LAMULUNGU LA 04 PA CHAKA – A
“Ngwodala iwo amene azindikira umphawi wao.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI ZEFANIYA; ZEFANIYA 02: 03; 03: 12 – 13. (Pakati panu ndidzasiya anthu odzichepetsa ndi otsika.)
Funafunani Chauta, inu nonse odzichepetsa, inu amene mumamvera malamulo ake. Chitani zolungama, khalani odzichepetsa. Mwina mwake mudzatha kupulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Chauta. Pakati panu ndidzasiya anthu odzichepetsa ndi otsika. Iwowo adzafunafuna populumukira m’dzina la Chauta. Otsala a mu Israelewa sadzalakwanso, sadzalankhulanso zabodza, sadzachitanso zonyenga. Adzakhala pabwino mwamtendere, popanda wina wowaopsa.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 146: 07 – 10.
Ngwodala iwo amene ali wosauka mu uzimu chifukwa ufumu wa kumwamba ndi wawo.
Chauta amasunga malonjezo ake nthawi zonse.
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama,
Amawapatsa chakudya anthu anjala.
Chauta amamasula am’ndende.
Ngwodala iwo amene ali wosauka mu uzimu chifukwa ufumu wa kumwamba ndi wawo.
Chauta amatsekula maso a anthu osapenya,
Chauta amakweza anthu otsitsidwa,
Chauta amateteza alendo,
Amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye.
Ngwodala iwo amene ali wosauka mu uzimu chifukwa ufumu wa kumwamba ndi wawo.
Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,
Koma njira za anthu oipa amazipotoza,
Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya,
Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse.
Ngwodala iwo amene ali wosauka mu uzimu chifukwa ufumu wa kumwamba ndi wawo.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01: 26 – 31. (Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa.)
Abale, taganizani m’mene munaliri pamene Mulungu adakuitanani. Pakati panu panalibe ambiri amene anthu ankawayesa anzeru. Panalibenso ambiri amphamvu, kapena obadwa m’mabanja omveka. Koma Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa, kuti Iye anyazitse nazo anthu anzeru. Adasankhanso zimene anthu amaziyesa zofooka, kuti Iye anyazitse nazo anthu amphamvu. Ndipo zimene anthu amaziyesa zachabe, zonyozeka ndi zosakhala zenizeni, Mulungu adazisankha kuti athetse mphamvu zinthu zimene iwowo amayesa kuti ndiye zenizeni. Mulungu adachita zimenezi kuti pasakhale wina aliyense woti nkumadzitukumula pamaso pake. Mulungu ndiye adakulunzanitsani ndi Khristu Yesu, ndipo adamsandutsa kuti akhale nzeru yathu. Chifukwa cha Yesu, timapezeka olungama pamaso pa Mulungu. Ndi Yesuyo amene amatisandutsa anthu akeake a Mulungu, ndiye amatipulumutsa. Nchifukwa chake, monga Malembo anenera, Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO –
Alleluia, Alleluia – Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaaululira anthu osaphunzira. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 05: 01 – 12a. (Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao.)
Yesu poona chikhamu cha anthu chija, adakwera pa phiri. Iye atakakhala pansi, ophunzira ake adamtsatira pomwepo. Kenaka adayamba kuwaphunzitsa, adati, “Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. Ngodala anthu amene akumva chisoni, pakuti Mulungu adzawasangalatsa. Ngodala anthu ofatsa, pakuti Mulungu adzawapatsa dziko la pansi pano kuti likhale lao. Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao. Ngodala anthu ochitira anzao chifundo, pakuti iwonso Mulungu adzawachitira chifundo. Ngodala anthu oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu. Ngodala anthu odzetsa mtendere, pakuti Mulungu adzawatcha ana ake. Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m’menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, popeza kuti timadalira Mulungu pa zonse, tiyeni timupemphe thandizo lake m’zosowa zathu ndi za anthu onse:
1. Eklezia wa Mulungu aunikire anthu onse ndi maphunziro ake, ndipo chifundo chake chosamalira amphawi chidzetse Ufumu wa Mulungu pakati pa anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu amene akuzunzika chifukwa cha Mthenga Wabwino, alimbikire m’chikhulupiriro ndi kukondwera, podziwa kuti mphotho yao njaikulu kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Iwo amene amayesetsa kudzetsa chilungamo, mtendere ndi umodzi pakati pa anthu, apitirize ntchito yao mwakhama, podziwa kuti Mulungu adzawatcha ana ake.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse amene takomana muno, moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wokomera Mulungu ndi wodzaza ndi ntchito zachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, Inu mufuna kuti anthu onse alowe m’chikondwerero chanu. Mulimbitse chikhulupiriro chathu, mutikhazikitse m’chikondi chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment