Saturday, May 24, 2025

LAMULUNGU LA 6 LA PASAKA—C


LAMULUNGU LA 6 LA PASAKA—C

“Ambuye akhale nanu.”

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 15: 1-2, 22-29. (Maganizo athu agwirizana ndi a Mzimu Woyera kuti tisakusenzetseni katundu wina).

Anthu ena ochokera ku Yudeya adabwera ku Antiokeya, namaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuumbala potsata mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.” Koma Paulo ndi Barnabasi adatsutsana nawo kolimba. Tsono abale adapangana kuti Paulo ndi Barnabasi, ndi abale ena a ku Antiokeya, apite ku Yerusalemu kukakambirana ndi atumwi ndi akulu a mpingo za nkhaniyi. Pamenepo atumwi ndi akulu a mpingo, pamodzi ndi mpingo wonse, adavomerezana kusankha anthu ena pakati pao kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Barnabasi. Adasankha Yudasi, wotchedwa Barsabasi, ndiponso Silasi, anthu aulemu pakati pa abale, kuti akapereke kalata yonena kuti, “Abale, ife atumwi pamodzi ndi akulu a mpingo tikuti moni inu abale a ku Antiokeya, a ku Siriya, ndi a ku Silisiya, amene simuli Ayuda. Tamva kuti anthu ena ochokera m'gulu lathu akhala akukuvutani ndi kukusokonezani maganizo. Amenewo sitidawatume ndife ai. Tsono titasonkhana, tavomerezana kusankha anthu ndi kuwatuma kwa inu. Adzabwera pamodzi ndi okondedwa athu Barnabasi ndi Paulo. Amene adadzipereka kuti atumikire Ambuye athu Yesu Khristu. Nchifukwa chake tatuma Yudasi ndi Silasi kuti adzakufotokozereni pakamwa zimene talemba m'kalatayi. Maganizo athu agwirizana ndi a Mzimu Woyera kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zofunika zokhazi: musamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe kwa mafano, musamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso musachite dama. Mukalewa zimenezi, mudzachita bwino.”

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 67: 2-3, 5-6, 8.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

 

Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa,

mutiwunikire ndi chikondi chanu,

Njira yanu idziŵike pa dziko lonse lapansi,

chipulumutso chanu chidziŵike pakati pa mitundu yonse.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu,

mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe,

chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo, ndi kuŵatsogolera pa dziko lapansi.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

 

Nthaka yabereka zipatso zake,

Mulungu, Mulungu wathu watidalitsa.

Inde, Mulungu watidalitsa,

Anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze Iye.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

---------------------------------------------------------------

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO: CHIVUMBULUTSO 21: 10-14, 22-23. (Adandiwonetsa Mzinda Woyera uja, Yerusalemu,

ukutsika kuchokera. Kumwamba kwa Mulungu).

Pamenepo Mnjelo uja adandinyamula chamumzimu nakanditula pa phiri lalikulu ndi lalitali. Adandiwonetsa Mzinda woyera uja, Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu. Unkawala ndi ulemelero wa Mulungu. Kuwala kwake kunali ngati kuwala kwa mwala wa mtengowapatali, ngati mwala wa mbee, wonyezimira ngati galasi. Mzindawo unali ndi linga lalikulu ndi lalitali. Lingalo linali ndi zipata khumi ndi ziwiri, pazipatapo panali angelo khumi ndi awiri, ndipo pazitseko zake padaalembedwa maina a mafuko khumi ndi awiri a Aisraele. Pa mbali zonse zinai za mzindawo panali zipata zitatuzitatu: kuvuma zitatu, kumwera zitatu, kumpoto zitatu, kuzambwe zitatu. Linga la mzindawo lidaamangidwa pa maziko khumi ndi awiri, ndipo pamazikopo padaalembedwa maina a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa uja.

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—YOHANE 14:23-29.

Alleluia, Alleluia!! – Yesu anati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine, Atate anga adzamkonda, ndipo ife tidzabwera nkudzakhazikika mwa iye.” – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 14: 23-29. (Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m’dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse).

 

Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m’dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m’mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu. Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

Abale, popeza kuti Ambuye ali nafe ndipo akutiwongolera ndi Mzimu wao Woyera, tiyeni tipemphere mosaopa ndi mosakaika:

1.      Tipempherere Apapa ndi Aepiskopi onse, kuti alondoloze anthu ao m’njira ya umodzi ndi ya chikondi, potsata nzeru ndi mphamvu zochokera kwa Mzimu Woyera.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.      Tipempherere akhristu a mipingo yosiyanasiyana, kuti Mzimu Woyera alunzise mitima yao, ndipo awafikitse ku umodzi weniweni.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.      Tipempherere akatekumeni ndi onse amene adakali padera, kuti aleke kukhulupirira zonama ndipo apeze mtendere weniweni potsata kuwala kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

Mulungu Atate athu, mudzaze mitima yathu ndi Mzimu Woyera, kuti mayendedwe athu ndi ntchito zathu zisonyeze anthu onse kuti mumakhala nafe nthawi zonse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB


No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...