Saturday, February 22, 2025

LAMULUNGU LA 7 PA CHAKA – C

LAMULUNGU LA 7 PA CHAKA – C

“Kondani adani anu, muwachitire zabwino.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LOYAMBA LA SAMUELE: 1 SAMUELE 26:2. 7-9.12-13,22-23. (Chauta anakuperekani m' manja mwanga lero, koma sindidaphe munthu wodzozedwa ufumu).

 

Saulo adanyamuka napita ku chipululu cha Zifi atatenga ankhondo 3,000 osankhidwa, kuti akafunefune Davide kuchipululuko. Choncho Davide ndi Abisai adakalowa ku zithando zankhondo usiku. Saulo anali gone m'chithando chake, atazika mkondo wake pansi cha kumutu kwake. Abinere ndi ankhondo onse adaagona momzungulira. Abisai adauza Davide kuti, “Mulungu wapereka mdani wanu kwa inu lero. Bwanji tsono mundilole kuti ndimbaye ndi mkondo kamodzinkamodzi ndi kumkhomerera pansi, sindichita kumbaya kawiri.” Koma Davide adamuuza kuti, “Ai, usamuphe. Ndani angathe kupweteka wodzozedwa wa Chauta nakhala wosachimwa?” Motero Davide adatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwa Saulo, nachokapo. Palibe amene adaona zimenezo ngakhale kuzidziwa, ndipo panalibe wina aliyense amene adadzuka. Onse anali m'tulo, chifukwa chakuti Chauta adaawagonetsa tulo tofa nato. Pambuyo pake Davide adakwerera mbali ina nakaimirira pamwamba pa phiri, pakati nkusiya mpata waukulu. Apo Davide adayankha kuti, “Suwu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi mwa ankhondowo adzatenge. Chauta amadalitsa munthu wokhulupirika ndi wochita zabwino. Chauta anakuperekani m' manja mwanga lero, koma sindidaphe munthu wodzozedwa ufumu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 103:1-4,8,10,12-13.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

 

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera,

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga,

Ndipo usaiwale zabwino zake zonse.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

 

Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse,

Ndi kuchiritsa matenda ako onse,

Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda,

Amakuveka chikondi ndiponso chifundo chake, ngati chisoti chaufumu.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga,

Ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu,

Satilanga moyenerera machimo athu,

Satibwezera molingana ndi zolakwa zathu.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

 

Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe,

Ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu,

Monga bambo amachitira chifundo ana ake,

Ndi momwenso Chauta amawachitira chifundo omulemekeza.

 

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 15:45-49. (Monga takhala ofanafana ndi Adamu, munthu wopangidwa ndi dothi uja, momwemonso tidzakhala ofanafana ndi Khristu, munthu wa Kumwamba).

 

Abale, Malembo akuti, “Munthu woyamba uja, Adamu, adachita kusanduka chinthu chamnofu chokhala ndi moyo.” Koma Adamu wotsiriza adakhala chinthu chauzimu chopatsa moyo. Loyamba sithupi lauzimu ai. Loyamba ndi lamnofu, pambuyo pake lauzimu. Adamu woyamba uja anali wochokera ku dothi, anali wapansipano, Koma Khristu, Adamu wachiwiri uja, anali wochokera Kumwamba. Anthu onse apansipano ali ngati Adamu wopangidwa ndi dothi uja. Ndipo onse amene ali a Kumwamba, ali ngati Khristu wa Kumwamba. Monga takhala ofanafana ndi Adamu, munthu wopangidwa ndi dothi uja, momwemonso tidzakhala ofanafana ndi Khristu, munthu wa kumwamba.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 13:34.

 

Alleluia, Alleluia Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana; monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana, atero Ambuye. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 6:27-38 (Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo).

 

Yesu adawauza ophunzira ake kuti, “Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziwachitira zabwino amene amadana nanu. Muziwafunira madalitso amene amakutembererani, muziwapempherera amene amakuvutitsani. Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe. Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akatenga zinthu zako, usamlamule kuti abweze. Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo. Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakondanso amene amawakonda. Ngati muchitira zabwino okhawo amene amakuchitirani zabwino, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amachita chimodzimodzi. Ndipo ngati mukongoza okhawo amene mukudziwa kuti adzakubwezerani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakongoza anzao ochimwa, kuti akalandirenso momwemo. Iyai, inu muzikonda adani anu, muzichita zabwino, ndipo muzikongoza osayembekeza kulandirapo kanthu. Mukatero mudzalandira mphotho yaikulu, ndiye kuti mudzakhala ana a Mulungu Wopambanazonse. Pajatu Iye amachitira zabwino anthu osayamika ndi oipa omwe. Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo. Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu

sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani. Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu

muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

Abale, podziwa kuti chifundo cha Mulungu nchopanda malire, tiyeni tipemphe Atate athu a Kumwamba kuti adzaze mitima yathu ndi ya anthu onse ndi Mzimu wao wachikondi:

 

1.     Tipempherere Akhristu onse, kuti kukondana kwao kupite m’tsogolo, ndipo adziwe kugonjetsa zoipa pakuchita zabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere anthu a mafuko onse, kuti alekeretu kukangana, ndipo choncho mtendere ukhazikike pakati pa maiko ndi pakati pa magulu a anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

3.     Tipempherere mabanja onse kuti eni ake akhale a mtima umodzi ndipo adziwe kumakhululukirana mwamsanga chifukwa chokhulupirira Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe tipemphererane kuti timange moyo wathu pa chikondi chimene Ambuye amatikonda nacho, pomaonetsa anzathu mtima wachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikuyamika chikondi chanu chosasinthika ndi chifundo chanu chopanda malire. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...