LAMULUNGU LA KANJEDZA (CHIYAMBI CHA MLUNGU WOYERA) – CHAKA A
“Adapita ndi Yesu kuti akampachike.”
Mwambo wodalitsira Nthambi [KU MDIPITI]
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA: MATEYO 21: 01 – 11 (Ngwodala amene alikudza m' dzina la Ambuye).
Pamene iwo ankayandikira ku Yerusalemu, nkufika ku Betefage, ku phiri la Olivi, Yesu adatuma ophunzira awiri, nawauza kuti, “Pitani m’mudzi mukuwonawo. Mukakangolowamo, mukapeza bulu ali chimangile, ndi mwana wake ali naye pamodzi. Mukawamasule nkubwera nawo kuno. Wina akakakufunsani kanthu, inu mukati, ‘Ambuye ali nawo ntchito, akangothana nawo awatumiza nthawi yomweyo.’” Zimenezi zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri adaanena kuti, “uzani mzinda wa Ziyoni kuti, ‘ona mfumu yako ikudza kwa iwe. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu. Zoonadi yakwera pa kabulu, mwana wa nyama yosenza katundu.’” Tsono ophunzira aja adapitadi nakachita monga momwe Yesu adaawalamulira. Adabwera naye bulu ndi mwana wake uja, nayala zovala zao pamsana pa abuluwo, Yesu nkukwerapo. Anthu ambiri ankayala zovala zao mu mseu, ndipo ena adakadula nthambi za mitengo nkumaziyalika mumseumo. Anthu ochuluka amene anali patsogolo, ndi amene anali m’mbuyo, adayamba kufuula kuti, “ulemu kwa mwana wa Davide. Ngwodala amene alikudza m’dzina la Ambuye. Ulemu kwa Mulungu kumwambamwambba.” Pamene Yesu adalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse udatekeseka, ena nkumafunsa kuti, “kodi ameneyu ndani?” Tsono onse aja adayankha kuti, “ameneyu ndi mneneri Yesu wochokera ku Nazarete, ku Galileya.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MNENERI YESAYA: YESAYA 50: 04 – 07 (Sindidawabisire nkhope ondinyoza. Ndikudziwa kuti Chauta
sadzandichititsa manyazi).
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziwe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M’mawa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira. Ambuye Chauta anditsekula makutu, ndipo sindidawanyoze kapena kuwapandukira. Ndidaperekera msana wanga kwa ondimenya, ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu. Sindidawabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu. Koma kunyoza kwawo sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziwa kuti sadzandichititsa manyazi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 22: 07 – 08. 16 – 19. 23 – 24.
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
Onse ondiwona amandiseka,
Amandikwenzulira ndi kupukusa mitu yao,
Amati, “unkadalira Chauta, Chauta yemweyo akupulumutse,
Akulanditsetu tsono, popeza kuti amakukonda.”
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
Anthu ankhanza andizinga ngati mimbulu,
Aboola manja anga ndi mapazi anga,
Mafupa anga akuwonekera, koma anthu aja akungondiyang’anitsitsa,
Akukondwera poona kuti ndikuvutika.
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
Agawana zovala zanga, ndipo achitira malaya anga maere,
Koma Inu Chauta musakhale kutali,
Inu, mphamvu zanga, fulumirani kudzandithandiza.
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu,
Ndidzatamanda dzina lanu pa msonkhano wa anthu anu,
Ndidzati, ‘inu omvera Chauta, mtamandeni Iye,
Inu nonse ana a Yakobe mlemekezeni Iye,
Inu nonse ana a Israele, mchitireni Iye ulemu.’
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI; AFILIPI 2: 6 – 11 (Ali munthu choncho adadzichepetsa, koma Mulungu adamkweza kopambana).
Abale, Yesu Khristu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingama ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphawi wa kapolo, ndi kukhala munthu monga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. Adachita zimene zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AFILIPI 02: 08 – 09.
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Ambuye, adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Nchifukwa chake chimene Mulungu adamkweza kopambana nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: KUSAUKA KWA YESU KHRISTU AMBUYE ATHU MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 26: 14 – 27: 66 ().
W – Wowerenga. | Y – Yesu. | M – Munthu. | A – Anthu ena.
1. Yesu adadya nawo phwando la Pasaka, napanga Ukaristia.
W. Pambuyo pake Yudasi Iskariote, m’modzi mwa ophunzira khumi ndi awiri aja, adapita kwa akulu a ansembe. Adakawafunsa kuti,
M. Kodi mudzandipatsa chiyani ndikadzampereka Yesuyu kwa inu?
W. Iwo adamupatsa ndalama zasiliva makumi atatu. Tsono kuyambira pomwepo iye adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo. Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, ophunzira aja adadza nafunsa Yesu kuti:
W. Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Pasaka?
W. Iye adawauza kuti:
Y. Pitani m’mudzimu kwa munthu wina wake. Mukanene kuti, Aphunzitsi akuti nthawi yao ili pafupi, akudzadyera kwanu kuno phwando la Pasaka pamodzi ndi ophunzira ao.
W. Ophunzira aja adapita nakachita zomwe Yesu adaawauza, nakakonzadi za phwando la Pasaka. Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi awiri aja adakhala pamodzi nkumadya. Iwowo alikudya, Yesu adawauza kuti:
Y. Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu andipereka kwa adani anga.
W. Ophunzirawo adamva chisoni kwambiri, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti:
M. Monga nkukhala ine, Ambuye?
W. Yesu adawayankha kuti:
Y. Yemwe wasunsa mkate m’mbalemu pamodzi ndi Ine, ameneyo ndiye andipereke. Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.
W. Yudasi, amene pambuyo pake adapereka Yesu, adafunsa kuti:
M. Monga nkukhala ine, Aphunzitsi?
W. Yesu adamuyankha kuti:
Y. Wanena wekha.
W. Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati:
Y. Kwayani, idyani, ili ndi thupi langa.
W. Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adawauza kuti:
Y. Imwani nonsenu. Pakuti awa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi amenewa ndiwakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu awakhululukire
machimo ao. Kunena zoona, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano pamodzi nanu mu Ufumu wa Atate anga.
[Kanyimbo]
2.Yesu adakapemphera ku munda wa Getsemani.
W. Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi. Pambuyo pake Yesu adawauza kuti:
Y. Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya usiku uno. Paja Malembo akuti, “Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa za msambiwo zidzangoti balala.” Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.
W. Petro adati:
M. Ngakhale onse akhumudwe nkukusiyani, ine ndekha ai.
W. Yesu adamuuza kuti:
Y. Ndithu ndikunenetsa kuti usiku womwe uno, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziwa.
W. Koma Petro adamuuza kuti:
M. Ngakhale atati andiphere nanu kumodzi, ine sindingakukaneni konse kuti sindikudziwani.
W. Ophunzira ena onse aja nawonso adanena chimodzimodzi. Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti:
Y. Inu bakhalani pano, Ine ndikupita uko kukapemphera.
W. Adatengako Petro ndi ana awiri aja a Zebedeo. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima. Adawauza kuti:
Y. Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, komatu mukhale maso pamodzi nane.
W. Adapita patsogolo pang’ono, nadzigwetsa choweramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati:
Y. Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.
W. Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, nawapeza ali m’tulo. Tsono adafunsa Petro kuti:
Y. Mongadi nonsenu mwalephera kukhala maso pamodzi nane ngakhale pa kanthawi kochepa? Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m’zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.
W. Adachokanso kachiwiri nakapemphera kuti:
Y. Atate, ngati chikho chamasautsochi sichingandichoke, mpaka nditamwa ndithu, chabwino, zimene mukufuna zichitike.
W. Pamene adabwerakonso, adawapeza ali m’tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera. Yesu adawasiyanso, napita kukapemphera kachitatu, akunena mau amodzimodzi omwe aja.
Pambuyo pake adabwera kwa ophunzira ake nati:
Y. Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Ndipotu nthawi ija yafika, Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa anthu ochimwa. Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.
W. Yesu akulankhula choncho, wafika Yudasi, m’modzi mwa ophunzira khumi ndi awiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaawatuma ndi akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda. Wodzampereka uja anali atawauza chizindikiro kuti:
M. Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo, mukamugwire. Tsono Yudasi adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti:
M. Moni Aphunzitsi!
W. Atatero adamumpsompsona. Yesu adamuuza kuti:
Y. Bwenzi langa, chita zimene wadzera.
W. Apo anthu aja adabwera namugwira Yesu. Koma wina mwa amene anali limodzi ndi Yesu, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu. Apo Yesu adamuuza kuti:
Y. Bwezera lupangalo m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga. Kodi ukuyesa kuti Ine sindingapemphe Atate, Iwo nthawi yomweyo nkunditumizira magulu ankhondo a angelo oposa khumi ndi awiri? Koma ndikadatero, nanga zikadachitika bwanji zimene Malembo adaneneratu kuti ziyenera kuchitika?
