Saturday, June 14, 2025

Chaka cha Utatu Woyera—C

Chaka cha Utatu Woyera—C

“Tiyamike Mulungu Atate ndi Mwana ndinso Mzimu Woyera.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA MIYAMBO: MIYAMBO 8:22-31. (Lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake, Ine ndinalipo kale).

 

Nzeru ya Mulungu imafuula kuti: “Chauta adandilenga ine nzeru pa chiyambi cha ntchito zake. Mwa ntchito zake zakalekale woyambilira ndinali ine. Ndidapangidwa masiku akalekale, pachiyambiyambi, dziko lapansi lisanalengedwe. Nyanja zozama zisanalengedwe, padakalibe akasupe odzaza ndi madzi, nkuti ine nditabadwa kale. Mapiri asanaumbidwe, magomo asanakhalepo, Mulungu anali atandilenga ineyo; lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake, lisanakhaleponso dothi loyamba la dziko lapansi. Ine ndinalipo kale, pamene ankakhazikitsa zakumwamba, pamene ankalemba mzere wa malire anyanja yozama, pamene ankaika thambo m’malo mwake, pamene ankatsekula akasupe a m’nyanja yozama, pamene ankaika malire a nyanja kuti madzi ake asabzole malirewo, pamene ankaika maziko a dziko lapansi. Nthawiyo nkuti ndili pambalipa ngati mmisiri wake, ndikumkondweretsa tsiku ndi tsiku, ndikusangalala pamaso pake nthawi zonse. Ndinkasangalala m’dziko lake lokhalamo anthu, ndi kumakondwa nawo ana a anthu.”

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 8:4-5, 6-7, 8-9.

 

Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.

 

Ndikamayang’ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu,

Ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti,

“Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”

 

Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.

 

Ndiyetu mudamlenga mochepera pang’ono kwa Mulungu amene,

Mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu,

Mudampatsa ulamuliro pa ntchito za manja anu,

Mudamgonjetsera zolengedwa zonse.

 

Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.

 

Nkhosa, ng’ombe ndi nyama zakuthengo,

Mbalame zamumlengalenga, nsomba za m’nyanja,

Ndi zonse zoyenda pansi pa nyanja.

 

Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 5:1-5. (Tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu).

 

Abale, popeza kuti pakukhulupilira tapeza kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa Mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupilira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandilako ulemelero wa Mulungu. Koma sipokhapo ai, timakondweranso m’masautso athu. Pakuti tikudziwa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa la moto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—
Chibvumbulutso 1:8.

 

Alleluia, Alleluia!! – Ulemu ukhale kwa Atate ndi Mwana ndi Mzimu Woyera, Mulungu amene alipo, amene analipo, amene alikudza. – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 16:12-15. (Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzakutenga zochokera kwa Ine, nadzakudziwitsani inu).

 

Yesu adawauza ophunzira ake kuti: “ndili nawo mau ena ambiri oti ndikuuzeni, koma simungathe kuwamvetsa tsopano ayi. Koma akadzafika Mzimu wodziwitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ayi, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziwitsani zinthu zam’tsogolo. Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa Ine nadzakudziwitsani. Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzatenga zochokera kwa ine, nadzakudziwitsani inu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tidalandira Mzimu Woyera wotitsimikizira kuti ndife ana a Mulungu ndithu. Tiyeni, tipemphe Atate athu a Kumwamba, mogwirizana ndi Mwana wao Yesu, kuti adalitse anthu onse:

 

1.     Tipempherere akhristu onse kuti kukondana kwao kutsimikize kuti iwo adasandukadi ana a Mulungu ndi abale ake a Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere onse osadziwa Mthenga Wabwino kuti Mzimu Woyera awaunikire ndi kuwafikitsa ku chikhulupiriro cha chikhristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere mabanja onse kuti eniake akhale okondana ndipo apereke chitsanzo chabwino kwa ana awo.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tipemphererane kuti timange moyo pa chikondi cha Mulungu pomaonetsa anthu onse mtima wachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

 

Mulungu Atate athu, tikukuthokozani chifukwa mwatiwonetsa nkhope yanu ndiponso kukoma mtima kwanu mwa Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...