Saturday, January 7, 2023

CHAKA CHA EPIFANIYA WA AMBUYE YESU – A

Yesu Mpulumutsi adadzera anthu a mitundu yonse.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI YESAYA; YESAYA 60: 01 – 06. (Ulemerero wa Chauta udzawonekera).

Iwe Yerusalemu dzuka, wala, kuwala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuwalira. Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuwalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Anthu a mitundu ina adzatsata kuwala kwako, mafumu adzalondola kunyezimira kwako konga dzuwa limene likutuluka kumene. Yang’ana pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Onse akusonkhana kuti abwere kwa iwe. Ana ako aakazi adzatengedwa m’manja ngati ana. Udzaona zimenezi, ndipo udzakondwa, mtima wako udzalumpha ndi chimwemwe. Chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe. Chuma cha maiko onse chidzabwera kwa iwe. Kudzafika mtindiri wa ngamira, ngamira zing’onozing’ono, kuchokera ku Midiyani ndi ku Efa. Onse a ku Sheba adzabwera. Adzakhala atatenga golide ndi lubani, ndipo adzatamanda Chauta mokweza mau.

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 72: 01 – 02, 07 – 08, 10 – 13.

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

 

Inu Mulungu, patsaniko mfumu nzeru zoweruzira,

Patsaniko mwana wa mfumu mtima wokonda chilungamo,

Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama,

Ndiponso anthu anu osauka mosakondera.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

 

Mafumu a ku Tarisisi ndi akuzilumba adzaipatsa mitulo,

Mafumu a ku Sheba ndi a ku Seba adzabwera ndi mphatso,

Mafumu onse adzaigwadira,

Ndipo mitundu yonse ya anthu idzaitumikira.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

 

Ndithu iyo idzalanditsa anthu osowa amene amaiitana,

Idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda wowathandiza,

Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osowa,

Ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphawi.

 

Mafumu onse adzakugwadirani ndipo mitundu yonse ya anthu idzakutumikirani, Ambuye.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO; AEFESO 03: 02 – 03, 05 – 06. (Chinsinsicho nchakuti anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda.)

Abale, kumva munamva za ntchito imene mwa ufulu wake Mulungu adandipatsa, yolalika pakati panu za kukoma mtima kwake. Adandiwululira chinsinsi chake, monga ndidakulemberani mwachidule posachedwapa. Chinsinsi chimenechi anthu a mibadwo yakale sadachidziwe, koma Mulungu wachiwulula tsopano mwa Mzimu Woyera kwa atumwi ake oyera mtima, ndiponso kwa aneneri ake. Chinsinsicho nchakuti mwa uthenga wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu.

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Mateyo 02: 02.

Alleluia, Alleluia – Ife tidaona nyenyezi ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza Ambuye. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 02: 01 – 12. (Ife tidaona nyenyezi ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza Ambuye).

Yesu adabadwira m’mudzi wa Betelehemu, m’dziko la Yudeya, pa nthawi imene Herode anali mfumu ya Dzikolo. Ndiye kudabwera akatswiri ena a Nyenyezi ku Yerusalemu kuchokera kuvuma. Iwowo ankafunsa kuti, “ali kuti mwana amene adabadwa kuti adzakhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona Nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.” Mfumu Herode atamva zimenezi, adavutika kwambiri ndipo anthu ena onse a m’Yerusalemu nawonso adavutika nazo. Tsono Herode yo adasonkhanitsa akulu onse a ansembe ndi Aphunzitsi onse a Malamulo a Mose, nawafunsa kuti, “kodi paja adati Mpulumutsi wolonjezedwa ndi Mulungu uja adzabadwira kuti?” Iwo adati, “m’mudzi wa Betelehemu ku Yudeya. Pajatu mneneri adalemba kuti, ‘iwe Betelehemu wa m’dziko la Yuda, sindiwe wamng’ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda. Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri pamene adzalamulira anthu anga Aisraele.’” Pamenepo Herode adawaitanira paseri akatswiri a Nyenyezi aja, nawafunsitsa za nthawi yeniyeni imene adaaiwonera Nyenyezi yo. Kenaka adawatumiza ku Betelehemu nkuwaudza kuti, “Pitani, kafunsitseni za mwanayo. Mukakampeza, mudzandidziwitse, kuti inenso ndidzapite kukampembedza.” Anthu aja atamva mau a mfumu, adanyamuka. Nyenyezi imene adaaiwona kuvuma ija idawatsogolera mpaka idakafika nkukaima pamwamba pa malo amene panali mwanayo. Ataiwona nyenyeziyo, adasangalala kwabasi. Adalowa m’nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake, ndipo Adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure. Mulungu adawachenjeza m’maloto kuti asadzerenso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao.

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...