“Tikatsata Yesu ndi khama, ifenso tidzauka ku moyo wosatha.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA AMAKABEO: 02 AMAKABEO 07: 01 – 02, 09 – 14 (Mfumu ya zolengedwa zonse idzatiwukitsa kuti itipatse moyo wosatha.)
Pa nthawi yomweyo, adagwiranso abale asanu ndi awiri pamodzi ndi amai ao. Mfumu idaafuna kuwaumiriza, pakuwazunza ndi zikoti ndi zingwe zokwapulira, kuti adye nyama yankhumba, imene malamulo ankaletsa. Mmodzi mwa iwowo adalankhula m’malo mwa onse adati, “kodi mukuyembekeza kumva chiyani pakutifunsafunsa? Ifetu tili okonzeka kufa, koma zophwanya malamulo a makolo athu ayi.” Ali pafupi kufa, iye adati, “iwe oipawe, ukutilanda moyo uno, koma Mfumu ya zolengedwa zonse idzatiwukitsa kuti itipatse moyo wosatha, ife amene tikuphedwa chifukwa chomvera malamulo ake.” Pambuyo pake adadzunza wachitatu. Ozunzawo atamulamula, pompo iye adapereka lilime lake natambalitsa manja ake mopanda mantha. Adalankhula molimba mtima kuti, “Ndidalandira ziwalozi kwa Mulungu, koma tsopano kwa ine malamulo ake ndiye chinthu chachikulu koposa ziwalo zangazo.” Mfumu pamodzi ndi onse amene anali naye pomwepo adadabwa ndi kulimba mtima kwa mnyamatayo, popeza kuti mazunzowo sankawayetsa kanthu. Atafa iyeyo, adazunza wachinai ndi mazunzo a mtundu womwewo. Ali pafupi kufa iye adati, “Ngodala amene aphedwa ndi anthu, nakhulupilira Mulungu kuti adzawaukitsanso. Koma iwe Antioko, kuuka kopatsa moyo sudzakuwona ai.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 17: 01, 05 – 06, 08, 15.
Tsono ine nditadzuka, ndidzakondwa kotheratu poonana ndi Inu.
Inu Chauta, Imvani pemphero la ine munthu wolungama,
Imvani kupemba kwanga,
Tcherani khutu kuti mumve mau,
Ochokera kwa ine, munthu wosanyengane.
Tsono ine nditadzuka, ndidzakondwa kotheratu poonana ndi Inu.
Ndayenda m’njira zanu nthawi zonse,
Sindidapatuke konse,
Ndikupemphera kwa Inu Mulungu,
Chifukwa mudzandiyankha,
Tcherani khutu kuti mumve mau anga.
Tsono ine nditadzuka, ndidzakondwa kotheratu poonana ndi Inu.
Mundisunge ngati mwana wa diso,
Munditeteze pansi pa mapiko anu,
Koma ine m’kulungama kwanga ndidzaona nkhope yanu,
Tsono ine nditadzuka, ndidzakondwa kotheratu poonana ndi Inu.
Tsono ine nditadzuka, ndidzakondwa kotheratu poonana ndi Inu.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YACHIWIRI YA PAULO WOYERA KWA ATESALONIKA; 02 ATESALONIKA 02: 16 – 03: 05. (Mulungu Atate athu akupatseni mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse.)
Abale, Mulungu Atate athu adatikonda, ndipo mwakukoma mtima kwake adatipatsa kulimba mtima kosatha ndi chiyembekezo chokoma. Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse. Potsiriza, abale, mutipempherere kuti mau a Ambuye afalikire mnsanga, ndipo anthu awalandire mauwo mwaulemu, monga momwe mudachitira inu. Mupempherenso kuti Mulungu atipulumutse kwa anthu ovuta ndi oipa, pakuti si onse ali ndi chikhulupiriro. Koma Ambuye ngokhurupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa woipa uja. Ambuye amatipatsa chikhulupiriro chakuti mukuchita zonse zimene timakuuzani, ndipo kuti mudzazichitabe. Ambuye aongolere maganizo anu kuti muziyenda m’chikondi cha Mulungu, ndikutsata khama la Khristu.
Mau a Ambuye……...Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO. – Chibvumbulutso 01: 05a, 06b.
Alleluia, Alleluia – Yesu Khristu, ali woyambirira kulandira moyo waulemerero; amenenso alandire ulemerero ndi mphamvu zolamulira mpaka muyaya. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 20: 27 – 38. (Ndi Mulungu osati wa anthu akufa, koma wa anthu a moyo.)
Asaduki ena adadza kwa Yesu. Paja iwo amati akufa sadzauka. Adamufunsa Yesu Kuti, “Aphunzitsi, Mose adatilembera lamulo lakuti, ‘ngati munthu amwalira, nasiya mkazi wake, koma opanda ana, m’bale wake wa womwalirayo alowe chokolo, kuti amuberekere ana m’bale wake uja.’ Tsono padaali anthu asanu ndi awiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, koma adamwalira osamsiyira mwana. Chimodzimodzinso wachiwiri, ndipo wachitatu nayenso adalowa chokolo. Onse asanu ndi awiri adachita chimodzimodzi, koma onse adamwalira osamsiyira ana mkazi yo. Potsiriza pake mai uja nayenso adamwalira. Nanga tsono pa tsiku lodzauka akufa, mwini mkaziyo adzakhala utiwuti, popeza kuti abale asanu ndi awiri onse aja adaamkwatirapo?” Yesu adawayankha kuti, “Anthu okhala pansi pano amakwatira ndi kukwatiwa. Koma amene amawayesa oyenera kukhala ndi moyo kutsogoloko, anthu atauka kwa akufa, sadzakwatiranso kapena kukwatiwa ai. Iwo adzakhala ngati angelo, mwakuti sangafenso ai. Iwo ndi ana a Mulungu popeza kuti Iye adawaukitsa kwa akufa. Koma zakuti anthu adzauka kwa akufa, Mose yemwe adaanenapo kale. Paja mbiri ija ya chitsamba choyaka moto, iye akuwatchula Ambuye kuti, ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe.’ Ndiye kutitu Sali Mulungu wa anthu akufa ai, koma wa anthu amoyo.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment