Saturday, December 10, 2022

 


             LAMULUNGU LACHITATU MU NYENGO YA ADVENT – CHAKA A

[Gaudete Sunday]

(Bwerani Ambuye, mudzatipulumutse.)

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 35: 01 – 06a, 10. (Mulungu Mwini akubwera kudzakupulumutsani.)

 

Chipululu ndi dziko lopanda madzi ndidzasangalala, dziko luoma lidzakondwa ndi kuchita maluwa. Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka ongodzimerera okha. Lidzasangalala ndi kufuula ndi chimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero wonga wa mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake adzakhala okongola ngati a ku Karimele ndi Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Chauta ndi ukulu wa Mulungu wathu. Mulimbitse manja ofooka, ndi kuwapatsa mphamvu maondo olobodoka. Muuze onse a mtima wamantha kuti, “limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.” Pamenepo maso a anthu akhungu adzapenyuka, ndipo makutu a agonthi adzatsekuka. Opunduka adzalumpha ngati mphoyo, ndipo osalankhula adzaimba mokondwa. Akasupe adzatumphuka m’chipululu, ndipo mitsinje idzayenda m’dziko louma. Amene Chauta adawaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi Chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 146: 06 – 10.

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

 

Chauta amasunga malonjezo ake nthawi zonse,

Amachitira anthu opsinjidwa zolungama,

Amawapatsa chakudya anthu anjala,

Chauta amamasula am’ndende.

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

 

Chauta amatsekula maso a anthu osapenya,

Chauta amakweza anthu otsitsidwa,

Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,

Chauta amateteza alendo, Amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye.

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

 

Chauta amakonda anthu ochita chilungamo,

Koma njira za anthu oipa amazipotoza,

Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya,

Mulungu wako, iwe Ziyoni, dzalamulira ku mibadwo yonse,

 

Bwerani Ambuye kudzatipulumutsa.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA YAKOBE; YAKOBE 05: 07 – 10. (Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera.)

 

Abale, khazikani mtima pansi mpaka Ambuye adzabwere. Onani m’mene amachitira mlimi. Amadikira kuti zipatso zokoma ziwoneke m’munda mwake. Amangoyembekeza mokhazika mtima kuti zilandire mvula yachizimalupsa ndi yachikokolansanu. Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera. Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo. Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m’dzina la Ambuye. Iwo adamva zowawa, komabe adapirira.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YESAYA 61: 01 (LUKA 04:18)

 

Alleluia, Alleluia – Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa Ine. Wandituma kuti ndikalalike uthenga Wabwino kwa anthu osauka. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 11: 02 – 11. (Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?)

 

Pamene Yohane Mbatizi anali m’ndende, adaamva zimene Khristu uja ankachita. Choncho adatuma ophunzira ake ena kwa Iye kukafunsa kuti, “kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Yesu adati, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mukuzimva ndi kuziwona. Akhungu akupenya ndipo Opunduka miyendo akuyenda; akhathe akuchira ndipo agonthi akumva; akufa akuukitsidwa ndipo amphawi akumva uthenga wabwino. Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha ine.” Pamene amithenga a Yohane aja ankachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “kodi m’mene mudaapita ku Chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Nanga mudaati mukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Iyai, anthu ovala zofewa amakhala m’nyumba za mafumu. Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri amene. Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, ‘nayitu Nthumwi yanga, ndikuituma m’tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’ Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane Mbatizi. Komabe ngakhale amene ali wamn’gonong’ono mu ufumu wakumwamba amampambana.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...