CHAKA CHA KUPEREKEDWA KWA AMBUYE YESU KU TEMPILE
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI MALAKI: MALAKI 3:1-4 (Chauta amene mukumfunafuna adzafika ku Nyumba yake).
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzatuma wamthenga wanga kuti akandikonzere njira. Kenaka mwadzidzidzi Chauta amene mukumfunafuna adzafika ku Nyumba yake. Wamthenga wa chipangano, amene mukumuyembekeza, suuyu akubwera. Kodi ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Kodi ndani adzatha kulimbikira iye akadzafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wapang’anjo, ndiponso ngati sopo wa munthu wochapa. Adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri wapang’anjo woyeretsa siliva, ndipo adzayeretsa Alevi monga amayeretsera golide ndi siliva, mpaka kuti azidzapereka nsembe zoyenera kwa Chauta. Choncho nsembe za Yuda ndi za Yerusalemu zidzakondweretsa Chauta, monga zidaaliri masiku amakedzana.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 24:7-10.
Kodi mfumu ya ulemereroyo ndani?
Kankhani zipata za mzinda,
tsekulani zitseko zakalekalezo,
kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
Kodi mfumu ya ulemereroyo ndani?
Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
Ndi Chauta wanyonga ndi wamphamvu,
Chauta ndiye ngwazi pa nkhondo.
Kodi mfumu ya ulemereroyo ndani?
Kankhani zipata za mzinda,
tsekulani zitseko zakalekalezo,
kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
Kodi mfumu ya ulemereroyo ndani?
Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
Ndi Chauta Wamphamvuzonse.
Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero.
Kodi mfumu ya ulemereroyo ndani?
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA KWA AHEBRI: AHEBRI 2:14-18 (Iye adaayenera kusanduka wofanafana ndi abale ake pa zonse).
Abale, popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa. Pakutero adafunanso kuti awamasule amene pa moyo wao wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa. Paja nchodziwikiratu kuti sadatekeseke ndi angelo ai koma ndi zidzukulu za Abrahamu. Nchifukwa chake adaayenera kusanduka wofanafana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe onse wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, ndipo kuti pakutero achotse machimo a anthu. Tsono popeza kuti iye yemwe adazunzikapo ndi kuyesedwapo, ndiye kuti angathe kuwathandiza anthu amene amayesedwa.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 2:32.
Alleluia, Alleluia – “Mwapereka kuwala kodzaunikira anthu a mitundu ina, kudzakhala ulemerero wa anthu anu Aisraele.” – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 2:22-40 (Ndi maso angawa ndachiwonadi chipulumutso).
Idafika nthawi yoti Yosefe ndi Maria achite mwambo wakuyeretsedwa potsata Malamulo a Mose. Tsono mwanayo adapita naye ku Yerusalemu kuti akampereke kwa Ambuye. Pajatu m'Malamulo a Ambuye muli mau akuti, “Mwana aliyense wamwamuna, woyamba kubadwa, apatulidwe kuti akhale wao wa Ambuye.” Adakaperekanso nsembe potsata Malamulo a Ambuye akuti, “Apereke njiwa ziwiri kapena maunda awiri.”
Ku Yerusalemuko kunali munthu wina, dzina lake Simeoni. Anali munthu wolungama ndi woopa Mulungu. Ankayembekezera nthawi yoti Mulungu adzapulumutse Aisraele, ndipo Mzimu Woyera anali naye. Mzimu Woyerayo adaamuululira kuti sadzafa asanaone Mpulumutsi amene Mulungu adaalonjeza. Tsiku lina Mzimu Woyera adamlamula kuti apite ku Nyumba ya Mulungu. Makolo a Yesu adalowanso m’Nyumbamo ndi mwana waoyo kukamchitira mwambo potsata Malamulo a Mose. Pamenepo Simeoni adalandira mwanayo m'manja mwake, nayamba kutamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu, ndipite ndi mtendere, pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi. Ndi maso angawa ndachiwonadi chipulumutso chija, chimene mudakonza kuti anthu a mitundu yonse achiwone. Mwapereka kuwala kodzaunikira anthu a mitundu ina, kodzakhala ulemerero wa anthu anu Aisraele.”
Atate ndi amai a mwanayo ankangodabwa nazo zimene Simeoni ankanena za mwanayo. Kenaka Simeoniyo adawadalitsa, nauza Maria, mai wa mwanayo, kuti, “Mwanayu Mulungu wamuika kuti Aisraele ambiri adzagwe, ambirinso adzadzuke, chifukwa cha iyeyu. Adzakhala chizindikiro chochokera kwa Mulungu, chimene anthu ambiri adzatsutsana nacho, kuti choncho maganizo amene ali m’mitima ya anthu ambiri adzaonekere poyera. Ndipo inunso mai, chisoni chidzabaya mtima wanu ngati lupanga.”
Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziwiri zokha, pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya. Iye adafikako nthawi yomweyo, nayamba kuyamika Mulungu, nkumakamba za Mwanayo ndi anthu onse amene ankayembekezera nthawi yoti Mulungu adzapulumutse Yerusalemu. Yosefe ndi Maria atachita zonse potsata Malamulo a Ambuye, adabwerera ku Galileya, kumudzi kwao ku Nazarete. Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB
No comments:
Post a Comment