LAMULUNGU LA 6 PA CHAKA – C
“Kodi munthu wodala ndani?”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA M’PROFETI YEREMIYA: YEREMIYA 17:5-8. (Tsoka kwa munthu wodalira munthu mnzake; ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta).
Chauta akunena kuti, “tsoka kwa munthu wodalira munthu mnzake, amene amagonera
pa munthu mnzake kuti amthandize, pamene mtima wake wafulatira Chauta. Woteroyo adzakhala ngati chitsamba m'chipululu, ndipo sadzapeza zabwino. Adzakhala m'chipululu mopanda madzi, m'dziko lamchere m'mene anthu sangathe kukhalamo. Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwamadzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhawa, ndipo suleka kubala zipatso.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 1:1-4.6.
Ngwodala munthu amene amadalira Chauta.
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa,
Wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa,
Wosakhala nawo m’gulu la anthu onyoza Mulungu,
Koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta,
Nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.
Ngwodala munthu amene amadalira Chauta.
Munthuyo ali ngati mtengo
Wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi.
Ngati mtengo wobereka zipatso pa nthawi yake,
Umene masamba ake safota konse.
Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.
Ngwodala munthu amene amadalira Chauta.
Anthu oipa sali choncho,
Ali ngati mungu wouluzika ndi mphepo.
Paja Chauta amawasamalira anthu ake.
koma anthu ochimwa adzaonongeka.
Ngwodala munthu amene amadalira Chauta.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 15: 12,16-21. (Ngati Khristu sadauke, chikhulupiriro chanu nchopanda pake).
Abale, popeza kuti chimene timalalika ndi chakuti Khristu adauka kwa akufa, bwanji ena mwa inu akunena kuti, “Anthu akufa sadzaukanso”? Pakuti ngati akufa sauka, Khristunso sadauke. Ndipotu ngati Khristu sadauke, chikhulupiriro chanu nchopanda pake, ndipo mukadali m'machimo anu. Pamenepo nawonso amene adamwalira ali okhulupirira Khristu, adatayika ndithu. Ngati taika chikhulupiriro chathu mwa Khristu chifukwa cha moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni koposa anthu ena onse. Koma ai, Khristu adauka ndithu kwa akufa. Pakati pa onse amene adafa, ndiye woyamba kuuka.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 06: 23ab.
Alleluia, Alleluia – Sangalalani ndi kuvina ndi chimwemwe, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 6:17,20-26. (Ndinu odala, inu osaukanu. Koma ndinu atsoka, anthu achumanu).
Yesu adatsika phiri pamodzi ndi ophunzira ake, naima pa chidikha. Panali khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi anthu ena ambirimbiri ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi ku Yerusalemu, ndi kumbali yakunyanja, ku Tiro, ndi Sidoni. Yesu adayang’ana ophunzira ake, nawauza kuti, “Ndinu odala, inu Osaukanu, Ufumu wa Mulungu ndi wanu. Ndinu odala, inu amene mukumva njala tsopano, chifukwa mudzakhuta. Ndinu odala, inu amene mukulira tsopano, chifukwa mudzakondwa. Ndinu odala anthu akamadana nanu, akamakusalani ndi kukuchitani chipongwe, ndipo akamaipitsa dzina lanu chifukwa cha Ine Mwana wa Munthu. Nthawi imeneyo sangalalani ndi kuvina ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi zomwenso makolo ao ankawachita aneneri kale. Koma ndinu atsoka, anthu achumanu, chifukwa mwalandiriratu zokusangalatsani. Ndinu atsoka, amene mukukhuta tsopanonu, chifukwa mudzamva njala. Ndinu atsoka, amene mukukondwa tsopanonu, chifukwa mudzamva chisoni ndiponso mudzalira. Ndinu atsoka, anthu onse akamakuyamikani. Paja makolo ao ankachitira aneneri onama akale zomwezi.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pakuti tikudalira Mulungu pa zonse, tiyeni timupemphe chithandizo chake pokumbukira zosowa zathu ndi za anthu onse:
1. Tipempherere Eklezia wa Yesu kuti mau ake ndi chifundo chake chosamala amphawi zidzetse ufumu wa Mulungu m’mitima ya anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Tipempherere akhristu amene akuzunzika chifukwa cha Mthenga Wabwino, kuti alimbe mtima ndi kukondwera, podziwa kuti mphoto yao njaikulu kumwamba.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Tipempherere anthu amene amangofuna za pansi pano zokha, kuti azindikire kulakwa kwao ndipo atembenukire kwa Mulungu ndi mtima wolapa.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tizipempherere ife tomwe kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wokomera Mulungu ndi wochitira anzathu zachifundo zambiri.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate okoma mtima, mverani mapemphero athu ndipo mutipatse ife tonse mtima wokhulupirira chikondi chanu chosasinthika. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment