LAMULUNGU LOYAMBA MU NYENGO YA ADVENT – CHAKA A
(Tikhale okonzeka poyembekeza kudza kwa Ambuye.)
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPROFETI YESAYA; YESAYA 02: 01 – 05. (Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo. Anthu a mitundu yambiri adzabwera.)
Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya, mwana wa Amozi, adaziwona m’masomphenya. Pa masiku akudzawa phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo. Anthu amitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m’njira zakezo. Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta. Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo. Inu zidzukulu za Yakobe, tiyeni tiyende m’kuwala kwa Chauta.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 122: 01 – 02, 04 – 05, 06 – 09.
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.
Ndidasangala pamene adandiwuza kuti,
“Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta,”
Mapazi athu akhala akuima m’kati mwa zipata zako,
Iwe Yerusalemu.
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.
Kumeneko kumapita mafuko onse, anthu ake a Chauta,
Monga momwe adzalamulira Israele,
Kuti ayamike dzina la Chauta,
Kumeneko adaikako mipando yaufumu yoweruzira,
Mipando yake ya banja la Davide.
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.
Pemphererani mtendere wa Yerusalemu ponena kuti,
“Anthu amene amakukonda iwe Yerusalemu,
Zinthu ziziwayendera bwino,
Mtendere ukhale m’kati mwa makoma ako,
Bata likhale m’nyumba zako zachifumu.”
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.
Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga ndidzanena kuti,
“Mtendere ukhaledi m’kati mwako.”
Chifukwa cha Nyumba ya Chauta, Mulungu wathu,
Ndidzakupemphera zabwino.
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU AM’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA; AROMA 13: 11 – 14. (Chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira.)
Abale, mukudziwa kuti yafika kale nthawi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopanso kuposa pamene tidayamba kukhulupirira. Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – SALIMO 85: 08.
Alleluia, Alleluia – Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYO WOYERA; MATEYO 24: 37 – 44. (Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziwa tsiku limene Ambuye anu adzabwere.)
Yesu anati kwa ophunzira ake: “kudza kwa Mwana wa Munthu kudzakhala monga momwe zinthu zidaayendera pa nthawi ya Nowa. Masiku amenewo, chisanafike chigumula, anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adalowa m’chombo. Sadazindikire kanthu mpaka chigumula chidafika nkuwaononga onse. Zidzateronso pamene mwana wa Munthu adzabwera. Pa nthawi imeneyo anthu awiri adzakhala ali m’munda, mmodzi adzamutenga, winayo nkumusiya. Azimai awiri adzakhala akusinja mmodzi adzamutenga, winayo nkumusiya. “Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziwa tsiku limene Ambuye anu adzabwere. Koma dziwani kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba. Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene inu simukuyembekeza.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment