Thursday, April 6, 2023

LACHINAYI LOYERA – CHAKA A [MISA YAMADZULO YA PHWANDO LA AMBUYE]


LACHINAYI LOYERA – CHAKA A

[MISA YAMADZULO YA PHWANDO LA AMBUYE]

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA EKSODO; EKSODO 12: 01 – 08, 11 – 14. (Malamulo okhudzana ndi phwando la Pasaka).

 

Chauta adalankhula kwa Mose ndi Aroni m’dziko lija la Ejipito kuti, “Mwezi uno udzakhala mwezi wanu woyambira chaka. Mulengeze kwa khamu lonse la Aisraele kuti pa tsiku lakhumi la mwezi uno, munthu aliyense adzasankhulire banja lake mwana wankhosa mmodzi. Banja lililonse lidzatenge mwana wankhosa mmodzi. Banja likachepa, kuti silingathe kudya nyama yonseyo, mabanja awiri oyandikana aphatikizane pamodzi, monga momwe aliri anthu, tsono onsewo adyere limodzi. Mulinganiziretu chiwerengero cha anthu odya nyamayo, modziwa m’mene munthu mmodzi angadyere. Mwana wankhosa wake adzakhale wopanda chilema, wamphongo, wa chaka chimodzi. Mungathe kusankhulanso mwana wambuzi. Mumsunge mpaka tsiku la 14 la mwezi, pamene khamu lonse la Aisraele lidzaphe nyama zaozo madzulo ndithu. Tsono adzatengeko magazi a nyamayo ndi kuwaza pa mphuthu ziwiri za chitsekozo, ndi pamwamba pa chitseko cha nyumba m’mene akadyeremo nyamayo. Nyamayo adzaiwotche usiku womwewo, ndipo adzaidye ndi buledi wosafufumitsa ndiponso ndi ndiwo zowawa zamasamba. Kudya kwake, muzikadya motere: Mudzavale zaulendo, nsapato zanu zili kuphazi, ndodo zili kumanja. Mudzadye mofulumira. Limeneli ndilo tsiku la Pasaka ya Chauta. Usiku umenewo, Ine ndidzapita m’dziko la Ejipito ndipo m’dziko lonselo ndidzapha ana onse oyamba kubadwa, a anthu ndi a nyama omwe. Ndidzalanga milungu yonse ya Ejipito. Ine ndine Chauta. Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito. “Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 116: 12 – 13, 15 – 18.

 

Chikho chimene timachidalitsa, timaphatikizana ndi Magazi a Khristu tikamweramo.

 

Ndidzambwezera chiyani Chauta,

Pa zabwino zonse zimene adandichitira?

Ndidzakweza chikho cha chipulumutso,

Ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.

 

Chikho chimene timachidalitsa, timaphatikizana ndi Magazi a Khristu tikamweramo.

 

Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta, ndi yamtengowapatali pamaso pake,

Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni,

Mwana wa mdzakazi wanu,

Inu mwamasula maunyolo anga.

 

Chikho chimene timachidalitsa, timaphatikizana ndi Magazi a Khristu tikamweramo.

 

Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera,

Ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta,

Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta,

Pamaso pa anthu ake onse.

 

Chikho chimene timachidalitsa, timaphatikizana ndi Magazi a Khristu tikamweramo.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO; 01 AKORINTO 11: 23 – 26. (Nthawi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye).

 

Abale, inetu zimene ndidalandira kwa Ambuye ndi zimene nanenso ndidazipereka kwa inu, zakuti usiku umene adaperekedwa uja, Ambuye Yesu adaatenga mkate. Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.” Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthawi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.” Pakuti nthawi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye, mpaka adzabwerenso.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 13: 34.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana; monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 13: 01 – 15 (Iye ankawakonda amene anali ake pansi pano, ndipo adaawakonda kotheratu).

 

Chikondwerero cha Pasaka chili pafupi, Yesu adaadziwiratu kuti nthawi yake yafika yakuti achoke pansi pano kupita kwa Atate. Iye ankawakonda amene anali ake pansi pano, ndipo adaawakonda kotheratu. Tsono Yesu ndi ophunzira ake ankadya chakudya chamadzulo. Satana nkuti ataika kale mumtima mwa Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, maganizo akuti akapereke Yesu kwa adani ake. Yesu ankadziwa kuti Atate adapereka zinthu zonse m’manja mwake. Ankadziwanso kuti adachokera kwa Mulungu, ndipo kuti akubwerera kwa Mulungu. Choncho pamene anali kudya, Yesu adaimirira, adavula mwinjiro wake, natenga nsalu yopukutira nkuimanga m’chiwuno. Atatero adathira madzi m’beseni, nayamba kutsuka mapazi a ophunzira ake, nkumawapukuta ndi nsalu yopukutira ija imene adaaimanga m’chiwuno. Pamene adafika pa Simoni Petro, iyeyo adati, “Ambuye, Inuyo nkundisambitsa ine mapazi?” Yesu adamuyankha kuti, “zimene ndikuchitazi, sukuzidziwa tsopano, koma udzazidziwa m’tsogolo muno.” Petro adati, “simudzandisambitsa konse mapazi.” Yesu adamuyankha kuti, “ngati sindikusambitsa, ndiye kuti chako palibe.” Simoni Petro adati, “Ambuye, ngati ndi choncho, mutsuke osati mapazi anga okha, komanso manja anga ndi mutu womwe.” Yesu adamuuza kuti, “Munthu amene wasamba, wayera yense. Palibe chifukwa choti asambenso, koma kungosamba mapazi okha basi. Tsono inu mwayera, koma osati nonsenu ai.” Yesu ankamudziwa munthu wodzampereka kwa adani ake, nchifukwa chake adaati, “Si nonsenu muli oyera.” Yesu atatsuka mapazi a ophunzira ake, adavalanso mwinjiro wake nakakhalanso podyera paja. Kenaka adawafunsa kuti, “kodi mwazimvetsa zimene ndakuchitiranizi? Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene. Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi. Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

­

Monga Yesu Khristu adakonda anthu kotheratu, napereka moyo wake chifukwa cha iwo, ifenso tikhale nawo mtima womwewo popempherera anthu onse:

 

1.     Tipempherere Aepiskopi ndi Ansembe onse kuti asenze udindo wao mokhulupirika, ndipo aonetse akhristu ao mtima wachifundo pakuwatumikira modzichepetsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

2.     Tipempherere Akhristu onse kuti apeze m’sakramenti la Ukaristia mphamvu zolimbikira pa moyo wao wa uzimu ndiponso chifundo chakukondana mwaubale.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Tipempherere Parishi yathu ino ndi maparishi ena onse, kuti apezeke anyamata ambiri ovomera kuitana kwa Ambuye ndi odzipereka ku ntchito ya unsembe.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tonse tili muno tipemphererane kuti tikhale a mtima umodzi ndi a changu pa ntchito zotumikira anzathu, mosaopa kupereka moyo wathu womwe chifukwa cha iwo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tili kuyamika chifundo chanu chotipulumutsa. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

 

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...