LAMULUNGU LA 07 PA CHAKA – A
“Kondani adani anu omwe.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA LEVITIKO: LEVITIKO 19: 01 – 02, 17 – 18 (Mukonde mnzanu monga momwe mumadzikondera inu nomwe).
Chauta adauzanso Mose kuti, “uza mpingo wonse wa Aisraele kuti, ‘mukhale oyera pakuti Ine Chauta, Mulungu wanu, Ndine woyera. Musadane ndi mbale wanu mumtima mwanu, koma mumdzudzule mosabisa kuti mungavomerezane naye pa tchimo lake. Musabwezere choipa, ndipo musakwiyire anthu a mtundu wanu, koma mukonde mnzanu monga mumadzikondera inu nomwe. Ine ndine Chauta.’”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 103: 01 – 04, 08, 10, 12 – 13.
Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,
Moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera,
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,
Ndipo usaiwale zabwino zake zonse.
Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.
Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse,
Ndi kuchiritsa matenda ako onse,
Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda,
Amakuveka chikondi chake chosasinthika,
Ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu.
Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.
Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga,
Ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu,
Satilanga moyenerera machimo athu,
Satibwezera molingana ndi zolakwa zathu.
Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.
Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe,
Ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
Ndi momwenso Chauta amawachitira chifundo omulemekeza.
Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 03: 16 – 23 (Inu ndinu ake a Khristu, ndipo Khristu ndi wake wa Mulungu).
Abale, kodi inu simudziwa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene. Tsono musadzinyenge. Ngati wina mwa inu adziyesa wanzeru, kunena za nzeru za masiku ano, ameneyo ayambe wakhala ngati wopusa, kuti asanduke wanzeru. Zoonadi nzeru za anthu odalira zapansipano, nzopusa pamaso pa Mulungu. Pajatu Malembo akuti, “Mulungu amakola anthu anzeru m’kuchenjera kwao.” Penanso malembo akuti, “Ambuye amawadziwa maganizo a anthu anzeru kuti ndi achabe.” Nchifukwa chake pasakhale wina aliyense wonyadira anthu chabe. Zinthu zonse nzanu: Paulo, Apolo ndi Kefa, dziko lapansi, moyo ndi imfa, zimene zilipo ndi zimene zilikudza. Koma ngakhale zonsezi nzanu, inu ndinu ake a Khristu, ndipo Khristu ndi wake wa Mulungu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO –
Alleluia, Alleluia – Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 05: 38 – 48 (Muzikonda adani anu).
Yesu adawauza ophunzira ake kuti, “mudamva kuti anthu akale aja adaawalamula kuti, ‘diso kulipa diso, ndipo dzino kulipa dzino.’ Chabwino, koma ine ndikukuuzani kuti munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja, upereke linalonso. Munthu akakuzenga mlandu nafuna kukulanda mkanjo wako, umlole atengenso ndi mwinjiro wako womwe. Munthu akakukakamiza kuyenda naye mtunda umodzi, uyende naye mitundu iwiri. Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize. Mudamva kuti anthu akale aja adaawalamula kuti, ‘ukonde mnzako, ndikudana ndi mdani wako.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziwapempherera amene amakuzunzani. Mukatero mudzakhaladi ana a Atate anu amene ali kumwamba. Paja iwo amawalitsa dzuwa lao pa anthu abwino ndi pa anthu oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe. Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungalandire mphoto yanji? Kodi suja ngakhale okhometsa msonkho amachita chimodzimodzi? Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okha, mwachitapo chiyani pamenepo choposa ena? Kodi suja ngakhale akunja amachita chimodzimodzi? Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Mulungu amafuna kuti tikhale angwiro monga Iye ali wangwiro, tiyeni tipemphe Atate athu akumwamba kuti adzaze mitima yathu ndi ya anthu onse ndi Mzimu wao wachikondi:
1. Akhristu onse ayanjane, ndipo kukondana kwao kupite mtsogolo, adziwe kugonjetsa zoipa pakuchita zabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Anthu a mafuko onse alekeretu kukangana ndi kuukirana ndipo choncho mtendere ukhazikike pakati pa maiko ndinso pakati pa magulu a anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Mabanja onse, eniake akhale a mtima umodzi, adziwe kukhulukirana mwansanga, ndipo apereke chitsanzo chokoma kwa ana ao.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse tili muno, Mulungu alunzitse mitima yathu, chifundo chathu chokonda anthu onse chikhale maziko ake a moyo wathu tsiku ndi tsiku.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, Inu mumachitira zokoma anthu abwino ndi oipa omwe. Mutithandize kukhala nawo mtima womwewo, kuti tikhaledi ana anu enieni. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment