Saturday, January 14, 2023


LAMULUNGU LA 02 PA CHAKA – A.

“Umboni wa Yohane Mbatizi”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI YESAYA; YESAYA 49: 03, 05 – 06. (Ndidzakusandutsa kuwala kounikira mitundu in ya anthu, kuti chipulumutso changa chikafike mpaka ku mathero a dziko lapansi).

 

Chauta adandiuza kuti, “iwe Israele ndiwe mtumiki wanga. Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.” Chauta ndi amene adandiwumba m’mimba mwa amai anga kuti ndikhale mtumiki wake, kuti ndibweze fuko la Yakobe kwa Iye, ndipo kuti ndisonkhanitse Aisraele pafupi ndi Iye. Choncho ndimalemekezeka m’maso mwa Chauta, ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga. Chautayo akunena kuti, “nchinthu chochepa kwambiri kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobe ndi kuwabweza kwao Aisraele amene adapulumuka. Ndidzakusandutsa kuwala kounikira mitundu ina ya anthu, kuti chipulumutso changa chikafike mpaka ku mathero a dziko lapansi.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 40: 02, 04, 07 – 10.

 

Ndilipo, ndikubwera. Ndimakonda kuchita zimene mumafuna.

 

Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize,

Adaweramira pansi kuyang’ana kwa ine, namva kulira kwanga,

Mulungu waika nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga,

Nyimbo yake yotamanda Iye.

 

Ndilipo, ndikubwera. Ndimakonda kuchita zimene mumafuna.

 

Simudafune nsembe ndi zopereka,

Koma mwandipatsa makutu oti ndizimvera,

Simudapemphe nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo,

Tsono ndidati, “ndilipo, ndikubwera.”

 

Ndilipo, ndikubwera. Ndimakonda kuchita zimene mumafuna.

 

Monga zidalembedwa za ine m’buku la malamulo,

Ndimakonda kuchita zimene mumafuna,

Inu Mulungu wanga,

Malamulo anu ali mumtima mwanga.

 

Ndilipo, ndikubwera. Ndimakonda kuchita zimene mumafuna.

 

Ndalalika uthenga wabwino wa chipulumutso chanu,

Pa msonkhano waukulu,

Sindidatseke pakamwa,

Monga mukudziwa, Inu Chauta.

 

Ndilipo, ndikubwera. Ndimakonda kuchita zimene mumafuna.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO; 01 AKORINTO 01: 01 – 03. (Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere).

 

Abale, ndine, Paulo, amene mwa kufuna kwa Mulungu ndidaitanidwa kuti ndikhale mtumwi wa Khristu Yesu. Ndili pamodzi ndi mbale wathu, Sostene. Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto. Mulungu adakupatulani mwa Khristu Yesu, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake, pamodzi ndi anthu onse amene ponseponse amatama dzina la Ambuye Yesu Khristu mopemba. Iye ndi Mbuye wathu ndi Mbuye waonso. Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Yohane 01:14a, 12a.

 

Alleluia, Alleluia – Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu; kwa amene adaamlandira nakhulupirira dzina lake, Iye adawapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu.  – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 01: 29 – 34. (Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu).

 

M’mawa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lapansi. Iyeyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘pambuyo panga pakubwera munthu wopambana ine, pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo,’ Inenso sindinkamudziwa, koma ndidabwera kudzabatiza ndi madzi kuti Aisraele amdziwe.” Yohane adachitanso umboni, adati, “ndidaona Mzimu Woyera akutsika kumwamba ngati nkhunda, nakhazikika pa Iye. Ine sindinkamudziwa, koma Mulungu amene adandituma kudzabatiza ndi madzi, ndiye adaandiwuza kuti, ‘amene udzaone Mzimu Woyera akutsika ndi kukhazikika pa Iye, ndi Iyeyo wobatiza mwa Mzimu Woyera.’ Ineyo ndidazionadi, ndipo ndikuchita umboni kuti ameneyu ndi Mwanadi wa Mulungu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu

 

Abale, Mulungu adatipatula natiyeretsa mwa Yesu Khristu kuti tikhale anthu akeake. Tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba, kuti adalitse anthu onse ndi kuwapatsa mtendere:

 

1. Eklezia, Mpingo wa Yesu, aonetse makhalidwe a ungwiro, akhale ngati nyale younikira onse ndi chizindikiro chosonyeza chipulumutso.

Tikupemphani…, mutivomereze.

 

2. Anthu a mafuko onse okhala mu mdima, Mulungu awaunikire mpaka adzazindikire kuwala kwa Yesu Khristu ndi chifundo chake chofuna kuwapulumutsa.

Tikupemphani…, mutivomereze.

 

3. Apapa ndi Aepiskopi onse, akhale a mtima umodzi, pokumbukira Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene adadzachotsa machimo a anthu onse.

Tikupemphani…, mutivomereze.

 

4. Ife tonse tili muno, timchitire Ambuye Yesu umboni pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, makamaka pakutumikira anzathu ndi mtima wachikondi.

Tikupemphani…, mutivomereze.

 

Atate, pamodzi ndi anthu onse amene amatamanda Yesu Khristu, tikuyamika kukoma mtima kwanu, chifukwa mwa Mwana wanuyo mudatipatsa madalitso onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

--------------------------------------

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...