LAMULUNGU LACHIWIRI MU NYENGO YA ADVENT – CHAKA A
(Konzani njira yodzeramo Ambuye.)
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 11: 01 – 10. (Amphawi adzawaweruza mwachilungamo.)
Nthambi idzaphuka patsinde pa Yese, ndipo mphukira idzatuluka ku mizu yake. Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye, Mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa, mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu, mzimu wopatsa kudziwa zinthu ndi kuwopa Chauta. Ndipo kuopa Chauta ndiye chidzakhale chinthu chomkondweretsa. Sadzaweruza potsata zooneka pamaso, kapena kugamula mlandu potsata zakumva. Koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo, ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi adzawagamulira mlandu wawo mosakondera. Mau ochokera m’kamwa mwake adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa, atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa. Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake, ndipo kukhulupirika, ngati chomangira m’chiwuno mwake. Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang’ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng’ono nkumaziweta. Ng’ombe yaikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi, ndipo ana awo adzagona pamodzi. Mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Mwana woyamwa adzasewera pa dzenje la mamba, ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake ku funkha la mphiri, osalumidwa. Sipazakhala chilichonse chopweteka kapena choononga pa phiri lopatulika la Mulungu. Ndipo anthu a pa dziko lonse lapansi adzakhala odzadza ndi nzeru ya kudziwa Chauta, monga nyanja imadzazira ndi madzi. Otengedwa ku ukapolo adzabwerako. Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera ku banja la Davide idzakhala chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Onse adzasonkhana kwa iye, ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 72: 01 – 02, 07 – 08, 12 – 13, 17.
Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!
Inu Mulungu, patsaniko mfumu nzeru zoweruzira,
Patsaniko mwana wa mfumu mtima wokonda chilungamo,
Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama,
Ndiponso anthu anu osauka mosakondera.
Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!
Pa masiku ake chilungamo chidzakula,
Mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!
Idzakhala ikulamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina,
Kuchokeranso ku mtsinje mpaka ku mathero a dziko.
Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!
Ndithu iyo idzalanditsa anthu osowa amene amaiitana,
Idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda wowathandiza,
Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osowa,
Ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphawi.
Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!
Dzina lake lisaiwalike, mbiri yake ikhalepobe,
Monga momwe limakhalira dzuwa,
Anthu alandire madalitso chifukwa cha iyo,
A mitundu yonse aitche yodala.
Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka Mwezi utaleka kuwala!
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU AM’KALATA YA PAULO WOYERA YOLEMBERA AROMA; AROMA 15: 04 – 09. (Khristu ndi Mpulumutsi wa anthu onse.)
Abale, zonse zolembedwa m’Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowa amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo. Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira nawalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono muzilandirana monga momwe Khristu adakulandirirani inu, kuti Mulungu alemekezedwe. Chifukwa kunena zoona, Khristu adasanduka mtumiki wa Ayuda, kutsimikiza kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Adatsimikiza kukhulupirikako pakuchita zimene Mulungu adawalonjeza makolo ao akale aja, ndiponso pakutsata anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Nchifukwa chake ndidzakuyamikani pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Luka 03: 04, 06.
Alleluia, Alleluia – Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo. Motero anthu onse adzaona chipulumutso chochokera kwa Mulungu – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 03: 01 – 12. (Tembenukani mtima, chifukwa ufumu wa Mulungu wayandikira.)
Pa masiku amenewo kudabwera Yohane M’batizi nayamba kulalika m’chipululu cha ku Yudeya. Ankati, “tembenukani mtima chifukwa Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.” Paja Yesaya ankanena za iyeyu pamene adati, “Liwu la munthu wofuula m’chipululu; akunena kuti, ‘konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.” Yohane yo ankavala zovala za ubweya wangamira, ndipo ankamangira lamba wachikopa m’chiwuno. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wam’thengo. Anthu ochokera ku Yerusalemu ndi ku dera lonse la Yudeya, ndi ku madera onse a pafupi ndi mtsinje wa Yordani ankadza kwa iye. Ndiye ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumawabatiza mu Mtsinje wa Yordaniwo. Ankaona Ayuda ambiri a m’gulu la Afarisi ndi Asaduki akubwera kuti iye awabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthawe chilango cha Mulungu chikudzachi? Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima. Ndipo m’mitima mwanu musayerekeze zomanena kuti, ‘Atate athu ndi Abrahamu.’ Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu angathe kusandutsa ngakhale miyala ili apayi kuti ikhale ana a Abrahamu. Pali pano nkhwangwa ili kale patsinde pa mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, adzaudula nkuuponya pa moto. Ine ndimakubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenuka mtima. Koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m’moto. Chopetera chake chili m’manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m’nkhokwe, koma mankhusu adzawatentha m’moto wosazimika.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment