LAMULUNGU LA 5 LA PASAKA—C
“Mukondane monga momwe Ine ndidakukonderani.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 14: 21-27. (Adasonkhanitsa mpingo wonse, naufotokezera zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo).
Paulo ndi Barnabasi atalalika uthenga wabwino ku Deribe kuja, ndi kukopa okhulupilira ambiri, adabwerera ku Listara, ku Ikonio ndi ku Antiokeya m’dera la Pisidiya. Adawalimbitsa Mtima ophunzira aja, nawauzitsa kuti asataye chikhulupiliro chao. Adawauza kuti, “kuti tilowe mu ufumu wa Mulungu tiyenera kupirira masautso ambiri.” Pa mpingo uliwonse adakhazika akulu a Mpingo. Ndipo pakupemphera ndi kusala zakudya adawapereka kwa Ambuye amene anali atamkhulupilira tsopano. Pambuyo pake adabzola Pisidiya nakafika ku Pamfiliya. Ndipo atalalika mau a Mulungu ku Perga, adapita ku Ataliya. Kumeneko adalowa m’chombo kupita ku Antiokeya kuja, kumene adaaperekedwa kwa Mulungu kuti awadalitse pa ntchito imene tsopano anali ataitsiriza. Pamene adafika kumeneko, adasonkhanitsa mpingo wonse, naufotokozera zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo, ndiponso m'mene iye adaatsekulira anthu a mitundu ina njira kuti akhulupilire.
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 145: 8-9, 10-13.
Ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya, Inu Ambuye, Mfumu yanga.
Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo,
Wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika.
Chauta ndi wabwino kwa onse,
Amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.
Ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya, Inu Ambuye, Mfumu yanga.
Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta,
Anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani.
Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu,
Adzasimba za mphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu.
Ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya, Inu Ambuye, Mfumu yanga.
Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,
ulamuliro wanu ndi wa pa mibadwo yonse.
Ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya, Inu Ambuye, Mfumu yanga.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO: CHIVUMBULUTSO 21:1-5a. (Mulungu adzawapukuta misozi yonse m’maso mwao).
Ine Yohane ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi la tsopano. Paja thambo loyamba lija zinali zitazimilira, ndipo nyanja padalibenso. Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake. Ndidamva mawu amphamvu ochokera kumpando wa Chifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao. Iye adzawapukuta misozi yonse m’maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zowawa. Zakale zonse zapitiratu.” Pamenepo okhala pampando wachifumu uja adati, “Tsopano ndisandutsa zonse kuti zikhale zatsopano.”
Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO
Alleluia, Alleluia!! – Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana.” – Alleluia, Alleluia!!
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 13: 31-33a, 34-35. (Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana).
Yudasi atatuluka, Yesu adati, “Tsopano mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa iyeyu Mulungu walemekezedwa. Ngati Mulungu walemekezedwa mwa iyeyu, Mulungu mwini nayenso adzamlemekeza iye, ndipo achita zimenezi tsopano apa. Ana anga, ndili nanube kanthawi pang’ono. Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziwa kuti ndinudi ophunzira anga.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tonse ndife a Mbumba imodzi mwa Yesu Khristu. Tsono tiyeni tipemphere tonse pamodzi, pokumbukira zosowa zathu ndi za anthu onse:
1. Tipempherere akhristu onse kuti kukondana kwao kukhale chizindikiro chosonyeza chifundo cha Mulungu kwa anthu a mafuko onse.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Tipempherere ansembe ndi onse ogwira ntchito zamishoni, kuti alimbikire kufalitsa Mthenga Wabwino ku maiko akunja, osaopa kupirira masautso.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Tipempherere onse osunga mkwiyo kapena chidani kuti ayanjane ndi kukhululukirana, pokumbukira chikondi chozama chimene Yesu adatikonda nacho.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tidzipempherere ife tomwe, kuti Mulungu atikhazikitse m'chikondi chake, ndipo ntchito zathu zitsimikize kuti ndifedi abale ake a Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mulunzitse mitima yathu kuti tikhale amodzi kwenikweni, ndipo choncho anthu onse adzazindikire kuti mumawakonda, monga momwe mumakondera Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment