Saturday, March 25, 2023

 

LAMULUNGU LA 05 MU NYENGO YA LENTI – CHAKA A

“Woukitsa anthu kwa akufa ndine.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI EZEKIELE; EZEKIELE 37: 12 – 14 (Ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo).

 

Ine Ambuye Chauta ndikuti, “inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo. Ndidzakubwezerani ku dziko la Israele. Motero Mudzadziwa kuti ine ndine Chauta, ndikadzafukula manda anu ndi kukutulutsanimo, inu anthu anga. Tsono ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo, pambuyo pake ndidzakukhazikani m’dziko lanu. Choncho Mudzadziwa kuti ine Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero ine Chauta.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 130: 01 – 04. 05 – 08.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Ndikulirira Inu Chauta, ndili m’dzenje lozama lamavuto,

Ambuye imvani liwu langa,

Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga.          

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Inu Chauta, mukadawerengera machimo,

Ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye?

Koma inu mumakhululukira,

Nchifukwa chake timakulemekezani.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta,

Ndimayembekeza ndi mtima wonse ndipo ndimakhulupirira mau ake,

Mtima wanga umayembekeza Chauta,

Kupambana m’mene alonda amayembekeza mbandakucha, Iwe Israele, khulupirira Chauta.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika,

Ndi wokonzeka kupulumutsa,

Adzaombola Israele ku machimo ake onse.

 

Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika ndi wokonzeka kupulumutsa.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 08: 08 – 11 (Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu).

 

Abale, anthu oipa mtima pa khalidwe limenelo, sangathe kukondweretsa Mulungu. Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufawa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 11: 25a, 26.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Ine Ndine kuuka ndinso moyo, aliyense wokhulupirira Ine sadzafa. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 11: 01 – 45 (Ine Ndine kuuka ndinso moyo).

 

Panali munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadwala. Anali wa ku mudzi wa Betaniya, kwao kwa Maria ndi mbale wake Marita. Mariayo ndi yemwe uja amene adaadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira, nkupukuta mapazi ao ndi tsitsi lake. Lazaro ankadwala yo anali ndi mlongo wake. Tsono alongo ake aja adatumiza thenga kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, bwenzi lanu uja akudwala.” Pamene Yesu adamva zimenezi adati, “kudwalako safanako ai, koma zatero kuti Mulungu alemekezedwe, ndipo kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.” Ndiye kuti Yesu ankakonda Marita ndi mng’ono wake Maria ndiponso Lazaro. Komabe pamene adamva za matendawo, Yesu adaswera masiku awiri pamalo pomwe adaaliripo. Pambuyo pake adawuza ophunzira ake kuti, “tiyeni tipitenso ku Yudeya.” Ophunzira akewo adati, “Aphunzitsi, tsopano apa Ayuda ankafuna kukuponyani miyala, ndiye mukuti mupitenso komweko?”  Yesu adati, “kodi suja usana uli ndi maora khumi ndi awiri? Munthu akayenda masana, sakhumudwa, chifukwa amaona kuwala kwa dzikoku. Koma akayenda usiku, amakhumudwa chifukwa kuwalako alibe.” Atatero adawauza kuti, “Lazaro bwezi lathu, wagona tulo, koma ndipite kuti ndikamudzutse ku tulo taketo.” Apo ophunzira ake adati, “Ambuye, ngati wagona tulo, achira.” Iwo ankayesa kuti akunena za tulo teniteni, koma Yesu ankanena za imfa yake ya Lazaro. Tsono Yesu adawauza mosabisa kuti, “Lazaro wamwalira, komabe chifukwa cha inu ndikukondwera kuti ine kunalibe kumeneko, kuti choncho mukakhulupirire. Tiyeni tipiteko.” Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, adauza ophunzira anzake kuti, “tiyeni ifenso tipite nao kuti tikafe naye pamodzi.”

