LAMULUNGU LACHINAYI MU NYENGO YA ADVENT – CHAKA A
(Imanuele: “Mulungu ali nafe.”)
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA; YESAYA 07: 10 – 14. (Onani, namwali uja watenga pathupi).
Chauta adalankhulanso ndi Ahazi kudzera mwa mneneri Yesaya kuti, “upemphe chizindikiro kwa Chauta Mulungu wako. Chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.” Koma Ahazi adati, “sindidzapempha, ndipo sindidzayesa Chauta ai.” Apo Yesaya adati, “mumve tsono, inu chidzukulu cha Davide! Kodi sikukukukwanirani kutopetsa anthu, apa mufuna kutopetsa ndi Mulungu wanga yemwe? Nchifukwa chake Ambuye omwe adzakupatsani inu chizindikiro. Onani, namwali uja watenga pathupi ndipo adzabala mwana wamwamuna, mwanayo adzamutcha dzina lake Imanuele.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 24: 01 – 06.
Mfumu yaulemerero ilowe. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.
Dziko lapansi ndi zonse zam’menemo ndi za Chauta,
Dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake,
Pakuti iye ndi amene adaika dziko lapansi,
Pa nyanja yaikulu, adalikhazika pa mitsinje yozama.
Mfumu yaulemerero ilowe. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.
Ndani angayenere kukwera phiri la Chauta?
Ndani angaime m’malo ake oyera?
Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake, ndipo amaganiza zabwino mumtima mwake,
Ndi amene salingalira zonama, ndipo salumbira monyenga.
Mfumu yaulemerero ilowe. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.
Adzalandira madalitso kwa Chauta,
Ndipo Mulungu Mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
Anthu otere ndiwo amene amafunitsitsa Chauta,
ndiwo amene amabwera kudzapembedza, Mulungu wa Yakobe.
Mfumu yaulemerero ilowe. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA YOLEMBERA AROMA; AROMA 01: 01 – 07. (Yesu Khristu, chidzukulu chochokera kwa Davide, Mwana wa Mulungu).
Abale, ndine, Paulo, mtumiki wa Yesu Khristu. Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, nandipatula kuti ndilalike uthenga wake wabwino. Uthengawu Iye adaulonjeza kale kudzera mwa aneneri ake ndipo udalembedwa m’Malembo Oyera. Umasimba za mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang’anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, koma poyang’anira kuyera kwake kwaumulungu, kuuka kwake kwa akufa kukutsimikiza kuti Yesuyo ndi mwana wa Mulungu. Mwa Khristuyo ife tidalandira mwai wokhala atumwi, kuti tithandize anthu a mitundu yonse kumukhulupirira ndi kumumvera, kuti Choncho dzina lake lilemekezedwe. Ena mwa anthuwo, ndinu amene Mulungu adakuitanani kuti mukhale ake a Yesu Khristu. Ndikulembera inu nonse amene muli ku Roma, amene Mulungu amakukondani, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake. Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima ndikukupatsani mtendere.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Mateyo 01: 23.
Alleluia, Alleluia – Namwali wina wosadziwa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele, ndiye kuti “Mulungu ali nafe”. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MAU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MATEYU WOYERA; MATEYO 01: 18 – 24. (Yesu Khristu adabadwa mwa Maria amene adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe Mwana wa Davide).
Kubadwa kwa Yesu Khristu kudaatere: amai ake Maria adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe; koma asanalowane, Maria adaapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mphamvu za Mzimu Woyera. Mwamuna wake Yosefe anali munthu wokonda chilungamo, komabe sadafune kumchititsa manyazi poyera. Nchifukwa chake adaganiza za kungothetsa mbeta ija osachitapo mlandu. Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuonekera m’maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.” Zonsezi zidaatero kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Namwali wina wosadziwa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.” Tsono Yosefe atadzuka, adachita monga momwe mngelo wa Ambuye uja adaamuuzira. Adamtenga Maria, mkazi wake uja, koma sadamdziwe mpaka adabala mwana wamwamuna. Pambuyo pake Yosefe adatcha mwanayo dzina loti Yesu.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment