TSIKU LA PHULUSA – CHAKA A (TSIKU LOYAMBA LA LENTI)
“Ino ndi nthawi yoti tiyanjanenso ndi Mulungu.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI YOWELE; YOWELE 02: 12 – 18 (Ng’ambani mitima yanu osati zovala zanu chabe).
Chauta akunena kuti, “ngakhale tsopano bwererani kwa ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni. Ng’ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthawi zonse ndi wokonzeka kukhululuka. Mwina mwake adzasintha mtima ndi kuleka, ndipo adzatisiyira madalitso. Madalitsowo adzakhala a chopereka cha chakudya ndi chakumwa zopereka kwa Chauta, Mulungu wanu. Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitanitse msonkhano waukulu. Sonkhanitsani anthu pamodzi, muwauze kuti adziyeretse. Sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Lamulani kuti nawonso akwati achoke m’chipinda mwao, abwere. Ansembe, amene ali atumiki a Chauta, azilira pakati pa guwa la ansembe ndi khonde. Azinena kuti, “Inu Chauta, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti ena awanyoze anthu anu osankhidwa. Anthu achikunja asawaseke pomafunsana kuti, ‘Ha, ali kuti Mulungu waoyo?’” Apo chikondi cha Chauta chidayaka ngati moto chifukwa cha dziko lake, ndipo adawachitira chifundo anthu ake.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 51: 03 – 06ab, 12 – 14, 17.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika,
Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu,
Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga,
Mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
Zolakwa zanga ndikuzidziwa,
Kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthawi zonse,
Ndachimwira Inu, Inu nokha,
Ndachita choipa pamaso panu.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu,
Muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika,
Musandipirikitse pamaso panu,
Musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu,
Mulimbitse mwa ine mtima womvera,
Ambuye, tsekulani milomo yanga,
Ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu.
Mutichitire chifundo, Inu Mulungu, chifukwa tinachimwa.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKORITO; 02 AKORITO 05: 20 – 06: 02 (Muvomere kuyanjananso ndi Mulungu... Pa nthawi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima.).
Abale, ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m’dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu. Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu. Tsono popeza kuti ndife ogwirizana ndi Mulungu pa ntchito yake, takupembani musawasandutse achabe madalitso amene Mulungu adzakupatsani. Paja Mulungu adati, “Pa nthawi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima, ndidakumvera, pa nyengo ya kupulumutsa anthu, ndidakuthandiza.” Mvetsani, ndi inotu nthawi yabwinoyo, imene Mulungu akukomera anthu mtima. Ndi lerotu tsiku la chipulumutsolo.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO –
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Mundilengere mtima woyera, In Mulungu, ndipo mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 06: 01 – 06, 16 – 18 (Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho).
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuwoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali kumwamba. Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m’nyumba zamapemphero ndiponso m’misewu yam’mzinda. Iwowa amachita zimenezi kuti anthu awatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe zimene dzanja lako lamanja likuchita. Ukatero, zachifundo zakozo zidzakhala zodziwa iwe wekha. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho. Pamene mukupemphera, musachite monga anthu achiphamaso ai. Iwowo amakonda kuimirira ndi kupemphera m’nyumba zamapemphero ndi pa mphambano za miseu yam’mzinda. Amachita zimenezi kuti anthu awaone. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphoto yao. Koma iwe, pamene ukuti upemphere, lowa m’chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho. Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphoto yao. Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m’maso nkudzola mafuta kumutu, kuti anthu asadziwe kuti ukusala zakudya. Koma Atate ako amene ali osaoneka ndiwo adziwe. Ndipo Atate akowo amene amaona zobisika, adzakupatsa mphotho.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, ino ndi nthawi yabwino imene Mulungu alikukomera anthu mtima. Tiyeni tidandaule kwa Atate athu a Kumwamba, pozindikira zosowa zathu ndi za anthu onse:
1. Ansembe akhale akazembe enieni a Yesu Khristu polalika Mthenga Wabwino ndi kutsogolera akhristu ao m’njira ya kulapa.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu amilandu ndi onse amene adaleka kupemphera, adzuke ndi kubwera kwa Mulungu Atate ao pa nthawi ino ya Lenti.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akatekumeni alimbike m’chikhulupiriro ndipo aonetse kulapa kwenikweni pakuwongola makhalidwe ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife amene talandira phulusa tsopano apa, tikhale nawo mtima watsopano, pogonjetsa zilakolako zoipa pochita ntchito zachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mutibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, ndipo pakamwa pathu padzayamika ulemu wanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment