LAMULUNGU LA 01 MU NYENGO YA LENTI – CHAKA A
“Tipeza mwa Yesu Khristu mphamvu zokonjetsera zoipa.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA GENESIS; GENESIS 02: 07 – 09; 03: 01 – 07 (Kuchimwa kwa makolo athu oyamba).
Chauta adatenga dothi pa nthaka, ndipo adaumba munthu ndi dothilo. Adamuuzira mpweya wopatsa moyo m’mphuno zake, ndipo munthuyo adakhala wamoyo. Kenaka Chauta adatsekula munda wa Edeni chakuvuma, ndipo munthu adamuumbayo adamkhazika m’menemo. Chauta adameretsamo mitengo yokongola ya zipatso zokoma. Pakati pa mundawo panali mtengo wopatsa moyo, ndiponso mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa. Njoka inali yochenjera kupambana zamoyo zonse zimene Chauta adazilenga. Njokayo idafunsa mkazi uja kuti, “kodi nzoona kuti Mulungu adakuletsani kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse m’munda muno?” Mkazi uja adayankha kuti, “tingathe kudya zipatso za mtengo uliwonse m’munda muno, kupatula wokhawo umene uli pakati pake. Mulungu adanena kuti tisadye zipatso za mtengo umenewo, ngakhale kuzikhudza, chifukwa choti tikadzangotero, tidzafa.” Koma Njokayo idayankha mkaziyo kuti, “iyayi, kufa simudzafa konse. Mulungu amadziwa kuti inu mukadzadya zipatso zimenezi, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala monga momwe aliri Mulunguyo. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.” Tsono mkaziyo adaona kuti mtengewo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya. Atangodya choncho, adazindikira kuti ali maliseche. Choncho adasoka masamba a mkuyu navala.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 51: 03 – 06, 12 – 13, 17.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika,
Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu,
Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga,
Mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
Zolakwa zanga ndikuzidziwa,
Kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthawi zonse,
Ndachimwira Inu, Inu nokha,
Ndachita choipa pamaso panu.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu,
Muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika,
Musandipirikitse pamaso panu,
Musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu,
Mulimbitse mwa ine mtima womvera,
Ambuye, tsekulani milomo yanga,
Ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA
KWA AROMA; AROMA 05: 12 – 19 (Monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, momwemonso amapezeka olungama).
Abale, uchimo udalowa m’dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke malamulo. Koma pamene palibe malamulo, machimo a munthu sawerengedwa ai. Komabe kuyambira nthawi ya Adamu kufikira nthawi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira iye uja amene Mulungu adati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye munthu mmodzi uja, Yesu Khristu. Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo. Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuwapatsa moyo. Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, Momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa munthu winanso mmodzi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Mateyo 04: 04b
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 04: 01 – 11 (Yesu adasala zakudya kwa masiku makumi anai, ndipo Satana anali kumuyesa).
Pa nthawi yomweyo, Mzimu Woyera adatsogolera Yesu kupita ku Chipululu kuti Satana akamuyese. Pa masiku makumi anai Yesu adasala zakudya usana ndi usiku, ndipo pambuyo pake adamva njala. Tsono woyesa uja adadza namuuza kuti, “ngati ndinu mwana wa Mulungu, Lamulani miyala ili apayi kuti isanduke chakudya.” Koma Yesu adati, “malembo akuti, ‘munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’” Pambuyo pake Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, mzinda wopatulika, nakamuimika pamwamba penipeni pa nyumba ya Mulungu. Adamuuza kuti, “ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja malembo akuti, ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni, iwo adzakunyamulani ndi m’manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’” Koma Yesu adati, “malembo akutinso, ‘usawayese Ambuye, Mulungu wako.’” Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye pa phiri lalitali kwambiri, ndipo adamuwonetsa maufumu onse a pansi pano ndi ulemerero wake. Tsono adamuuza kuti, “zonsezi ndidzakupatsani mukagwada pansi ndi kundipembedza.” Apo Yesu adati, “choka, Satana! Paja malembo akuti, ‘uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziwatumikira Iwo wokha.’” Pamenepo Satana adamsiya, angelo nkubwera kumadzamutumikira Yesuyo.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pozindikira umphawi wathu ndi kufooka kwathu, tiyeni tikweze mitima yathu kumwamba pamodzi ndi mapemphero athu:
1. Apapa ndi Aepiskopi ndi ansembe onse atsogolere akhristu ao m’njira ya ungwiro, powazindikiritsa nzeru zolapira machimo.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu ofooka ndi onse amene adalowerera, adzidzimuke mumtima mwao, pokumbukira chifundo chozama cha Yesu Khristu Mpulumutsi wao.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anthu onse amene sadamvebe Mthenga Wabwino, Mulungu awaunikire ndi Mzimu Woyera ndi kuwalondoloza m’njira ya chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse tili muno, ntchito zathu za nthawi ino ya Lenti zisonyeze kulapa kwenikweni ndi kuthandiza anzathu kupulumuka.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mwa kukoma mtima kwanu mutibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, ndipo tidzayamika ulemerero wanu mpaka muyaya. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment