LAMULUNGU LA 03 PA CHAKA (CYCLE A)
“Adandituma kuti ndilalike Mthenga Wabwino.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI YESAYA; YESAYA 08: 23 – 09: 01 – 04. (M’dziko la Galilea, anthu aona kuwala kwakukulu.)
Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu adaanyozetsa dziko la Zebuloni ndi la Nafutali, koma kutsogolo kuno adzalisandutsa laulemu dera lonseli, kuyambira ku Nyanja yaikulu kuzambwe mpaka kukafika ku dziko la patsidya pa mtsinje wa Yordani, ndiye kuti dziko la Galilea, dziko la anthu a mitundu ina. Anthu amene ankayenda mumdima aona kuwala kwakukulu. Amene ankakhala m’dziko la mdima wandiweyani, kuwala kwawaonekera. Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m’mene anthu amakondwera nthawi ya masika, monganso m’mene anthu amakondwera pogawana zofunkha. Pakuti inu mwathyola goli limene linkawalemera, ndodo zimene ankamenyera mapewa ao, ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza, monga mudachitira pogonjetsa Amidiyani.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 27: 01, 04, 13 – 14.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.
Ndidzaopa yani?
Chauta ndiye linga la moyo wanga,
Nanga ndichitirenji mantha?
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri,
Chakuti ndizikhala m’Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga,
Kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza lye m'Nyumba mwakemo.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.
Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta m’dziko la amoyo.
Tsono khulupirira Chauta,
Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima,
Ndithu, khulupirira Chauta.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO; 01 AKORINTO 01: 10 – 13, 17. (Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni.)
Abale, ndikukupemphani m’dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi. Pakuti ena a m’banja la Koloe andifotokozera kuti pali kukangana pakati panu, abale anga. Chimene ndikufuna nchakuti aliyense mwa inu akungonena zakezake. Wina akuti, “ine ndi wa Paulo,” winanso akuti, “ine ndine wa Apolo,” wina akuti, “ndine wa Kefa,” winanso akuti, “ine ndine wa Khristu.” Kodi Khristu wagawika? Kodi adakuferani pamtanda ndi Paulo? Kodi mudabatizidwa m’dzina la Paulo? Paja Khristu adandituma, osati kuti ndizibatiza ai, koma kuti ndizilalika uthenga wabwino. Ndipo ndiyenera kumaulalika mosagwiritsa ntchito luso lake la ulaliki, kuwopa kuti mtanda wa Khristu ungatheretu mphamvu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Mateyo 04: 23.
Alleluia, Alleluia – Yesu adalalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 04: 12 – 23. (Anakakhala ku Kapernao monga mneneri Yesaya adaanena.)
Yesu atamva kuti Yohane adamponya m’ndende, adabwera ku Galileya. Adachokako ku Nazarete, nakakhala ku Kapernao, Mzinda wina wa m’mbali mwa Nyanja ku dera la Zebuloni ndi Nafutali. Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena kuti, “iwe dziko la Zebuloni ndi iwe dziko la Nafutali, njira yakunyanja, patsidya pa Yordani, iwe Galileya, dziko la anthu akunja! Anthu okhala mu mdima aona kuwala kwakukulu. Anthu okhala m’dziko la mdima wabii wa imfa, kuwala kwawaonekera.” Kuyambira nthawi imeneyo Yesu adayamba kulalika kuti, “tembenukani mtima, chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.” Yesu akuyenda m’mbali mwa Nyanja ya Galileya, adaona anthu awiri pachibale pao: Simoni wotchedwa Petro, ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi. Yesu adawauza kuti, “inu, munditsate, ndikusandutseni asodzi a anthu.” Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi. Atapitirira pamenepo, Yesu adaona enanso awiri pachibale pao: Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwo anali m’chombo pamodzi ndi bambo waoyo, akukonza makoka ao, Yesu nkuwaitana. Pomwepo iwowo adasiya chombo chao ndi bambo wao uja, namatsata Yesu. Yesu adayendera dziko lonse la Galileya akuphunzitsa m’nyumba zamapemphero ndi kulalika uthenga wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam’thupi.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu
Abale, Yesu Khristu watiitana tonse ku ntchito yake. Tsono tiyeni tipemphere mogwirizana, kuti ufumu wa Mulungu ukhazikike mwa ife ndi mwa anthu onse.
1. Apapa ndi Aepiskopi onse, akhale a mtima umodzi polalika mthenga wa Khristu, ndipo atsogolere anthu ao m’njira ya ungwiro.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akhristu ofooka ndi otayika, atembenuke mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, pakumva mau a Mthenga Wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anyamata ndi atsikana oitanidwa, atembenukire ku ntchito zotumikira Mpingo, alimbikire pa maphunziro ao, ndipo alondole mapazi a Yesu Khristu mosacheukira m’mbuyo.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse osonkhana pano, tisenze udindo wachikhristu modzipereka ndi mogwirizana, potsogolera anzathu m’njira ya chikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, Inu mukudziwa zosowa za munthu aliyense. Mutigawireko zokoma za ufumu wanu, kuti tiyende molimba m’njira ya chipulumutso. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment