Saturday, November 12, 2022

 


LAMULUNGU LA 33 PACHAKA (CYCLE C)

“Limbikani ndipo mudzapulumuka.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA MPROFETI MALAKI; MALAKI 03: 19 – 20a [04: 01 – 02.] (Dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani.)

 

Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “tsiku likubwera pamene anthu onse odzikuza ndi ochita zoipa adzapsa ngati chiputu m’ng’anjo. Tsiku limenelo adzapserereratu osatsalako muzu kapena nthambi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 98: 05 – 09.

 

Chauta akubwera kudzaweruza dziko lonse lapansi mwachilungamo.

 

Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe,

Lizani pangwe ndi nyimbo zokoma,

Imbirani Chauta Mfumu,

Imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.

 

Chauta akubwera kudzaweruza dziko lonse lapansi mwachilungamo.

 

Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse za m’menemo,

Dziko lifuule pamodzi ndi anthu onse am’menemo,

Mitsinje iwombe m’manja,

Mapiri aimbe pamodzi mwachimwemwe pamene Chauta akufika.

 

Chauta akubwera kudzaweruza dziko lonse lapansi mwachilungamo.

 

Popeza kuti akubwera,

Kudzaweruza dziko lapansi,

Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,

Adzaweruza mitundu yonse mosakondera.

 

Chauta akubwera kudzaweruza dziko lonse lapansi mwachilungamo.

--------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA ATESALONIKA; 02 ATESALONIKA 03: 07 – 12. (Munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye.)

 

Abale, inu nomwe mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsanzira. Ife sitinali aulesi pamene tinali pakati panu. Sitidalandire chakudya kwa munthu aliyense osalipira, koma tidagwira ntchito kwambiri usana ndi usiku mpaka kutopa, kuwopa kuti tingalemetse wina aliyense mwa inu. Sitidachitetu zimenezi chifukwa choti tilibe mphamvu zopemphera chithandizo kwa inu, koma tinkafuna kukhala chitsanzo choti muzichitsanzira. Paja nthawi imene tinali nanu pamodzi, tidaakulamulani kuti munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye. Tikunena zimenezi popeza kuti tikumva kuti pali ena pakati panu amene ali ndi khalidwe laulesi. Anthu amenewa sagwira ntchito konse, koma amangolowera pa za anzao. M’dzina la Ambuye Yesu Khristu tikuwalamula ndi kuwachenjeza anthu otere kuti azigwira ntchito mwabata, ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito.

 

Mau a Ambuye……...Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – Luka 21: 28.

 

Alleluia, Alleluia – Mudzaimire nkukweza mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira. – Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 21: 05 – 19. (Mukadzalimbikira, ndiye mudzapate moyo wanu.)

 

Anthu ena ankalankhula za Nyumba ya Mulungu kuti adaikongoletsa ndi miyala yokoma, ndiponso ndi mitulo yopereka kwa Mulungu. Yesu adati, “kunena kuti zinthu mukuziwonazi, masiku adzabwera mwakuti sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.” Anthu aja adafunsa Yesu kuti. “Aphunzitsi, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti zonsezi zili pafupi kuchitika?” Yesu adati, “chenjerani kuti anthu angakusokonezeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m’dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine.’ Adzatinso, ‘Nthawi yayandikira.’ Amenewo musadzawatsate. Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi za zipolowe, musadzachite mantha. Zimenezi zidzayenera kuyamba zaoneka, koma sindiye kuti chimalizo chafika nthawi yomweyo.” Yesu adawauzanso kuti, “Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi zazikulu. Kudzakhala njala ndi mliri ku malo osiyanasiyana. Kudzakhalanso zoopsa ndi zizindikiro zodabwitsa mu mlengalenga. Koma zisanachitike zonsezi, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzapita nanu ku milandu ku nyumba zamapemphero, nadzakuponyani m’ndende. Adzakuperekani kwa mafumu ndi kwa akulu ena a Boma chifukwa chotsatira ine. Umenewu udzakhala mpata wanu wondichitira umboni. Tsono mudziwiretu kuti musadzachite kukonzekera mau oti mudzawayankhe pamlandupo. Ineyo ndidzakupatsani mau ndi nzeru zimene adani anuwo sadzatha konse kuzikana kapena kuzitsutsa. Makolo anu omwe, abale anu, Anansi anu, ndi abwenzi anu, amenewo adzakuperekani kwa adani anu, ndipo ena mwa inu mudzaphedwa. Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha ine. Koma silidzatayikapo tsitsi lanu ndi limodzi lomwe. Mukadzalimbikira, ndiye mudzapate moyo wanu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...