikapita miyezi inai, ndiye kuti yafika nyengo yokolola’. Koma ndithu, taonani m’mindamu, kodi simukuona kuti mbeu zacha kale kudikira kholola? Okolola ayamba kale kulandira malipiro, ndipo akututira mbeu ku moyo wosatha, kuti obzala ndiokolola akondwere pamodzi. Paja amanenadi zoona aja amati, ‘wobzala ndi wina, wokolola ndi winanso.’ Ine ndidakutumani kukakolola mbeu zimene simudagwirirepo ntchito. Anthu ena ndiwo adagwira ntchito, inu mwangolandirapo phindu la ntchito yaoyo.” Asamariya ambiri a m’mudzi muja adakhulupilira Yesu chifukwa cha umboni wa mai uja, wakuti, “iye wandiwuza zonse zimene ndidachita.” Tsono pamene Asamariyawo adafika kwa Yesu, adampempha kuti akhale nao kwaoko. Ndipo adakhaladi komweko masiku awiri. Pamenepo anthu enanso ambiri adakhulupirira chifukwa cha mau a Yesu. Mwakuti adauza mai uja kuti, “takhulupirira tsopano, osati chifukwa cha mau ako, koma chifukwa tazimvera tokha. Tadziwa kuti ameneyu ndi mpulumutsidi wa anthu a pa dziko lonse lapansi.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba, kuti adzaze mitima yathu ndi ya anthu onse ndi Mzimu Woyera pa nthawi ino ya Lenti:
1. Ansembe ndi akulu a Mpingo ayesetse kuutsa chikhulupiriro m’mitima ya anthu ao, pakuwalalikira Mthenga Wabwino ndi pakuwapempherera.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akatekumeni ndi onse amene adayamba kumva za Yesu Khristu aonetse mtima wachidwi pa maphunziro ao, polakalaka zokoma za chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu otsata zipembedzo zosiyanasiyana ndi ena onse amene adakali padera, Mzimu Woyera awaunikire ndi kuwatsogolera m’njira yachilungamo.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tomwe tili muno, misonkhano ya nthawi ino ya Lenti itithandize kupembedza Mulungu moonadi, potsata nzeru zija za kulapa.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate achifundo, mverani madandaulo athu, poti mitima yathu ikumva ludzu lokhumba Inu amene muli gwero la zabwino zonse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment