LAMULUNGU LA 05 PA CHAKA – A
“Kuwala kwanu kuwoneke pamaso pa anthu.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI YESAYA; YESAYA 58: 07 – 10. (Mukatero, mudzawala ngati mbandakucha.)
Chauta akunena kuti: Anthu anjala muziwagawirako chakudya chanu, osowa pokhala muziwapatsako malo. Mukaona wausiwa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu. Mukatero, mudzawala ngati mbandakucha, ndipo mabala anu adzapola msanga. Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani, ndipo ulemelero wanga udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu. Mukamapemphera ndidzakumverani, ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani. Mukaleka kuzunza anzanu, mukasiya kulozana chala, mukaleka kunena zoipa za anzanu, mukamadyetsa anthu anjala, ndikuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuwala ngati kwa usana.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 112: 04 – 09.
Munthu wochita chilungamo ayenda m’kuwala.
Munthu wochita chilungamo ayenda m’kuwala,
Chifukwa ngwokoma mtima, wachifundo ndi woongoka.
Munthu amene amakongoza mosafuna phindu,
Amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.
Munthu wochita chilungamo ayenda m’kuwala.
Pakuti munthu wochita chilungamo sadzagwedezeka konse,
Sadzaiwalika mpaka muyaya.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika.
Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Munthu wochita chilungamo ayenda m’kuwala.
Ali wolimba mtima, sadzachita mantha.
Amapereka chithandizo mwaufulu.
Chilungamo chake chidzakhala chamuyaya,
Adzakhala wamphamvu ndipo anthu adzampatsa ulemu.
Munthu wochita chilungamo ayenda m’kuwala.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 02: 01 – 05. (Ndidaatsimikiza kuti pamene ndili pakati panu, ndiwale zina zonse, kupatula Yesu Khristu yekha, amene adapachikidwa pa mtanda.)
Abale, inetu pamene ndidafika kwanu kuti ndikulalikireni chinsinsi chimene Mulungu adatiwululira, sindidayese kulankhula mwaluso, ngati munthu wodziwa zapatali. Koma ndiidaatsimikiza kuti pamene ndili pakati panu, ndiiwale zonse, kupatula Yesu Khristu yekha, koma tsono amene adapachikidwa pa mtanda. Choncho pamene ndidafika kwanuko, ndinali wofooka, ndiponso ndinkanjenjemera kwambiri ndi mantha. Ndipo pamene ndinkalankhula kapena kulalika, sindinkalankhula moonetsa nzeru, kuyesa kukopa anthu, koma mau anga anali otsimikizika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiliro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Yohane 08:12.
Alleluia, Alleluia – Ine ndine kuwala kounikira anthu onse. Atero Ambuye. Munthu
wotsata Ine, adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 05: 13 – 16. (Inu ndinu kuwala kounikira anthu onse.)
Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “Inu ndinu Mchere wa dziko la pansi. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Ulibenso ntchito mpang’ono pomwe, koma kungoutaya kunja basi, anthu nkumauponda. Inu ndinu kuwala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m’nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu
Abale, titembenukire kwa Mulungu Atate athu achifundo, ndipo titule m’manja mwake zosowa zathu ndi za anthu onse:
1. Mpingo wa Mulungu upitirize kuunikira anthu onse ndi maphunzitso ake, makamaka poonetsa makhalidwe angwiro ndi achikondi.
Tikupemphani…, mutivomereze.
2. Akhristu a mipingo yosiyanasiyana agwirizane kwenikweni pa ntchito zosamalira matenda ndi zokometsera miyoyo ya anthu.
Tikupemphani…, mutivomereze.
3. Anyamata ndi atsikana avomere kuitana kwa Mulungu, akhale nyale zounikira anzawo ndi m’chere wokometsa dziko lonse lapansi.
Tikupemphani…, mutivomereze.
4. Ifenso tili muno, tilimbikire kuchita ntchito zachifundo: chikhulupiriro chathu chisati chikhale cha pakamwa pokha, koma chiwonekere poyera m’zochita zathu zonse.
Tikupemphani…, mutivomereze.
Atate, mutidzaze ndi Mzimu wanu Woyera kuti tisanduke mboni zenizeni za Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment