LAMULUNGU LA 8 PA CHAKA – C
“Munthu wabwino amazindikirika chifukwa cha zochita zake.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPHUNZITSI: MPHUNZITSI 27:4-7. (Usatamande munthu usanamve zolankhula zake).
Munthu akagwedeza sefa, zinyatsi zimatsalira momwemo. Chimodzimodzinso zolakwa za munthu zimaoneka iye akamalankhula. Monga mbiya amaiyesa pa moto, momwemonso munthu amayesedwa pa zokamba zake. Monga chipatso cha mtengo chimatidziwitsa luso la mlimi, momwemonso zokamba za munthu zimaonetsa zimene zili mumtima mwake. Usatamande munthu usanamve zolankhula zake, poti mayeso enieni a anthu ali pamenepa.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 92:2-3,13-16.
Nkwabwino kuthokoza Chauta.
Nkwabwino kuthokoza Chauta,
Kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Nkwabwino m’mawa kulalika za chikondi chanu chosasinthika,
Ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu.
Nkwabwino kuthokoza Chauta.
Ali ngati mitengo yookedwa m’Nyumba ya Chauta,
Yokondwa m’mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu.
Nkwabwino kuthokoza Chauta.
Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba,
Nthawi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriwira,
Imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama.
iye ndiye thanthwe langa, mwa Iye mulibe chokhota.
Nkwabwino kuthokoza Chauta.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 15:54-58 (Tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu).
Abale, thupi lotha kuwolali likadzasanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzachitikadi zimene Malembo adanena kuti, Imfa yagonjetsedwa kwathunthu. Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti? Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo. Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziwa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AFILIPI 2:15d,16a.
Alleluia, Alleluia – Pakati pa anthu mumawala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi pakuwauza mau opatsa moyo. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 6:39-45. (Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima).
Yesu adawapheranso fanizo, adati, “Kodi wakhungu nkutsogolera wakhungu mnzake? Nanga onse awiri sadzagwa m’dzenje kodi? Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake. Umaoneranji kachitsotso kamene kali m’maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m’maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m’maso mwakoka, pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m’maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m’maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m’maso mwa mbale wako. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapenanso mtengo woipa kubala zipatso zabwino. Mtengo uliwonse umadziwika ndi zipatso zake. Sathyola nkhuyu pa minga, kapenanso mphesa pa mtula. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m’chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu
Abale, tikhale a mtima umodzi ndi Ambuye Yesu popereka kwa Mulungu mapemphero athu opempherera anthu onse:
Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikuyamika chifundo chanu chofuna kusonkhanitsa anthu onse mu Ufumu wanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_buttonBlog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment