Saturday, May 31, 2025

Chaka cha Kukwera kwa Ambuye Yesu Khristu Kumwamba—C


Chaka cha Kukwera kwa Ambuye Yesu Khristu Kumwamba—C

“Inetu ndili nanu masiku onse.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 1:1-11 (Yesu adatengedwa kupita Kumwamba, iwo akupenya).

 

A Teofilo, m’buku langa loyamba lija ndidakulemberani za zonse zimene Yesu ankachita ndi kuphunzitsa kuyambira pa chiyambi, kufikira tsiku limene adatengedwa kupita kumwamba. Mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, anali atauza atumwi amene adawasankha aja zoti iwowo adzachite. Iye ataphedwa, adadzionetsa wa moyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adawaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai. Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adawalamula kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani. Pajatu Yohane ankabatiza ndi madzi, koma pasanapite masiku ambiri, inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.” Tsono atumwi aja atasonkhana, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi ino ndiyo nthawi imene mukhazikitsenso ufumu mu Israele?” Iye adati, “si ntchito yanu kuti mudziwe nthawi kapena nyengo pamene zidzachitike zimene Atate adakhazikitsa mwa mphamvu yao. Koma munalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, Ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.’’ Atanena zimenezi, Yesu adatengedwa kupita kumwamba, iwo akupenya. Ndipo mtambo udamulandira nkumubisa, iwo osamuonanso. Mmene Atumwi aja ankayang’anitsitsabe kumwamba, iye akupita, mwadzidzi anthu awiri ovala zoyera adaimirira pa mbali pao. Anthuwo adawafunsa kuti, “Inu anthu a ku Galileya, mwatani mwangoti chilili pamenepa mukuyanga’ana kumwamba? Yesuyu amene watengedwa kuchokera kumwamba, adzabweranso monga momwe mwamuoneramu akupita kumwambako.’’

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 47:2-3,6-9.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.

 

Ombani m’manja inu anthu a mitundu yonse,

Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe,

Paja Chauta Wopambanazonse ndi woopsa,

Ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira,

Chauta wakwera, akumuimbira lipenga,

Imbani nyimbo zotamanda Mulungu,

Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.

 

Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi,

Imbani mwaluso nyimbo zotamanda,

Mulungu amalamulira mitundu ya anthu,

Mulungu amakhala pa mpando wake woyera waufumu.

 

Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.

 

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO; AEFESO 1:17-23. (Iye wakhala kudzanja lamanja la Atate).

 

Abale, ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemelero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatseni nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziwe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyera yo akuunikireni m`mitima mwanu, kuti mudziwe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziwe kukula kwake kwa ulemelero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake. Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupilira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa, imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja lake lamanja m’dziko la kumwamba. Adamkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi akuluakulu onse akumwamba, ndiponso pamwamba pa maina ena onse amene anthu angawatchule nthawi ino kapenanso nthawi ili nkudza. Mulungu adagonjetsa zonse kuti zikhale pa mapazi a Khristu, ndipo adamkhazika pamwamba pa zonse kuti akhale mutu wa Mpingo. Mpingowu ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse kotheratu.

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—MATEYU 28: 19a, 20b.

 

Alleluia, Alleluia!! – Pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukawasandutse ophunzira anga. Ndipo ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi. – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA; LUKA 24:46-53 (Akuwadalitsa, natengedwa kupita Kumwamba).

 

Yesu adawauza ophunzira ake kuti, “zimene zidalembedwa ndi izi; zakuti mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zowawa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, kuti m’dzina lake mau alalikidwe kwa anthu amitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu awakhululukire machimo ao. Inuyo ndi mboni ya zimenezi. Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera kumwamba.” Atatero Yesu adawatsogolera kuchokera mumzindawo mpaka ku mudzi wa Betaniya. Kumeneko adakweza manja ake nawadalitsa. Akuwadalitsa choncho, adalekana nawo, natengedwa kupita kumwamba. Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwelera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. Tsono ankasonkhana m’Nyumba ya Mulungu nthawi ndi nthawi akutamanda Mulungu.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Yesu Khristu waima pakati pathu, atikokera tonse ku ulemerero wa Kumwamba. Tiyeni timuyamike popempha madalitso a Mulungu pa ife ndi pa anthu onse:

 

1.     Tipempherere Mpingo woyera wa Mulungu, kuti chikondwerero chalero chidzaze mitima ya akhristu onse ndi chikhulupiriro ndi chimwemwe.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere anthu amene amakhulupirira za pansi pano zokha, kuti azindikire zabwino zimene Mulungu adakonzera anthu ake Kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere enawo amene akulakalaka zabwino za Kumwamba, kuti asaiwale kutumikira anzao ndi kukometsa miyoyo yao, pa ulendo wao pansi pano.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tidzipempherere ife tonse a m’parishi yathu ino, kuti mayendedwe athu ndi ntchito zathu zonse zitsimikize kuti ndifedi mboni zenizeni za Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate achifundo mupitirize kuongolera mitima ya anthu onse ndi Mzimu wanu Woyera. Tizifunafuna zokoma za Kumwamba, kumene Mwana wanu alikukhala ku dzanja lanu lamanja. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, May 24, 2025

LAMULUNGU LA 6 LA PASAKA—C


LAMULUNGU LA 6 LA PASAKA—C

“Ambuye akhale nanu.”

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 15: 1-2, 22-29. (Maganizo athu agwirizana ndi a Mzimu Woyera kuti tisakusenzetseni katundu wina).

Anthu ena ochokera ku Yudeya adabwera ku Antiokeya, namaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuumbala potsata mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.” Koma Paulo ndi Barnabasi adatsutsana nawo kolimba. Tsono abale adapangana kuti Paulo ndi Barnabasi, ndi abale ena a ku Antiokeya, apite ku Yerusalemu kukakambirana ndi atumwi ndi akulu a mpingo za nkhaniyi. Pamenepo atumwi ndi akulu a mpingo, pamodzi ndi mpingo wonse, adavomerezana kusankha anthu ena pakati pao kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Barnabasi. Adasankha Yudasi, wotchedwa Barsabasi, ndiponso Silasi, anthu aulemu pakati pa abale, kuti akapereke kalata yonena kuti, “Abale, ife atumwi pamodzi ndi akulu a mpingo tikuti moni inu abale a ku Antiokeya, a ku Siriya, ndi a ku Silisiya, amene simuli Ayuda. Tamva kuti anthu ena ochokera m'gulu lathu akhala akukuvutani ndi kukusokonezani maganizo. Amenewo sitidawatume ndife ai. Tsono titasonkhana, tavomerezana kusankha anthu ndi kuwatuma kwa inu. Adzabwera pamodzi ndi okondedwa athu Barnabasi ndi Paulo. Amene adadzipereka kuti atumikire Ambuye athu Yesu Khristu. Nchifukwa chake tatuma Yudasi ndi Silasi kuti adzakufotokozereni pakamwa zimene talemba m'kalatayi. Maganizo athu agwirizana ndi a Mzimu Woyera kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zofunika zokhazi: musamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe kwa mafano, musamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso musachite dama. Mukalewa zimenezi, mudzachita bwino.”

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 67: 2-3, 5-6, 8.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

 

Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa,

mutiwunikire ndi chikondi chanu,

Njira yanu idziŵike pa dziko lonse lapansi,

chipulumutso chanu chidziŵike pakati pa mitundu yonse.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu,

mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe,

chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo, ndi kuŵatsogolera pa dziko lapansi.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

 

Nthaka yabereka zipatso zake,

Mulungu, Mulungu wathu watidalitsa.

Inde, Mulungu watidalitsa,

Anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze Iye.

 

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.

---------------------------------------------------------------

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO: CHIVUMBULUTSO 21: 10-14, 22-23. (Adandiwonetsa Mzinda Woyera uja, Yerusalemu,

ukutsika kuchokera. Kumwamba kwa Mulungu).

Pamenepo Mnjelo uja adandinyamula chamumzimu nakanditula pa phiri lalikulu ndi lalitali. Adandiwonetsa Mzinda woyera uja, Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu. Unkawala ndi ulemelero wa Mulungu. Kuwala kwake kunali ngati kuwala kwa mwala wa mtengowapatali, ngati mwala wa mbee, wonyezimira ngati galasi. Mzindawo unali ndi linga lalikulu ndi lalitali. Lingalo linali ndi zipata khumi ndi ziwiri, pazipatapo panali angelo khumi ndi awiri, ndipo pazitseko zake padaalembedwa maina a mafuko khumi ndi awiri a Aisraele. Pa mbali zonse zinai za mzindawo panali zipata zitatuzitatu: kuvuma zitatu, kumwera zitatu, kumpoto zitatu, kuzambwe zitatu. Linga la mzindawo lidaamangidwa pa maziko khumi ndi awiri, ndipo pamazikopo padaalembedwa maina a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa uja.

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—YOHANE 14:23-29.

Alleluia, Alleluia!! – Yesu anati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine, Atate anga adzamkonda, ndipo ife tidzabwera nkudzakhazikika mwa iye.” – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 14: 23-29. (Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m’dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse).

 

Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m’dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m’mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu. Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire.”

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

Abale, popeza kuti Ambuye ali nafe ndipo akutiwongolera ndi Mzimu wao Woyera, tiyeni tipemphere mosaopa ndi mosakaika:

1.      Tipempherere Apapa ndi Aepiskopi onse, kuti alondoloze anthu ao m’njira ya umodzi ndi ya chikondi, potsata nzeru ndi mphamvu zochokera kwa Mzimu Woyera.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.      Tipempherere akhristu a mipingo yosiyanasiyana, kuti Mzimu Woyera alunzise mitima yao, ndipo awafikitse ku umodzi weniweni.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.      Tipempherere akatekumeni ndi onse amene adakali padera, kuti aleke kukhulupirira zonama ndipo apeze mtendere weniweni potsata kuwala kwa Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

Mulungu Atate athu, mudzaze mitima yathu ndi Mzimu Woyera, kuti mayendedwe athu ndi ntchito zathu zisonyeze anthu onse kuti mumakhala nafe nthawi zonse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB


Saturday, May 17, 2025

LAMULUNGU LA 5 LA PASAKA—C

 LAMULUNGU LA 5 LA PASAKA—C

“Mukondane monga momwe Ine ndidakukonderani.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 14: 21-27. (Adasonkhanitsa mpingo wonse, naufotokezera zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo).

 

Paulo ndi Barnabasi atalalika uthenga wabwino ku Deribe kuja, ndi kukopa okhulupilira ambiri, adabwerera ku Listara, ku Ikonio ndi ku Antiokeya m’dera la Pisidiya. Adawalimbitsa Mtima ophunzira aja, nawauzitsa kuti asataye chikhulupiliro chao. Adawauza kuti, “kuti tilowe mu ufumu wa Mulungu tiyenera kupirira masautso ambiri.” Pa mpingo uliwonse adakhazika akulu a Mpingo. Ndipo pakupemphera ndi kusala zakudya adawapereka kwa Ambuye amene anali atamkhulupilira tsopano. Pambuyo pake adabzola Pisidiya nakafika ku Pamfiliya. Ndipo atalalika mau a Mulungu ku Perga, adapita ku Ataliya. Kumeneko adalowa m’chombo kupita ku Antiokeya kuja, kumene adaaperekedwa kwa Mulungu kuti awadalitse pa ntchito imene tsopano anali ataitsiriza. Pamene adafika kumeneko, adasonkhanitsa mpingo wonse, naufotokozera zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo, ndiponso m'mene iye adaatsekulira anthu a mitundu ina njira kuti akhulupilire.

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 145: 8-9, 10-13.

 

Ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya, Inu Ambuye, Mfumu yanga.

 

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo,

Wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika.

Chauta ndi wabwino kwa onse,

Amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.

 

Ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya, Inu Ambuye, Mfumu yanga.

 

Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta,

Anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani.

Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu,

Adzasimba za mphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu.

 

Ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya, Inu Ambuye, Mfumu yanga.

 

Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,

ulamuliro wanu ndi wa pa mibadwo yonse.

 

Ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya, Inu Ambuye, Mfumu yanga.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO: CHIVUMBULUTSO 21:1-5a. (Mulungu adzawapukuta misozi yonse m’maso mwao).

 

Ine Yohane ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi la tsopano. Paja thambo loyamba lija zinali zitazimilira, ndipo nyanja padalibenso. Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake. Ndidamva mawu amphamvu ochokera kumpando wa Chifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao. Iye adzawapukuta misozi yonse m’maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zowawa. Zakale zonse zapitiratu.” Pamenepo okhala pampando wachifumu uja adati, “Tsopano ndisandutsa zonse kuti zikhale zatsopano.”

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO

 

Alleluia, Alleluia!! – Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. – Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 13: 31-33a, 34-35. (Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana).

 

Yudasi atatuluka, Yesu adati, “Tsopano mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa iyeyu Mulungu walemekezedwa. Ngati Mulungu walemekezedwa mwa iyeyu, Mulungu mwini nayenso adzamlemekeza iye, ndipo achita zimenezi tsopano apa. Ana anga, ndili nanube kanthawi pang’ono. Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziwa kuti ndinudi ophunzira anga.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, tonse ndife a Mbumba imodzi mwa Yesu Khristu. Tsono tiyeni tipemphere tonse pamodzi, pokumbukira zosowa zathu ndi za anthu onse:

 

1.     Tipempherere akhristu onse kuti kukondana kwao kukhale chizindikiro chosonyeza chifundo cha Mulungu kwa anthu a mafuko onse.
Tikupemphani, mutivomereze.


2.     Tipempherere ansembe ndi onse ogwira ntchito zamishoni, kuti alimbikire kufalitsa Mthenga Wabwino ku maiko akunja, osaopa kupirira masautso.
Tikupemphani, mutivomereze.


3.     Tipempherere onse osunga mkwiyo kapena chidani kuti ayanjane ndi kukhululukirana, pokumbukira chikondi chozama chimene Yesu adatikonda nacho.
Tikupemphani, mutivomereze.


4.     Tidzipempherere ife tomwe, kuti Mulungu atikhazikitse m'chikondi chake, ndipo ntchito zathu zitsimikize kuti ndifedi abale ake a Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, mulunzitse mitima yathu kuti tikhale amodzi kwenikweni, ndipo choncho anthu onse adzazindikire kuti mumawakonda, monga momwe mumakondera Mwana wanu Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Saturday, May 10, 2025

LAMULUNGU LA 4 LA PASAKA—C [Lamulungu Lokondwelera Maitanidwe/Vocations Sunday]

LAMULUNGU LA 4 LA PASAKA—C

[Lamulungu Lokondwelera Maitanidwe/Vocations Sunday]

“Nkhosa zanga zimamva mau anga.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A BUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI: NTCHITO 13:14, 43-52. (Ife tikusiyani, tipita kwa anthu akunja).

 

Kuchokera ku Perga iwo adapitilira nakafika ku Antiokeya m’dera la Pisidiya. Patsiku la Sabata adalowa m’nyumba yamapemphero ya a Yuda, nakhala pansi. Anthu osonkhana aja atamwazikana, Ayuda ambiri, ndiponso anthu a mitundu Ina otembenuka nkumatsata zachiyuda, adatsatira Paulo ndi Barnabasi. Awiriwa adalankhula ndi anthu aja, nawapempha kuti alimbikire kutsata zimene Mulungu adawachitira mwa kukoma mtima kwake. Pa tsiku la Sabata linalo pafupi anthu onse amumzindamo adasonkhana kuti amve mau a Ambuye. Pamene Ayuda aja adaona anthu ambiriwo, adachita nsanje kwambiri. Adayamba kutsutsa zimene Paulo ankanena, ndipo adamchita chipongwe. Koma Paulo ndi Barnabasi adalankhula molimbika, adati, “kudaayenera ndithu kuti tiyambe talalika mau a Mulungu kwa inu. Tsono popeza kuti mwawakana, ndipo potero mwaonetsa nokha kuti ndinu osayenera kulandira moyo wosatha, ife tikusiyani, tipita kwa anthu a kunja. Paja Ambuye adatilamula kuti, ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja, kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ Pamene anthu amitundu Ina ija adamva zimenezi, anakondwa, nayamikira mawu a Ambuye. Ndipo onse amene Mulungu adawasankha kuti alandira moyo Wosatha, adakhulupilira. Mau a Ambuye adafikira m’dziko monse muja. Koma Ayuda aja adautsa mitima ya akazi ena apamwamba opembedza Mulungu, ndiponso ya atsogoleri achimuna amumzindamo. Tsono adayambitsa mazunzo osautsa Paulo ndi Barnabasi, nawapirikitsa m’dziko mwaomo. Koma iwo adasasa fumbi la ku mapazi kwao mowatsutsa, napita ku Ikonia. Ndipo ophunzira a ku Antiokeya adadzazidwa ndi Mzimu woyera ndipo adakhala ndi Chimwemwe chachikulu.

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 100: 1-2, 3, 5.

 

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse!

Tumikirani Chauta mosangalala.

Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa.

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

Dziwani kuti Chauta ndiye Mulungu.

Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake,

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

Paja Iye ndi wabwino.

Chikondi chake nchamuyaya,

Kukhulupirika kwake nkosatha.

 

Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.

 

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA CHIVUMBULUTSO: CHIVUMBULUTSO 7:9, 14b-17. (Mwanawankhosa uja adzakhala Mbusa wao ndipo

adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo).

 

Ine, Yohane, nditayang’ana, ndidaona chinamtindi cha anthu osawerengeka. Anthuwo anali ochokera m’mitundu yonse ya anthu, ndi m’mafuko onse, ndipo anali a zilankhulo zonse. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Mwanawankhosa uja; anali atavala mikanjo yoyera, nthambi zakanjedza zili m’manja. Ine ndidati, Mbuyanga, mukudziwa ndinu. Ndipo iye adandiwuza kuti, amenewa ndi amene adapambana m’masautso aakulu aja. Adachapa mikanjo yao ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa. Nchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndipo amampembedza m’Nyumba mwake usana ndi usiku. Wokhala pa mpando wachifumu uja adakhala ngati hema lao lowateteza. Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Sadzaombedwanso ndi dzuwa kapena kusauka ndi kutentha. Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse m’maso.

 

Mau a Ambuye... Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------


NYIMBO YA MTHENGA WABWINO—YOHANE 10:14.

 

Alleluia, Alleluia!! —Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziwa, ndipo

izozo Ineyo zimandidziwa. —Alleluia, Alleluia!!

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 10:27-30. (Ndimazipatsa moyo wosatha nkhosa zanga).

 

Yesu anati, “Nkhosa zanga zimamva mau anga. Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsatira. Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m’manja mwanga. Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m’manja mwao. Ine ndi Atate ndife amodzi.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, ndife mbumba ya Mulungu ndi nkhosa za busa lake. Tsono tonse pamodzi tipempherere zosowa zathu ndi za anthu onse:

 

1.     Tipempherere ansembe onse kuti azisenza udindo wao mokhulupirika potsatira Yesu Khristu Mbusa wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere anthu a mafuko onse kuti azindikire umodzi wao ndi ubale wao pakumva Mthenga Wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere anyamata ndi atsikana kuti avomere kuitana kwa Mulungu, ndipo akonzekere wino udindo wao.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tidzipempherere ife tomwe amene tasonkhana muno kuti mau a Mulungu agwire ntchito mwa ife ndi kutisandutsa mboni zenizeni za Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu Atate athu, musonkhanitse nkhosa zanu zonse mu ulamuliro wa Mwana wanu, kuti anthu onse akudziweni Inu Mulungu woona, ndiponso Iye amene mudamtuma, Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...