Saturday, February 11, 2023

 


LAMULUNGU LA 06 PA CHAKA – A

“Ngwodala iwo amene asunga malamulo.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPHUNZITSI; MPHUNZITSI 15: 15 – 20. (Chikhalire sadalamule munthu aliyense kuti akhale wosasamala za Mulungu).

 

Ngati ufuna, ungathe kutsata malamulo. Kukhala wokhulupirika kapena ai zili kwa iwe. Adakuikira moto ndi madzi pamaso pako, tambalitsa dzanja lako usankhepo chimene ufuna. Munthu amamuonetsa moyo ndi imfa, ndipo amalandira chimene wasankhapo. Nzeru za Ambuye nzambiri kwabasi, ali ndi mphamvu zonse, ndipo amaona zonse. Ambuye amayang’ana onse owaopa, ndipo zonse zimene anthu amachita iwo amazidziwa. Chikhalire sadalamule munthu aliyense kuti akhale wosasamala za Mulungu, kapena kumlola kuti azichimwa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 119: 01 – 05, 17 – 18, 33 – 34.

 

Ngodala amene amatsata malamulo a Mulungu.

 

Ngodala amene moyo wao ulibe chowadzudzulira,

Amene amayenda motsata malamulo a Chauta,

Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta,

Amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse.

 

Ngodala amene amatsata malamulo a Mulungu.

 

Inu Chauta, mwapereka malamulo anu,

Ndipo mwalamula kuti atsatidwe kwathunthu,

Ndikadakonda kuti njira zanga zikhale zokhulupirika,

Pakumvera malamulo anu.

 

Ngodala amene amatsata malamulo a Mulungu.

 

Komereni mtima ine mtumiki wanu,

Kuti ndikhale ndi moyo ndi kusunga mau anu,

Tsekulani maso anga,

Kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m’malamulo anu.

 

Ngodala amene amatsata malamulo a Mulungu.

 

Chauta, phunzitseni njira zosungira malamulo anu,

Ndipo ndidzazitsata mpaka kumathero,

Patseni nzeru kuti ndizisunga malamulo anu,

Ndiziwatsata ndi mtima wanga wonse.

Ngodala amene amatsata malamulo a Mulungu.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 02: 06 – 10. (Mulungu asanalenge dziko lapansi, adaakonzeratu kuti atipatse ulemerero.)

 

Pakati pa anthu okhwima m’chikhulupiliro, timalankhula zanzeru. Koma nzeruzo si za masiku anozi, kapena za akulu olamulira dziko lino lapansi, amene mphamvu zao nzodzatha. Nzeru zimene timalankhulana, ndi nzeru za Mulungu, zachinsinsi zobisika kwa anthu. Mulungu asanalenge dziko lapansi, adaakonzeratu zimenezi kuti atipatse ulemerero. Panalibiretu wolamulira wa masiku ano odziwa zimenezi. Akadazidziwa, sadakapachika Ambuye aulemelero pa mtanda. Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “maso a munthu sanaziwone, makutu amunthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adawakonzera amene amamkonda.” Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziwa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO –

 

Alleluia, Alleluia – Lankhulani, Inu Ambuye, poti mtumiki wanune ndilikumva. Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 05: 17 – 37. (Mudamva kuti anthu akale aja adaawalamula, koma Ine ndikukuuzani kuti...)

 

Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “Musamaganiza kuti ndidadzathetsa malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzawathetsa, koma kudzawafikitsa pachimake penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang’ono komwe kapena kankhodolera pa malamulowo, mpaka zonse zitachitika. Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo amenewa, ngakhale laling’ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng’ono ndithu mu ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amawatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba. Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti ngati kukhulupirika kwanu sikuposa kukhulupirika kwa Aphunzitsi a malamulo ndi kwa Afarisi, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. Mudamva kuti anthu akale aja adaawalamula kuti, “usaphe. Aliyense wopha mnzake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu.” Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, “wopandapake iwe,” adzayenera kuzengedwera ku bwalo lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, “chitsiru,” adzayenera kuzaponyedwa ku moto wa Gehena. Nchifukwa chake ngati wabwera ndi chopereka chako ku guwa, nthawi yomweyo nkukumbukira kuti mnzako wina ali nawe nkathu, siya chopereka chakocho kuguwa komweko, ndipo pita, kayambe wayanjana naye mnzakoyo. Pambuyo pake ndiye ubwere kudzapereka chopereka chako chija. Uziyanjana mnsanga ndi mnzako wamlandu, mukali pa njira yopita ku bwalo la milandu, kuwopa kuti angakakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m’ndende. Ndithu ndikunenetsa kuti sudzatulukamo mpaka utalipira zonse. Mudamva kuti anthu akale aja adaawalamula kuti, “Usachite chigolo.” Chabwino, koma ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang’ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake. Ngati diso lako la ku dzanja lamanja likuchimwitsa, likolowole nkulitaya. Ndi bwino koposa kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kusiyana nkuti thupi lako lonse aliponye ku Gehena. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena. Anthu akale aja adaawalamulanso kuti, “ngati munthu asudzula mkazi wake, ampatse mkaziyo kalata yachisudzulo.” Chabwino, koma ine ndikukuuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, akumuchititsa chigololo mkaziyo ngati akwatiwanso. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo. Mudamvanso kuti anthu akale aja adaawalamula kuti, “usalumbire monama, koma uchitedi zimene udawalonjeza Ambuye molumbira.” Chabwino, koma ine ndikukuuzani kuti muleke nkulumbira komwe. Usalumbire kuti, “kumwambadi!” Paja kumwamba kuli mpando waufumu wa Mulungu. Usalumbire kuti, “pali dziko lapansi!” Paja dziko lapansi ndi chopondapo mapazi ake. Usalumbire kuti, “pali Yerusalemu!” Paja Yerusalemu ndi mzinda wa mfumu yaikulu. Usalumbire ngakhale pa mutu wako, pakuti sungathe kusandulitsa ndi tsitsi limodzi lomwe kuti likhale loyera kapena lakuda. Muzingoti, “inde,” kapena “ai.” Zimene muwonjezerapo nzochokera kwa Satana, woipa uja.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu

 

Abale, podziwa kuti ndife ana a Mulungu, tileke mtima wamantha. Titembenukire kwa Iye mokhulupirira, ndipo timupemphe madalitso ake pa ife ndi pa anthu onse:

 

1.     Atsogoleri a Mpingo, alondoloze anthu ao m’njira ya ungwiro, potsata maphunzitso ndi zitsanzo zokoma zimene Yesu adatisiyira mu Mthenga Wabwino.

Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akulu olamulira maiko asenze udindo wao mokhulupirika ndi modzichepetsa, potsata ubwino wa anthu ao.

Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Aphunzitsi agwire ntchito yao modzipereka ndipo athandize ana awo kutenga makhalidwe abwino.

Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Makolo a ana alere bwino ana ao poongolera nzeru zao ndi mitima yao pachiyambi pomwe, ndipo awaphunzitse kupemphera ndi kukonda Mulungu.

Tikupemphani, mutivomereze.

5.     Ife amene tili muno, Mzimu Woyera atitsogolere m’zochita zathu zonse, tizitumikira Mulungu mwachikondi osati mwamantha.

Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, mukhazikitse mitima yathu ndi ya anthu onse m’chikondi chanu kuti tiyende molimbika ndi mosangalala m’njira ya malamulo anu. Mwa Yesu Khristu, Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...