W. Pamenepo Yesu adawafunsa anthu aja kuti:
Y. Bwanji mwachita kudzandigwira muli ndi malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigawenga? Tsiku ndi tsiku ndinkakhala pansi m’Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira. Koma zonsezi zachitika kuti ziwonekedi zimene aneneri adalemba.
W. Pamenepo ophunzira ake onse aja adathawa, kumusiya yekha.
[Kanyimbo]
3. Anthu aja adapita naye Yesu ku Bwalo la Ayuda.
W. Tsono anthu amene adagwira Yesu aja adapita naye kunyumba kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda. Koma Petro ankamutsatira chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adalowa mkati, nakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu kuti one m’mene zithere.
Akulu a ansembe aja ndi onse a m’Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni wonama woneneza Yesu kuti amuphe. Koma sadaupeze ngakhale padaabwera mboni zambiri zabodza. Potsiriza padabwera anthu awiri. Adati:
A. Munthu uyu ankati, ‘Ine ndingathe kupasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu.’
W. Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira nafunsa Yesu kuti:
M. Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuwa akukunenezazi?
W. Koma Yesu adangokhala chete. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adauza Yesu kuti:
M. Ndikukulamula m’dzina la Mulungu wamoyo kuti utiwuze molumbira ngati ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu.
W. Yesu adamuyankha kuti:
Y. Mwanena nokha. Komanso ndikukuuzani kuti kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu Wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.
W. Apo mkulu wa ansembe uja adang’amba zovala zake nati:
M. Kunyoza Mulungu koopsatu kumeneku! Kodi pamenepa nkufunanso mboni zina ngati? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku. Ndiye inu mukuganiza bwanji?
W. Iwo aja adayankha kuti:
A. Ayenera kuphedwa.
W. Pomwepo iwo adayamba kumthira malovu kumaso nkumamumenya, ena kumamuwomba makofi, nkumanena kuti:
A. Iwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, nanga sindiwe mneneri? Lota, wakumenya ndani?
W. Petro adaakhala kunja m’bwalo la nyumba ija. Mtsikana wina wantchito adabwera namuuza kuti:
M. Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.
W. Koma iye adakana pamaso pa anthu onse, adati:
M. Sindikuzidziwa zimenezo ine.
W. Pamene Petro ankatuluka kumapita ku chipata, mtsikana winanso wantchito adamuwona, nayamba kuuza amene anali pamenepo kuti:
M. Akulu amenewa anali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.
W. Petro adakananso molumbira kuti:
M. Ndithudi sindikumdziwa munthu ameneyo.
W. Ndipo patangopita kanthawi, anthu amene anali pamenepo adadza nauza Petro kuti:
A. Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli, tadziwira kalankhulidwe kakoka.
W. Apo Petro adayamba kulumbira nkumanena kuti:
M. Mulungu andilange, munthu mukunenayu ine sindimdziwa konse.
W. Nthawi yomweyo tambala adalira. Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire, ukhala utakana katatu kuti sundidziwa.” Pomwepo adatuluka, nakalira misozi ndi chisoni chachikulu. Kutacha akulu a ansembe onse ndi akulu a Ayuda adasonkhana kuti apangane zoti aphe Yesu. Adammanga, napita naye kwa Pilato, mkulu wa Boma. Pamene Yudasi uja, amene adapereka Yesu kwa adani ake, adaona kuti mlandu wamuipira Yesu, adalapa. Tsono adakawabwezera akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda aja ndalama makumi atatu zasiliva zija. Adati:
M. Ndidachimwa pakupereka munthu wosalakwa kuti aphedwe.
W. Koma iwo adati:
A. Ife tilibe nazo kanthu. Nzako zimenezo.
W. Yudasi adaponya ndalama zija m’Nyumba ya Mulungu, nachokapo ndi kukadzikhweza. Akulu a ansembe aja adatola ndalamazo nati:
A. Malamulo athu satilola kuika ndalamazi mosungira chuma cha Nyumba ya Mulungu ai, popeza nza magazi.
W. Tsono adapangana kuti ndalamazo agulire munda wa mmisiri woumba mbiya kuti ukhale manda a alendo. Chifukwa chake mpaka lero mundawo umatchedwa “Munda wa magazi.” Apo zidachitikadi zimene mneneri Yeremiya adanena kuti, “Adatenga ndalama zija makumi atatu (mtengo wake umene Aisraele adagamula) nagulira munda wa mmisiri woumba mbiya, monga momwe ambuye adandilamulira.”
[Kanyimbo]
4. Kwa Pilato, mkulu wa Boma.
W. Tsono adaimika Yesu pamaso pa mkulu wa Boma. Iye adafunsa Yesu kuti:
M. Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?
W. Yesu adati:
Y. Mukutero ndinu.
W. Koma pamene akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda aja anali kumneneza, Yesu sadayankhepo kanthu. Tsono Pilato adamfunsa kuti:
M. Kodi sukumva zonse ali kukunenezani?
W. Koma Yesu sadamuyankhe ndi mau amodzi omwe, kotero kuti mkulu wa Boma uja anadabwa kwambiri. Pa nthawi ya chikondwerero cha Pasaka, mkulu wa Boma ankamasulira anthu wandende mmodzi, yemwe iwo ankafuna. Pa nthawi imeneyo padaali wandende wina wodziwika, dzina lake Barabasi. Tsono pamene anthu aja adasonkhana, Pilato adawafunsa kuti:
M. Mufuna kuti ndikumasulireni uti, Barabasi, kapena Yesu, wotchedwa Khristu?
W. Adatero popeza adadziwa kuti adapereka Yesu chifukwa cha kaduka chabe. Pilato ali pa mpando woweruzira milandu, mkazi wake adamtumizira mau. Adati:
M. Musachite naye kanthu munthu wolungamayo, pakuti maloto andivuta kwambiri usiku chifukwa cha lye.
W. Akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adakakamiza anthu kupempha Pilato kuti amasule Barabasi, ndipo kuti Yesu aphedwe.
Tsono pamene mkulu wa Boma uja adawafunsa kuti, ‘Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awiriwa?' Anthu aja adati:
A. Barabasi.
W. Pilato adawafunsa kuti:
M. Nanga tsono ndichite naye chiyani Yesuyu, wotchedwa Khristu?
W. Anthu onse aja adati:
A. Ampachike pa mtanda.
M. Ine ndekha ndilibe kanthu pa imfa ya munthu uyu. Zimenezo nzanu.
W. Anthu onse aja adati:
A. Chilango chigwere ife ndiponso ana athu chifukwa cha imfa yake.
W. Apo Pilato adawamasulira Barabasi, koma adalamula kuti Yesu akwapulidwe, ndipo pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa manda. Pamenepo asirikali a mkulu wa Boma uja adalowetsa Yesu m’nyumba ya mkuluyo. Ndipo adasonkhanitsa gulu lonse la asirikali anzao, nazinga Yesu. Adamvula, namveka malaya ofiira. Adaluka chisoti chaminga, nachiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa bango m’dzanja lamanja. Kenaka adamgwadira, nasewera naye mwachipongwe ndi kunena kuti:
A. Moni, Amfumu ya Ayuda.
W. Adamthira malovu, natenga bango lija ndi kummenya m’mutu. Atasewera naye choncho, adamvula malaya aja, namvekanso zovala zake. Ndipo adamtenga, napita naye kuti akampachike pamtanda.
[Kanyimbo]
5. Ku Gologota.
W. Pamene anali kutuluka, adakomana ndi munthu wina dzina lake Simoni wa ku Kirene. Asirikali aja adamlamula kuti anyamule mtanda wa Yesu. Ndipo adafika ku malo otchedwa Gologota, tanthauzo lake ndiye kuti “malo a Chibade cha Mutu.” Kumeneko adampatsa Yesu vinyo wosakaniza ndi ndulu, kuti amwe. Koma atalawa, adakana kumwa. Atampachika pamtanda, adagawana zovala zake pakuchita mare. Kenaka adakhala pansi, namamlonda. Pa mwamba pa mutu wake adalembapo mau osonyeza mlandu womphera, akuti, “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.” Adapachikanso pamtanda zigawenga ziwiri, chigawenga china ku dzanja la manja, china ku dzanja lamanzere. Anthu amene ankadutsa pamenepo, analikumnenera mau achipongwe, ndi kumapukusa mitu. Anali kunena kuti:
A. Suja unkati, 'Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu ndi kumanganso pa masiku atatu?' Ngati ndiwedi Mwana wa Mulungu tadzipulumutsa ndi kutsika pamtandapo.
W. Nawonso akulu a ansembe pamodzi ndi aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda, analikumseka. Ankati:
A. Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye mwini. Si Mfumu ya Aisraele nanga? Atsiketu tsopano pamtandapo ndipo tidzamkhulupirira. Suja amakhulupirira Mulungu ndi kumati, 'Ndine Mwana wa Mulungu.' Mulungu ampulumutsetu tsopano ngati amfunadi.
W. Zigawenga zija, zimene adazipachika pamodzi ndi Yesu, nazonso zinali kumtukwana chimodzimodzi. Kuyambira pa 12 koloko masana mpaka pa 3 koloko, dzuwa litapendeka, padachita mdima pa dziko lonse. Ndipo monga pa 3 kolokopo Yesu adafuula kwakukulu nati:
Y. Eli, Eli, lama sabakatani?
W. Ndiye kuti:
Y. Mulungu wanga, bwanji mwandisiya ndekha?
W. Anthu ena amene analikuimirira pamenepo adamva mauwo nati:
A. Munthuyu alikuitana mneneri Elia.
W. Pompo wina adathamanga, nakatenga chinkhupule. Adachiviika m’vinyo wosasa, nkuchitsomeka pa bango kuti ampatsire, amwe. Koma ena adati:
A. Taima, tiwone ngati Elia ati abweredi kudzamplumutsa.
W. Koma Yesu adafuulanso kwakukulu, natsirizika.
Onse agwade ndikukhala chete kwa kanthawi.
[Kanyimbo]
W. Pompo chinsalu chotchinga cha m’Nyumba ya Mulungu chidang’ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo mathanthwe adang’ambika. Manda adatsekuka ndipo anthu a Mulungu ambiri amene adamwalira kale, adauka kwa akufa. Adatuluka m’manda, ndipo Yesu atauka kwa akufa, iwo adalowa mu Yerusalemu, Mzinda Wopatulika, ndipo anthu ambiri adawaona. Mkulu wa asirikali ndi iwo amene anali naye polonda Yesu, ataona chivomezi chija ndi zina zonse zimene zidachitika, adachita mantha kwambiri nati:
M. Zoona, munthu uyu analidi Mwana wa Mulungu.
W. Patali poteropo panali azimai angapo alikuyang’anitsitsa. Ndiwo amene adatsata Yesu kuchokera ku Galilea ndi kumamtumikira. Pakati pao panali Maria wa ku Magadala, Maria mai wa Yakobe ndi Yosefe, ndiponso mai wa ana a Zebedeo. Kutada, kudafika munthu wina wolemera, wochokera ku Arimatea, dzina lake Yosefe. Nayenso anali wophunzira wa Yesu. Iyeyu adakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Pilato adalamula kuti ampatse mtembowo. Tsono Yosefe adautenga, naukulunga m’nsalu yoyera ya balafuta. Adakaika m’manda ake atsopano ochita chosema m’nthanthwe.
M. Iwo adapitadi, nakatseka manda kolimba posindikiza chizindikiro pa chimwala chotsekeracho. Kenaka adasiya asilikali akulonda pomwepo.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, poona umo Yesu adasaukira chifukwa cha ife, tikuzindikira kuti chikondi cha Mulungu ndi chozama kwambiri. Tiyeni tipemphere anthu onse:
1. Akulu a Eklezia akhale a mtima wodzichepetsa nthawi zonse, kuti athe kutsogolera akhristu. Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akulu olamulira maiko nawonso akhale a mtima wodzichepetsa: kuti athe kulamulira anthu ao moyenera.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akhristu ndi akatekumeni a Parishi yathu ino, agwirizane pakukhala odzichepetsa ndipo athe kutembenuza akunja ndi chitsanzo chawo chabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Makolo a ana ayesetse kulera bwino ana ao, pakuwapatsa zitsanzo zokoma ndi maphunziro oyenera, kukokera anawo ku ntchito za Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.
5. Ifeyo mutipatse chikondi Atate, kuti pamene anzathu atichitira zoipa tisawabwezere konse: choncho anzathu adzatha kutembenuka mtima.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mwa chifundo chanu tcherani makutu ndi kutimvera ife amene tikukupemphani. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:
Post a Comment