LAMULUNGU LA 5 PA CHAKA – C
“Ambuye! Ndilipo, munditume.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA M’PROFETI YESAYA: YESAYA 6:1-8. (Ndilipo ineyo, tumeni).
Chaka chimene mfumu Uziya adamwalira, ndidaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu wautali ndi wokwezedwa. Mkanjo wao unali wautali kwambiri, kotero kuti udadzaza Nyumba yao yonse. Pamwamba pao padaaimirira Aserafi. Aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri ophimbira kumaso, awiri ophimbira mapazi, awiri oulukira. Aserafiwo ankafuulirana kuti, “ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse, ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi. Chifukwa cha kufuulako maziko onse ndi ziwundo adagwedezeka ndipo m’Nyumba ya Chautamo mudangoti utsi pha. Apo ine ndidati: “Tsoka langa ine! Ndatayika. Pakuti ndine munthu wa pakamwa poipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poipa. Komabe maso anga aona Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse.” Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja adaulukira kwa ine, ali ndi khala lamoto m’manja mwake. Khalalo adalichotsa pa guwa la nsembe ndi mbaniro. Ndipo adandikhuza pakamwa ndi khala lamotolo nati, “taona, ndakukhudza milomo ndi khalali. Kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.” Kenaka ndidamva mau a Ambuye akuti, “kodi ndidzatuma yani, ndani adzatipitire?” Apo ndidati, “ndilipo ineyo, tumeni.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 138:1-5, 7-8.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse,
Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu,
Ndikugwada mowerama,
Kunyumba kwa Nyumba yanu yoyera.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
Ndikutamanda dzina lanu,
Chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika,
Chifukwanso cha kukhulupirika kwanu,
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha,
Mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
Mafumu onse a m’dziko adzakutamandani, Inu Chauta,
Chifukwa amva mau a pakamwa panu,
Adzaimba nyimbo zotamanda njira za Chauta,
Pakuti ulemerero wa Chauta ndi waukulu.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya,
Dzanja lanu lamanja limandipulumutsa,
Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya,
Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 1 AKORINTO 15:1-11. (Zimene timalalika ndi zomwezo, zimene mudakhulupirira ndi zomwezonso).
Abale, ndifuna kukukumbutsani Uthenga Wabwino umene ndidakulalikirani. Mudaulandira, ndipo mudakhazikitsapo chikhulupiriro chanu molimba. Mulungu adzakupulumutsani ndi Uthenga Wabwinowu, ngati musunga bwino mau ake monga ndidakulalikirani. Popanda kutero, bwenzi mutangokhulupirira pachabe. Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera. Adaikidwa m’manda, mkucha wake adauka, monga Malembo anenera. Motero adaonekera Kefa, kenaka atumwi khumi ndi awiri aja. Pambuyo pake adaonekera abale opitirira mazana asanu pa nthawi imodzi. Ambiri mwa iwowo akalipo, ena adamwalira. Ndipo adaonekera Yakobo, kenaka atumwi onse. Potsiriza, pambuyo pa onse adandiwonekeranso ineyo, ngakhale ndili ngati mpolo chabe. Inetu ndine wamng’onong’onodi mwa atumwi onse. Sindine woyenera konse kuti ndizitchedwa mtumwi, pakuti ndinkazunza Mpingo wa Mulungu. Koma chifukwa chakuti Mulungu adandikomera mtima, ndili monga ndilirimu. Ndipo kukoma mtima kwakeko sikunali kopanda phindu, popeza kuti ndidagwira ntchito koposa atumwi ena onse. Komabe si ndine ndidaigwira, koma mphamvu za Mulungu zimene zikundilimbikitsa. Motero kaya ndi ineyo kaya ndi iwowo, zimene timalalika ndi zomwezo, zimene mudakhulupirira ndi zomwezonso.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 4:19.
Alleluia, Alleluia – Inu, munditsate, atero Ambuye, ndikakusandetseni asodzi a anthu – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 5:1-11. (Adasiya zonse namatsata Yesu).
Tsiku lina Yesu adaimirira pamphepete pa nyanja ya Genesarete, anthu ambirimbiri nkumamupanikiza kuti amve mau a Mulungu. Iye adaona zombo ziwiri pamphepetepo. Asodzi anali atatulukamo, ndipo ankatsuka makoka ao. Yesu adalowa m’chombo chimodzi, chimene chinali cha Simoni, nampempha kuti asunthire pang’ono ku nyanja. Adakhala pansi, ndipo ali m’chombo momwemo, adayamba kuwaphunzitsa anthuwo. Atatsiriza kulankhula, adauza Simoni kuti, “Sunthirani kozamako, muponye makoka anu kuti muphe nsomba.” Simoni adati, “Aphunzitsi, usiku wonsewu takhalira kugwira ntchito, osapha kanthu, koma chifukwa Inuyo mwatero, chabwino ndiponya makoka.” Tsono iwo adaponyadi makoka, napha nsomba zambirimbiri, kotero kuti makokawo ankayamba kung’ambika. Adachita kukodola anzao a m’chombo china chija kuti adzawathandize. Iwo adabwera, ndipo adadzaza zombo ziwiri zonse zija mpaka zinali pafupi kumira. Pamene Simoni Petro adaona zimenezo, adagwada nkuwerama kwambiri pamaso pa Yesu nati, “Pepani Ambuye, mundichokere, ndine munthu wochimwa.” Adaatero popeza kuti iye, pamodzi ndi onse amene anali naye, adaazizwa nako kuchuluka kwa nsomba zimene adaaphazo. Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, anzake a Simoni, nawonso adaazizwa. Tsono Yesu adauza Simoni kuti, “Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.” Motero, atakokera zombozo ku mtunda, adasiya zonse namatsata Yesu.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, popeza kuti Mulungu saleka kuitana anthu ku ntchito yake, tiyeni, timudziwitse zosowa zathu ndi za anthu onse:
1. Atate, mudalitse Apapa, Aepiskopi ndi ansembe onse kuti asenze udindo molimbika, azitsogolera bwino anthu ao pa njira ya chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atate, muitane anyamata ndi atsikana ambiri kuti adzipereke ndi mtima wonse ku ntchito yodziwitsa anzao Mthenga wanu Wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Atate, muunikire nzeru za akhristu onse, kuti azindikire udindo wao ndipo ayesetse kukokera anzao mu ufumu wanu.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Atate, mutithandize ife tomwe kuti tikhale akhristu achangu pomatekeseka ndi chipulumutso cha anzathu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Mulungu Atate athu, sindife oyenera konse kuti tikhale atumwi anu. Komabe tikukhulupirira Inu, muzitithandiza kukutumikirani moyenera. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment