KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – CHAKA A
[MISA YA MASANA]
“Adadzatisandutsa ana a Mulungu.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 52: 07 – 10. (Dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu).
Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m’mapiri, kubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu. Mverani, alonda anu akukweza mau, akuimba pamodzi mokondwa, popeza kuti akuwona chamaso Chauta akubweranso ku Ziyoni. Fuulani mokondwera inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Chauta wawatonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu. Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98: 01 – 06.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,
Popeza kuti wachita zodabwitsa,
Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo,
Waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse kuti Iye ndi wolungama,
Wakumbukira chikondi chake chosasinthika,
Ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi,
Aona chipulumutso cha Mulungu wathu,
Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi.
Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe,
Lizani pangwe ndi nyimbo zokoma,
Imbirani Chauta Mfumu,
Imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.
Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA KWA AHEBERI; AHEBERI 01: 01 – 06. (Mulungu analankhula kwa ife kuchokera kwa Mwana wake).
Abale, kale lija pa nthawi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati cholowa chake. lye ndiye kuwala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuwachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero. Mwana wa Mulunguyo ngwoposa angelo, monga momwe dzina limene Mulungu adampatsa limaposera dzina la angelo. Nchifukwa chake kale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala.” Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti, “Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga.” Koma pamene ankatuma Mwana wake wachisamba pansi pano, Mulungu adati, “Angelo onse a Mulungu azimpembedza.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Yohane 01: 01 – 18.
Alleluia, Alleluia – Tsiku loyera lija latifikira ife. Bwerani inu mafuko onse, kuti timulambire Ambuye, popeza lero kuwala kwationekera pa dziko lonse lapansi. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 01: 01 – 05, 09 – 14. (Mau aja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu).
Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu. Anali kwa Mulungu chikhalire. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye. Mwa lyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuwala kounikira anthu. Kuwalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuwalako. Kuwala kwenikweni, kounikira anthu onse, kunkadza pansi pano. Wotchedwa Mauyo anali m’dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa lye, komabe anthu apansipano sadamzindikire. Adaabwera kwao ndithu, koma anthu ake omwe sadamlandire. Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo amenewa lye adawapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m’kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu. Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment