Saturday, December 14, 2024

LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENTI – C [Gaudete Sunday]

                              LAMULUNGU LA 3 MU NYENGO YA ADVENTI – C.       

[Gaudete Sunday]

“Kondwani nthawi zonse: Ambuye ali pafupi.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI ZEFANIYA: ZEFANIYA 3:14-18. (Mulungu wako adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe).

 

Imbani mokweza, inu anthu a ku Ziyoni! Fuulani inu Aisraele! Sangalalani, kondwani ndi mtima wonse, inu okhala mu Yerusalemu. Chauta wachotsa chilango chanu. Wapirikitsa adani anu. Chauta, Mfumu ya Aisraele, ali nanu pamodzi. Simudzaopanso choipa chilichonse. Tsiku limenelo adzauza Yerusalemu kuti, Usaope, iwe Ziyoni, usataye mtima. Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m’chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe. Monga pa masiku achikondwerero, ndidzakuchotsera tsoka, limene lingokuvutitsa ndi kukunyozetsa.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: YESAYA 12:2-6.

 

Fuulani ndi kuimba mokondwa, pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.

 

Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga,

Ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa,

Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa,

Ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.

 

Fuulani ndi kuimba mokondwa, pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.

 

Mudzakondwera pokatunga madzi m’zitsime za chipulumutso,

Tsiku limenelo mudzati: “Thokozani Chauta,

Tamandani dzina lake,

Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,

Mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.”

 

Fuulani ndi kuimba mokondwa, pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.

 

Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu,

Zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi,

Fuulani ndi kuimba mokondwa, inu anthu a ku Ziyoni,

Pakuti Woyera uja wa Aisraele ndi wamkulu pakati panu.

 

Fuulani ndi kuimba mokondwa, pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI: AFILIPI 4:4-7. (Ambuye tu ali pafupi).

 

Abale, muzikondwa mwa Ambuye nthawi zonse. Ndikubwerezanso kuti, muzikondwa. Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi. Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma m’mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusowani, ndipo nthawi zonse muzipempha ndimtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YESAYA 61:1 (OTENGEDWA PA LUKA 4:18).

Alleluia, Alleluia Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa Ine. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 3:10-18. (Kodi ife tizichita zabwino zanji?)

 

Pamenepo anthu aja adafunsa Yohane kuti, “tsono ife tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “amene ali ndi miinjiro iwiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.” Kudabweranso okhometsa msonkho kuti Yohane awabatize. Iwo adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ife tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “musamakhometsa msonkho moonjezera pa zimene adakulamulani.” Asilikali omwe adamufunsa kuli, “nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.” Chiyembekezo cha anthu chidaayamba kukula, ndipo onse ankaganiza za Yohane ankawauza onse kuti, “ine ndimakubatizani ndi madzi, koma akubwera wina woposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso moto. Chopetera chake chili m’manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m’nkhokwe, koma mankhusu adzawatentha m’moto wosazimika.” Yohane ankalalikira anthu Uthenga Wabwino pakuwalangiza motero, ndiponso mwa njira zina zambiri.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, Paulo Woyera watiuza kuti: m’mapemphero anu onse muzipempha ndi mtima woyamika. Tiyeni tsono, titule m’manja mwa Atate athu a Kumwamba mapemphero athu ndi madandaulo a anthu onse:

 

1.     Atate, mulimbitse atsogoleri a Mpingo kuti asaleke kuphunzitsa anthu ao za kulapa ndi kukonzera Mwana wanu njira yake.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Tipempherere akhristu onse kuti akhale ofatsa ndi okondwa nthawi zonse, kusonyeza kuti Ambuye ali pafupi.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Tipempherere odwala, ovulala ndi onse amene ali m’mavuto, kuti apeze anzawo achifundo odzawasangalatsa ndi kuwathandiza m’zosowa zao.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Tipempherere mafuko onse a pansi pano kuti akhale oyanjana, ndipo ponseponse pakhale mtendere ndi chilungamo.
Tikupemphani, mutivomereze.

5.     Tidzipempherere ife tomwe tili muno, kuti kukondana kwathu kupite m’tsogolo, ndipo ntchito zathu zachifundo zidzetse chimwemwe m’mitima ya anthu.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Mulungu wathu, tikukuyamikani chifukwa mwatipatsa chitsimikizo chakuti Ambuye ali pafupi. Mutiphunzitse kuyembekeza kudza kwao ndi mtima wokondwa. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...