Chaka cha Kutsika kwa Mzimu Woyera kwa Apositoli (Pentecost Sunday)—C
“Adawauzira mpweya wopatsa moyo.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 2:1-11. (Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula).
Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m’nyumba imodzi. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Ndipo adaona ngati timalawi ta moto tooneka ngati malilime tikugawikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankawalankhulitsira. Tsono, m’Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi. Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankawamva akulankhula chilankhulo chake. Adadabwa, nathedwa nzeru ndipo adati, “kodi onse akulankhulawa, si Agalileya? Nanga bwanji aliyense mwa ife akuwamva akulankhula chilankhulo chakwawo? Ena mwa ife ndi Aparti ndi Amedi ndi Aelami, ena ndi okhala ku Mesapotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, Ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma, ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuwamva anthuwa akulankhula m’zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.”
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 104:1, 24, 29-31.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,
Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri,
Inu Chauta ntchito zanu zambiri,
Ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Mukazichotsera mpweya, zimafa nkubwerera ku fumbi,
Mukatumiza mpweya wanu zimalengedwa,
Ndipo mumakonzanso maonekedwe a dziko lapansi.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
Ulemerero wa Chauta ukhalebe mpaka muyaya,
Chauta akondwe nazo ntchito zakezo,
Mapemphero anga amkomere Chauta,
Popeza kuti ndimakondwa mwa Iye.
Tumizani Mzimu wanu, Ambuye, ndipo muwalitsenso dziko lonse lapansi.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 8: 8-17. (Onse amene Mzimu wa Mulungu amawatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu).
Abale, anthu oika mtima pa khalidwe limenelo, sangathe kukondweretsa Mulungu. Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufawa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m’moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene Mzimu wa Mulungu amawatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, ‘Abba! Atate!’ Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nso madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
[KAPENA]
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORITO; 1 AKORINTO 12: 3b-7, 12-13 (Tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi).
Abale, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, ‘Yesu ndi Ambuye.’
Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera m’modzimodzi. Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timawatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi m’modzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense. Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakuti yakuti yoti ayigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse. Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA PENTEKOSTE (SEQUENCE) [Nyimboyi itha kunenedwa kapena kuyimbidwa]
1. Bwerani Mzimu Woyera,
Tumizani kuwala kwanu,
Kufumira kumwambako.
2. Bwerani, Tate wa amphawi,
Bwerani, wopatsa mphatso,
Inu muuni wa mitima.
3. Ndinu Msangalatsi ndithu,
Woyendera mitima yathu,
Kuti mudzaithuzitsa.
4. Pa ntchito ndinu Mpumulo,
Mumatichotsera kutentha,
Ndi kutsangula misozi yathu.
5. Ndinu kuwala kokoma,
Dzazani mitima yathu,
Ya ife anthu okumverani.
6. Mutapanda kudzamthandiza,
Munthu sangapeze kanthu,
Zonse zidzamuipira.
7. Tsukani zoipa zathu,
Dzatsirireni zouma,
Chiritsani mabala athu.
8. Dzafewetseni zolimba,
Funditsani zozizira,
Lungamitsani zokhota.
9. Tipatseni anthu anufe,
Okhulupirira Inu,
Mphatso zisanu ndi ziwiri.
10. Kometsani makhalidwe athu,
Katifikitseni kumwamba,
Kukadala nthawi zonse,
Amen.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.
Alleluia, Alleluia!! – Bwerani Mzimu Woyera, mudzaze m’mitima ya anthu okhulupirira ndipo chikondi chanu chikhazikike mwa iwo. – Alleluia, Alleluia!!
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 14: 15-16, 23-26. (Mzimu Woyera ndiye adzakuphunzitseni zonse).
Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa ife. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvawa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m’dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
[KAPENA]
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 20: 19-23 (Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani. Landirani Mzimu Woyera).
Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adawaonetsa manja ake ndi m’thiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri powaona Ambuyewo. Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” Pambuyo pake adawauzira m’pweya nati, “Landirani Mzimu Woyera. Anthu amene mudzawakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzawakhululukira, sadzakhululukidwa ai.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Mzimu Woyera amene wakhazikika mwa ife akutitsimikizira kuti ndifedi ana a Mulungu. Tiyeni tsono, timupemphe kuti apitirize ntchito zake zamphamvu mwa ife ndi mwa anthu onse:
1. Tipempherere akulu oyang’anira Mpingo wa Mulungu, kuti asenze udindo wao molimbika ndi mwachikondi, potsata mphamvu zochokera kwa Mzimu Woyera.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Tipempherere akhristu onse, kuti Mzimu Woyera alunzitse mitima yao ndi kuwakhazikitsa m'chikondi chake, kuti akhale Mpingo umodzi ndithu.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Tipempherere anthu onse amene akadali mu mdima, osadziwa Mthenga Wabwino, kuti Mzimu Woyera awaunikire ndi kuwalondoloza m’njira ya chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tipemphererane ife tonse amene tasonkhana lero, kuti tigwiritse ntchito nzeru ndi mphamvu zofumira kwa Mzimu Woyera, pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate okoma mtima, mudakwaniritsa malonjezo anu pakutitumizira Mzimu Woyera. Mudzaze mitima ya anthu onse ndi mphatso zake zamphamvu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment