CHAKA CHA YESU KHRISTU MFUMU - LAMULUNGU LOTSIRIZA MU CHAKA CHA MPINGO – C (Adatigawirako zokoma za Ufumu wake.)
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LACHIWIRI LA SAMUELE; 02 SAMUELE 05: 01 – 03. (Adomdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse)
Pambuyo pake mafuko onse a Aisraele adadzasonkhona kwa Davide ku Hebroni. Adamuuza kuti, “Ifetu ndi inuyo tili magazi amodzi. Kale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo nkubwera nawonso. Ndipo Chauta adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Israele.’” Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono mfumu Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 122: 01 – 05.
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku nyumba ya Chauta.”
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti,
“Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta,”
Mapazi athu akhala akuima m’kati mwa zipata zako,
Iwe Yerusalemu.
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku nyumba ya Chauta.”
Yerusalemu adamangidwa bwino,
Zigawo zake zonse nzogwirizana pamodzi,
Kumeneko kumapita mafuko onse,
Anthu ake a Chauta.
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku nyumba ya Chauta.”
Monga momwe adzalamulira Israele,
Kuti akayamike dzina la Chauta,
Kumeneko adaikako mipando yaufumu yoweruzira,
Mipando yake ya banja la Davide.
Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku nyumba ya Chauta.”
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AKOLOSE; AKOLOSE 01:12 – 20 (Iye anatilowetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa.)
Abale, timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuwala. Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutilowetsa mu Ufumu wa mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu. Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye mwana wake Woyamba, wolamulira zolengedwa zonse. Kudzera mwa iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezi adalenga Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse padakalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi. Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu. Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo. Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Mawu a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MARKO 11: 09, 10.
Alleluia, Alleluia – Ngwodala amene alikudza m’dzina la Ambuye. Udalitsidwe Ufumu wa atate athu Davide umene ulikudza tsopano. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 23: 35 – 43. (Ambuye, mukandikumbukire mukakafika mu Ufumu wanu.)
Anthu ena onse adaimirira pomwepo nkumaonerera. Komanso akulu a Ayuda ankamunyodola nkumanena kuti, “Adapulumutsa ena, adzipulumutse yekha ngati ndiyedi Mpulumutsi uja amene Mulungu adamsankha.” Nawonso asilikali adayamba kumseka. Adadza pafupi ndi Iye, nampatsa vinyo wosasa kuti amwe. Adati, “Ngati ndiwedi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” Pamwamba pa mtanda panali kalata yolembedwa m’Chigriki, m’Chilatini, ndi m’Chiyuda. Mau ake anali akuti, “Uyu ndi mfumu ya Ayuda.” Chigawenga chimodzi chimene chidaapachikidwa nao, chidayamba kunyoza Yesu nkumanena kuti, “Ha! Kodi iwe sindiwe Mpulumutsi Wolonjezedwa uja? Udzipulumutse wekha ndi ife tomwe.” Koma mnzake uja adamdzudzula, adati, “Kodi iwe, suwopa ndi Mulungu yemwe, chidziwirecho kuti nawenso ukulandira chilango chomwechi? Tsonotu ife zikutiyeneradi zimenezi, tikulandira zolingana ndi zimene tidachita. Koma awa sadachite cholakwa chilichonse.” Ndipo adati, “Inu, mukandikumbukire mukakafika mu Ufumu wanu.” Yesu adamuyankha kuti, “ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, kumwamba.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

No comments:
Post a Comment