CHAKA CHA MARIA WOYERA, AMAI A MULUNGU – A
“Adabadwa mwa Virgo Maria.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NUMERI; NUMERI 06: 22 – 27. (Akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzawadalitsadi).
Chauta adauza Mose kuti, “uza Aroni ndi ana ake kuti azidalitsa Aisraele motere: Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang’aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima.
Chauta akuyang’aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.” Ndipo Chauta adati, “akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzawadalitsadi.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 67: 02 – 03, 05 – 06, 08.
Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.
Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa,
Mutiwunikire ndi chikondi chanu,
Njira yanu idziwike pa dziko lonse lapansi,
Chipulumutso chanu chidziwike pakati pa mitundu yonse.
Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.
Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe,
Chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo,
Ndi kuwatsogolera pa dziko lapansi.
Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.
Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu,
Mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.
Inde, Mulungu watidalitsa,
Anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze lye.
Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AGALATIYA; AGALATIYA 04: 04 – 07. (Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi).
Abale, nthawi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu. Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m’mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, ‘Abba! Atate!’ Motero sindiwenso kapolo ai, koma mwana. Ndipo popeza kuti ndiwe mwana wake, Mulungu adakusandutsanso mlowachuma wake.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Aheberi 01: 01 – 02.
Alleluia, Alleluia – Kale lija pa nthawi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano, walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 02: 16 – 21. (Adampeza Maria ndi Yosefe ndi Mwanayo …Pamene tsiku la chisanu ndi chitatu linakwana anampatsa mwanayo dzina loti Yesu).
Abusa adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m’chodyera cha zoweta chija. Pamene adamuwona, abusawo adawafotokozera zimene mngelo uja adaawauza za mwanayo. Onse amene ankamva, ankadabwa ndi zimene abusawo ankawasimbira. Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake. Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaawauzira. Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment