“Inetu ndili nanu masiku onse.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 1:1-11 (Yesu adatengedwa kupita Kumwamba, iwo akupenya).
A Teofilo, m’buku langa loyamba lija ndidakulemberani za zonse zimene Yesu ankachita ndi kuphunzitsa kuyambira pa chiyambi, kufikira tsiku limene adatengedwa kupita kumwamba. Mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, anali atauza atumwi amene adawasankha aja zoti iwowo adzachite. Iye ataphedwa, adadzionetsa wa moyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adawaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai. Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adawalamula kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani. Pajatu Yohane ankabatiza ndi madzi, koma pasanapite masiku ambiri, inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.” Tsono atumwi aja atasonkhana, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi ino ndiyo nthawi imene mukhazikitsenso ufumu mu Israele?” Iye adati, “si ntchito yanu kuti mudziwe nthawi kapena nyengo pamene zidzachitike zimene Atate adakhazikitsa mwa mphamvu yao. Koma munalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, Ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.’’ Atanena zimenezi, Yesu adatengedwa kupita kumwamba, iwo akupenya. Ndipo mtambo udamulandira nkumubisa, iwo osamuonanso. Mmene Atumwi aja ankayang’anitsitsabe kumwamba, iye akupita, mwadzidzi anthu awiri ovala zoyera adaimirira pa mbali pao. Anthuwo adawafunsa kuti, “Inu anthu a ku Galileya, mwatani mwangoti chilili pamenepa mukuyanga’ana kumwamba? Yesuyu amene watengedwa kuchokera kumwamba, adzabweranso monga momwe mwamuoneramu akupita kumwambako.’’
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 47:2-3,6-9.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.
Ombani m’manja inu anthu a mitundu yonse,
Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe,
Paja Chauta Wopambanazonse ndi woopsa,
Ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira,
Chauta wakwera, akumuimbira lipenga,
Imbani nyimbo zotamanda Mulungu,
Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.
Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi,
Imbani mwaluso nyimbo zotamanda,
Mulungu amalamulira mitundu ya anthu,
Mulungu amakhala pa mpando wake woyera waufumu.
Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO; AEFESO 1:17-23. (Iye wakhala kudzanja lamanja la Atate).
Abale, ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemelero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatseni nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziwe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyera yo akuunikireni m`mitima mwanu, kuti mudziwe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziwe kukula kwake kwa ulemelero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake. Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupilira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa, imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja lake lamanja m’dziko la kumwamba. Adamkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi akuluakulu onse akumwamba, ndiponso pamwamba pa maina ena onse amene anthu angawatchule nthawi ino kapenanso nthawi ili nkudza. Mulungu adagonjetsa zonse kuti zikhale pa mapazi a Khristu, ndipo adamkhazika pamwamba pa zonse kuti akhale mutu wa Mpingo. Mpingowu ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse kotheratu.
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—MATEYU 28: 19a, 20b.
Alleluia, Alleluia!! – Pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukawasandutse ophunzira anga. Ndipo ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi. – Alleluia, Alleluia!!
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 24:46-53 (Akuwadalitsa, natengedwa kupita Kumwamba).
Yesu adawauza ophunzira ake kuti, “zimene zidalembedwa ndi izi; zakuti mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zowawa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, kuti m’dzina lake mau alalikidwe kwa anthu amitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu awakhululukire machimo ao. Inuyo ndi mboni ya zimenezi. Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera kumwamba.” Atatero Yesu adawatsogolera kuchokera mumzindawo mpaka ku mudzi wa Betaniya. Kumeneko adakweza manja ake nawadalitsa. Akuwadalitsa choncho, adalekana nawo, natengedwa kupita kumwamba. Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwelera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. Tsono ankasonkhana m’Nyumba ya Mulungu nthawi ndi nthawi akutamanda Mulungu.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Yesu Khristu waima pakati pathu, atikokera tonse ku ulemerero wa Kumwamba. Tiyeni timuyamike popempha madalitso a Mulungu pa ife ndi pa anthu onse:
1. Tipempherere Mpingo woyera wa Mulungu, kuti chikondwerero chalero chidzaze mitima ya akhristu onse ndi chikhulupiriro ndi chimwemwe.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Tipempherere anthu amene amakhulupirira za pansi pano zokha, kuti azindikire zabwino zimene Mulungu adakonzera anthu ake Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Tipempherere enawo amene akulakalaka zabwino za Kumwamba, kuti asaiwale kutumikira anzao ndi kukometsa miyoyo yao, pa ulendo wao pansi pano.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tidzipempherere ife tonse a m’parishi yathu ino, kuti mayendedwe athu ndi ntchito zathu zonse zitsimikize kuti ndifedi mboni zenizeni za Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate achifundo mupitirize kuongolera mitima ya anthu onse ndi Mzimu wanu Woyera. Tizifunafuna zokoma za Kumwamba, kumene Mwana wanu alikukhala ku dzanja lanu lamanja. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment