LAMULUNGU LA 02 MU NYENGO YA LENTI – CHAKA A
“Ambuye, tiwonetseni kuwala kwa nkhope yanu.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 12: 01 – 04a (Kuyitanidwa kwa Abrahamu, Tate wa anthu a Mulungu).
Tsiku lina Chauta adauza Abramu kuti, “choka kudziko kwako kuno. Usiye abale ako ndi banja la bambo wako, ndipo upite ku dziko limene nditi ndikusonyeze. Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena. Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndizatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.” Abramu anali ndi zaka 75 pamene ankachoka ku Harani monga Chauta adaamlamulira, ndipo Loti adapita naye limodzi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 33: 04 – 05, 18 – 22.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Mau a Chauta ndi olungama,
Zochita zake zonse amazichita mokhulupirika,
Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera,
Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Chauta amayang’ana anthu omumvera,
Ndi odalira chikondi chake chosasinthika,
Iye amachita izi kuti awapulumutse ku imfa,
Ndi kuwasungira moyo anthuwo pa nthawi ya njala.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta,
Chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu,
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika,
Chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA TIMOTEYO: 02 TIMOTEYO 01: 08b – 10 (Mulungu anatiitana ndipo amatitsogolera).
Wokondeka, usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m’ndende chifukwa cha iye, koma umve nawo zowawa chifukwa cha uthenga wabwino, ndichithandizo cha mphamvu za Mulungu. Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthawi isanayambe. Koma tsopano Mulungu watiwululira zimenezi kudzera m’kuwoneka kwa mpulumutsi wathu, Yesu Khristu. Khristuyo adzathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa uthenga wabwino adaonetsera poyera moyo umene sungafe konse.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 17: 05.
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.” – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 17: 01 – 09 (Nkhope yake idawala ngati dzuwa).
Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, Yakobe ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuona. Nkhope yake idawala ngati dzuwa, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. Nthawi yomweyo ophunzira aja adaona Mose ndi Eliya akulankhula naye. Petro adauza Yesu kuti, “Ambuye, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Ngati mukufuna, ndimanga misasa itatu pano, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” Akulankhula choncho, kudadza mtambo wowala nuwaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “uyu ndiye mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.” Ophunzira aja atamva zimenezi, adachita mantha kwambiri nadzigwetsa chafufumimba. Koma Yesu adabwera, nawakhudza nkunena kuti, “dzukani, musachite mantha.” Iwo aja poweramuka, adangoona kuti palibe munthu winanso, koma Yesu yekha. Pamene ankatsika phiri lija, Yesu adaawalamula kuti, “zimene mwaona m’masomphenyazi musakauze wina aliyense mpaka mwana wa munthu atauka kwa akufa.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, lero popempherera anthu onse, tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti awaonetseko kuwala kwa nkhope yao, pakuwaninkha zabwino zomwe iwo akuziwona.
1. Eklezia Woyera wa Mulungu akhale chizindikiro chosonyeza kuwala kwa Yesu Khristu kwa anthu a mafuko onse.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anyamata ndi atsikana amene Mulungu awaitana ku ntchito yake, avomere kuitanidwa kwao ndipo alimbikire pa maphunziro ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu odwala ndi onse amene akuvutika m’mitima mwao, asaleke kukhulupirira Mulungu pakati pa mavuto ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Akhristu anzathu amene adaleka kupemphera, azindikire chifundo cha Mulungu chofuna kuwapulumutsa, poona ntchito zathu zowatumikira.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mwa chifundo chanu mverani mapemphero athuwa, ndipo mulimbitse chikhulupiriro chathu, mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment