Saturday, December 31, 2022

CHAKA CHA MARIA WOYERA, AMAI A MULUNGU – A

“Adabadwa mwa Virgo Maria.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA NUMERI; NUMERI 06: 22 – 27. (Akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzawadalitsadi).

 

Chauta adauza Mose kuti, “uza Aroni ndi ana ake kuti azidalitsa Aisraele motere: Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang’aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima.

Chauta akuyang’aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.” Ndipo Chauta adati, “akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzawadalitsadi.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 67: 02 – 03, 05 – 06, 08.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

 

Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa,

Mutiwunikire ndi chikondi chanu,

Njira yanu idziwike pa dziko lonse lapansi,

Chipulumutso chanu chidziwike pakati pa mitundu yonse.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

 

Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe,

Chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo,

Ndi kuwatsogolera pa dziko lapansi.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

 

Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu,

Mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

Inde, Mulungu watidalitsa,

Anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze lye.

 

Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AGALATIYA; AGALATIYA 04: 04 – 07. (Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi).

 

Abale, nthawi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu. Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m’mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, ‘Abba! Atate!’ Motero sindiwenso kapolo ai, koma mwana. Ndipo popeza kuti ndiwe mwana wake, Mulungu adakusandutsanso mlowachuma wake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Aheberi 01: 01 – 02.

Alleluia, Alleluia – Kale lija pa nthawi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano, walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 02: 16 – 21. (Adampeza Maria ndi Yosefe ndi Mwanayo …Pamene tsiku la chisanu ndi chitatu linakwana anampatsa mwanayo dzina loti Yesu).

 

Abusa adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m’chodyera cha zoweta chija. Pamene adamuwona, abusawo adawafotokozera zimene mngelo uja adaawauza za mwanayo. Onse amene ankamva, ankadabwa ndi zimene abusawo ankawasimbira. Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake. Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaawauzira. Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, December 24, 2022

 


KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – CHAKA A

[MISA YA MASANA]

“Adadzatisandutsa ana a Mulungu.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 52: 07 – 10. (Dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu).

 

Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m’mapiri, kubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu. Mverani, alonda anu akukweza mau, akuimba pamodzi mokondwa, popeza kuti akuwona chamaso Chauta akubweranso ku Ziyoni. Fuulani mokondwera inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Chauta wawatonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu. Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98: 01 – 06.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,

Popeza kuti wachita zodabwitsa,

Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo,

Waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse kuti Iye ndi wolungama,

Wakumbukira chikondi chake chosasinthika,

Ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi,

Aona chipulumutso cha Mulungu wathu,

Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi.

Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

 

Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe,

Lizani pangwe ndi nyimbo zokoma,

Imbirani Chauta Mfumu,

Imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.

 

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA KWA AHEBERI; AHEBERI 01: 01 – 06. (Mulungu analankhula kwa ife kuchokera kwa Mwana wake).

 

Abale, kale lija pa nthawi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati cholowa chake. lye ndiye kuwala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuwachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero. Mwana wa Mulunguyo ngwoposa angelo, monga momwe dzina limene Mulungu adampatsa limaposera dzina la angelo. Nchifukwa chake kale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala.” Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti, “Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga.” Koma pamene ankatuma Mwana wake wachisamba pansi pano, Mulungu adati, “Angelo onse a Mulungu azimpembedza.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Yohane 01: 01 – 18.

Alleluia, AlleluiaTsiku loyera lija latifikira ife. Bwerani inu mafuko onse, kuti timulambire Ambuye, popeza lero kuwala kwationekera pa dziko lonse lapansi. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE WOYERA; YOHANE 01: 01 – 05, 09 – 14. (Mau aja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu).

 

Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu. Anali kwa Mulungu chikhalire. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye. Mwa lyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuwala kounikira anthu. Kuwalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuwalako. Kuwala kwenikweni, kounikira anthu onse, kunkadza pansi pano. Wotchedwa Mauyo anali m’dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa lye, komabe anthu apansipano sadamzindikire. Adaabwera kwao ndithu, koma anthu ake omwe sadamlandire. Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo amenewa lye adawapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m’kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu. Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.


#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/ 


Friday, December 23, 2022

 


KUBADWA KWA AMBUYE YESU KHRISTU – CHAKA A
                                    [MISA YA USIKU]
              “Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 09: 01 – 07. (Mwana watibadwira)

 

Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu adaanyozetsa dziko la Zebuloni ndi la Nafutali, koma kutsogolo kuno adzalisandutsa laulemu dera lonseli, kuyambira ku nyanja yaikulu kuzambwe mpaka kukafika ku dziko la patsidya pa mtsinje wa Yordani, ndiye kuti dziko la Galilea, dziko la anthu a mitundu ina. Aneneratu za mfumu yam’tsogolo. Anthu amene ankayenda mumdima aona kuwala kwakukulu. Amene ankakhala m’dziko la mdima wandiweyani, kuwala kwawaonekera. Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m’mene anthu amakondwera nthawi ya masika, monganso m’mene anthu amakondwera pogawana zofunkha. Pakuti inu mwathyola goli limene linkawalemera, ndodo zimene ankamenyera mapewa ao, ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza, monga mudaachitira pogonjetsa Amidiyani. Ndithu, nsapato iliyonse ya munthu wankhondo ndi chovala chilichonse chothonyezekera magazi, zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni. Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m’manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.” Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide, ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 96: 01 – 03, 11 – 13.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano!

Imbirani Chauta, anthu a m’dziko lonse lapansi!

Imbirani Chauta, tamandani dzina lake!

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku,

Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse,

Simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m’maiko onse.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere,

Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam’menemo,

Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam’menemo,

Mitengo yam’nkhalango idzaimba mokondwa pamaso pa Chauta,

Pamene adzabwera kudzalamulira dziko lapansi.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

 

Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo,

Adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.

 

Usiku womwe uno wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA TITO; TITO 02: 11 – 14. (Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse).

 

Abale, Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse. Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu. Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake. Paja lye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Luka 02:10 – 11.

Alleluia, Alleluia Ndadzakuuzani za uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 02: 01 – 14. (Lero Mpulumutsi watibadwira).

 

Masiku amenewo, Augusto, Mfumu ya ku Roma, adalamula kuti pakhale kalembera wa anthu a m’maiko ake onse. Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo adachitika pamene Kwirinio anali bwanamkubwa wa dziko la Siriya. Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao. Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m’banja ndi fuko la Davideyo. Adapita kukalembedwa pamodzi ndi Maria, mkazi wake, amene anali ndi pathupi. Pamene anali kumeneko, nthawi yake yoti Maria achire idakwana, ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m’nsalu namgoneka m’chodyera cha zoweta, chifukwa adaasowa malo m’nyumba ya alendo. Ku dera lomwelo kunali abusa amene ankalonda zoweta zao ku dambo usiku. Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye adadzaimirira pakati pao, ndipo ulemerero wa Ambuye udawala ponse pozungulira, mwakuti abusawo adaachita mantha kwambiri. Koma mngeloyo adawauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Usiku womwe uno m’mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye. Chitsimikizo chake ndi ichi: mukapeza mwana wakhanda, wokutidwa ndi nsalu, atagona m’chodyera cha zoweta.” Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, December 17, 2022

 


 LAMULUNGU LACHINAYI MU NYENGO YA ADVENT – CHAKA A

(Imanuele: “Mulungu ali nafe.”)

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 07: 10 – 14. (Onani, namwali uja watenga pathupi).

 

Chauta adalankhulanso ndi Ahazi kudzera mwa mneneri Yesaya kuti, “upemphe chizindikiro kwa Chauta Mulungu wako. Chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.” Koma Ahazi adati, “sindidzapempha, ndipo sindidzayesa Chauta ai.” Apo Yesaya adati, “mumve tsono, inu chidzukulu cha Davide! Kodi sikukukukwanirani kutopetsa anthu, apa mufuna kutopetsa ndi Mulungu wanga yemwe? Nchifukwa chake Ambuye omwe adzakupatsani inu chizindikiro. Onani, namwali uja watenga pathupi ndipo adzabala mwana wamwamuna, mwanayo adzamutcha dzina lake Imanuele.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 24: 01 – 06.

 

Mfumu yaulemerero ilowe. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.

 

Dziko lapansi ndi zonse zam’menemo ndi za Chauta,

Dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake,

Pakuti iye ndi amene adaika dziko lapansi,

Pa nyanja yaikulu, adalikhazika pa mitsinje yozama.

 

Mfumu yaulemerero ilowe. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.

 

Ndani angayenere kukwera phiri la Chauta?

Ndani angaime m’malo ake oyera?

Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake, ndipo amaganiza zabwino mumtima mwake,

Ndi amene salingalira zonama, ndipo salumbira monyenga.

 

Mfumu yaulemerero ilowe. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.

 

Adzalandira madalitso kwa Chauta,

Ndipo Mulungu Mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.

Anthu otere ndiwo amene amafunitsitsa Chauta,

ndiwo amene amabwera kudzapembedza, Mulungu wa Yakobe.

 

Mfumu yaulemerero ilowe. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA YOLEMBERA AROMA; AROMA 01: 01 – 07. (Yesu Khristu, chidzukulu chochokera kwa Davide, Mwana wa Mulungu).

 

Abale, ndine, Paulo, mtumiki wa Yesu Khristu. Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, nandipatula kuti ndilalike uthenga wake wabwino. Uthengawu Iye adaulonjeza kale kudzera mwa aneneri ake ndipo udalembedwa m’Malembo Oyera. Umasimba za mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang’anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, koma poyang’anira kuyera kwake kwaumulungu, kuuka kwake kwa akufa kukutsimikiza kuti Yesuyo ndi mwana wa Mulungu. Mwa Khristuyo ife tidalandira mwai wokhala atumwi, kuti tithandize anthu a mitundu yonse kumukhulupirira ndi kumumvera, kuti Choncho dzina lake lilemekezedwe. Ena mwa anthuwo, ndinu amene Mulungu adakuitanani kuti mukhale ake a Yesu Khristu. Ndikulembera inu nonse amene muli ku Roma, amene Mulungu amakukondani, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake. Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima ndikukupatsani mtendere.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Mateyo 01: 23.

Alleluia, Alleluia – Namwali wina wosadziwa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele, ndiye kuti “Mulungu ali nafe”. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYU WOYERA; MATEYO 01: 18 – 24. (Yesu Khristu adabadwa mwa Maria amene adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe Mwana wa Davide).

 

Kubadwa kwa Yesu Khristu kudaatere: amai ake Maria adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe; koma asanalowane, Maria adaapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mphamvu za Mzimu Woyera. Mwamuna wake Yosefe anali munthu wokonda chilungamo, komabe sadafune kumchititsa manyazi poyera. Nchifukwa chake adaganiza za kungothetsa mbeta ija osachitapo mlandu. Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuonekera m’maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.” Zonsezi zidaatero kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Namwali wina wosadziwa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.” Tsono Yosefe atadzuka, adachita monga momwe mngelo wa Ambuye uja adaamuuzira. Adamtenga Maria, mkazi wake uja, koma sadamdziwe mpaka adabala mwana wamwamuna. Pambuyo pake Yosefe adatcha mwanayo dzina loti Yesu.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Saturday, December 10, 2022

 


             LAMULUNGU LACHITATU MU NYENGO YA ADVENT – CHAKA A

[Gaudete Sunday]

(Bwerani Ambuye, mudzatipulumutse.)

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 35: 01 – 06a, 10. (Mulungu Mwini akubwera kudzakupulumutsani.)

 

Chipululu ndi dziko lopanda madzi ndidzasangalala, dziko luoma lidzakondwa ndi kuchita maluwa. Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka ongodzimerera okha. Lidzasangalala ndi kufuula ndi chimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero wonga wa mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake adzakhala okongola ngati a ku Karimele ndi Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Chauta ndi ukulu wa Mulungu wathu. Mulimbitse manja ofooka, ndi kuwapatsa mphamvu maondo olobodoka. Muuze onse a mtima wamantha kuti, “limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.” Pamenepo maso a anthu akhungu adzapenyuka, ndipo makutu a agonthi adzatsekuka. Opunduka adzalumpha ngati mphoyo, ndipo osalankhula adzaimba mokondwa. Akasupe adzatumphuka m’chipululu, ndipo mitsinje idzayenda m’dziko louma. Amene Chauta adawaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi Chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 146: 06 – 10.

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

 

Chauta amasunga malonjezo ake nthawi zonse,

Amachitira anthu opsinjidwa zolungama,

Amawapatsa chakudya anthu anjala,

Chauta amamasula am’ndende.

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

 

Chauta amatsekula maso a anthu osapenya,

Chauta amakweza anthu otsitsidwa,

Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,

Chauta amateteza alendo, Amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye.

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

 

Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,

Koma njira za anthu oipa amazipotoza,

Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya,

Mulungu wako, iwe Ziyoni, dzalamulira ku mibadwo yonse,

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA YAKOBE; YAKOBE 05: 07 – 10. (Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera.)

 

Abale, khazikani mtima pansi mpaka Ambuye adzabwere. Onani m’mene amachitira mlimi. Amadikira kuti zipatso zokoma ziwoneke m’munda mwake. Amangoyembekeza mokhazika mtima kuti zilandire mvula yachizimalupsa ndi yachikokolansanu. Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera. Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo. Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m’dzina la Ambuye. Iwo adamva zowawa, komabe adapirira.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YESAYA 61: 01 (LUKA 04:18)

 

Alleluia, Alleluia – Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa Ine. Wandituma kuti ndikalalike uthenga Wabwino kwa anthu osauka. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 11: 02 – 11. (Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?)

 

Pamene Yohane Mbatizi anali m’ndende, adaamva zimene Khristu uja ankachita. Choncho adatuma ophunzira ake ena kwa Iye kukafunsa kuti, “kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Yesu adati, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mukuzimva ndi kuziwona. Akhungu akupenya ndipo Opunduka miyendo akuyenda; akhathe akuchira ndipo agonthi akumva; akufa akuukitsidwa ndipo amphawi akumva uthenga wabwino. Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha ine.” Pamene amithenga a Yohane aja ankachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “kodi m’mene mudaapita ku Chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Nanga mudaati mukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Iyai, anthu ovala zofewa amakhala m’nyumba za mafumu. Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri amene. Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, ‘nayitu Nthumwi yanga, ndikuituma m’tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’ Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane Mbatizi. Komabe ngakhale amene ali wamn’gonong’ono mu ufumu wakumwamba amampambana.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...