 

Pamene Yesu adafika ku Betaniya, adapeza Lazaro atagona m’manda masiku anai. Ku Betaniya kunali kufupi ndi ku Yerusalemu, mtunda wokwanira pafupi makilomita atatu. Panali anthu ambiri amene adaabwera kwa Marita ndi Maria kudzawapepesa chifukwa cha imfa ya mlongo wao. Pamene Marita adamva kuti Yesu akubwera, adapita kukamchingamira. Koma Maria adaatsalira m’nyumba. Tsono Marita adauza Yesu kuti, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira. Koma ngakhale tsopano, ndikudziwa kuti Mulungu adzakupatsani zilizonse mungapemphe.” Yesu adamuuza kuti, “Mlongo wako adzauka.”  Marita adati, “ndikudziwa kuti adzauka podzauka anthu kwa akufa pa tsiku lomaliza.” Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso wowapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?” Iye adati, “Inde Ambuye, ndikukhulupirira kuti inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, mwana wa Mulungu, amene adayenera kubwera pansi pano.” Marita atanena zimenezi, adaitanira paseri Maria mng’ono wake namuuza kuti, “afika Aphunzitsi, akukuitana.” Maria atamva zimenezi, adanyamuka msangamsanga, nadza kwa Yesu. Pamenepo nkuti Yesu asanafike kumudziko, koma anali chikhalire pamalo pomwe Marita adaakumana naye. Anthu amene anali m’nyumba akupepesa Mariayo, ataona kuti wanyamuka msangamsanga ndikutuluka, adamtsatira. Ankayesa kuti akupita kumanda kukhalira kumeneko.

 

Maria atafika pamene panali Yesu, namuona, adadzigwetsa kumapazi kwake nati, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira.” Yesu ataona Maria akulira, ndiponso anthu amene adadza naye iwonso akulira, zidamukhudza kwambiri ndipo adavutika mu mtima. Tsono adawafunsa kuti, “mudamuika kuti?” Iwo adati, “Ambuye, tiyeni mukaone.” Yesu adayamba kulira. Pamenepo anthu aja adati, “Onani, ankamukonda zedi.” Koma ena mwa iwo adati “Munthu uyu suja adapenyetsa munthu wosapenya uja? Monga sakadatha kuchitapo kanthu kuti Lazaro asafe?” Yesu adavutikanso mu mtima, nakafika ku manda amene anali phanga. Pakhomo pake panali chimwala. Tsono adati, “tachotsani chimwalacho.” Marita, mlongo wa womwalirayo, adamuuza kuti, “pepani Ambuye, wayamba kale kununkha, pakuti wagonamo masiku anai.” Yesu adamufunsa kuti, “kodi sindinakuuze kuti ukakhulupirira uwona ulemerero wa Mulungu?” Tsono anthu adachotsa chimwala chija. Yesu adayang’ana kumwamba nati, “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimvera. Ndikudziwa kuti mumandimvera nthawi zonse. Koma ndanena zimenezi chifukwa cha khamu la anthu amene ali panowa, kuti akhulupirire kuti ndinu mudandituma.” Atatero adaitana mokweza mau kuti, “Lazaro, tuluka.” Pomwepo munthu amene adaamwalirayo adatuluka, miyendo yake ndi manja ake zili zomangidwa ndi nsalu zamaliro. Nkhope yake inali yokutidwa ndi nsalu. Yesu adawauza kuti, “mmasuleni, ndipo mlekeni azipita.” Ambiri mwa anthu amene adaabwera kwa Maria, adaona zimene Yesu adachita, ndipo adakhulupirira.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, popeza kuti Mzimu wake wa Khristu akhala mwa ife, tiyeni tipemphere ndi chikhulupiriro, podziwa kuti Mulungu adzatipatsa zili zonse zimene tingamupemphe:

 

1.     Atsogoleri olalika mau a Mulungu apitirire kulimbitsa mitima ya anthu, powalalikira za kuuka kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Adokotala ndi anamwino ogwira ntchito m’zipatala, aonetse anthu odwala mtima wachifundo powasamalira bwino.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Anthu amene ali pafupi kufa ndinso onse amene ali ofedwa, aike chikhulupiriro chao mwa Yesu Khristu, kuti Iyeyo awalimbikitse.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

4.     Ife tomwe tili muno, Mzimu Woyera apititize ntchito yake mwa ife potiwongolera m’njira ya ungwiro ndi ya chikondi.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, tikukuyamikani chifukwa mwa Mzimu Woyera wanu mwatipatsa chiyembekezo cha kukondwera pamodzi nanu mpaka muyaya. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...