LAMULUNGU LA 2 MU NYENGO YA ADVENTI – C.
“Tikonze mseu woti Ambuye adzeremo”.
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI BARUKI: BARUKI 05: 01 – 09. (Mulungu akufuna kuwonetsa ulemerero wako).
Iwe Yerusalemu, vula chovala chako chamaliro ndi chachisoni. Uvale mpaka muyaya zovala za ulemerero wa Mulungu. Funda mwinjiro wachilungamo wochokera kwa Mulungu. Vala chisoti cha ulemerero wa Mulungu wamuyaya. Chifukwa Mulungu akufuna kuwonetsa ulemerero wako kwa onse okhala pansi pa thambo lakumwamba. Mulungu adzakutcha dzina limene mpaka muyaya lidzakhala “mtendere wa chilungamo” ndipo “ulemerero wa chipembedzo”. Dzuka, iwe, Yerusalemu, imirira pamtundapo, uyang’ane kuvuma. Ona ana ako amene Woyera uja wawasonkhanitsa kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Akukondwa pakuti Mulungu wawakumbukira. Adakusiya akuyenda pansi, adani ao atawatenga. Koma Mulungu adzawabwezanso kwa iwe, utawanyamula mwaulemerero ngati ana a ku nyumba ya mfumu. Pajatu Mulungu adalamula kuti mapiri aatali ndi zitunda zosatha azichepetse, ndiponso kuti zigwa azifotsere kuti mbali zonse zilingane. Motero Aisraele adzayenda mwamtendere mu ulemerero wa Mulungu. Potsata lamulo la Mulungu nkhalango ndi mitengo yonse ya fungo labwino zidzawakonzera mthunzi Aisraele. Zoonadi Mulungu adzatsogolera Aisarele mwachimwemwe ndi kuwala kwa ulemerero wake, ndiponso ndi chifundo ndi chilungamo chake.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 126.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni,
Tinali ngati anthu amene akulota,
Pamenepo tidasekera kwambiri,
Ndipo tidalulutira ndi chimwemwe.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
Tsono mitundu in ya anthu inkanena kuti,
“Chauta wawachitira zazikulu,”
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu,
Ndipo tasangalala.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
Tibwezereni ufulu wathu, Inu Chauta,
Tikhale ngati mitsinje yam’chipululu,
Anthu amene amafesa akulira,
Adzakolola akufuula ndi chimwemwe.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
Munthu amene amapita akulira,
Atatenga mbeu zokafesa,
Adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe,
Atatenga mitolo yake yambiri.
Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala.
---------------------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AFILIPI: AFILIPI 01: 03 – 06, 08 – 11. (Mudzapezeka oyera mtima, ndi opanda cholakwa chilichonse).
Abale, ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikamakukumbukirani. Nthawi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano. Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu. Mulungu akundichitira umboni kuti ndimakulakalakani kwambiri, pakuti ndimakukondani ndi mtima wonse, motsanzira chikondi cha Khristu Yesu mwini. Pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chinke chikukulirakulira pamodzi ndi nzeru ndi kumvetsetsa zinthu mozama. Pamenepo mudzadziwa kusankha zimene zili zabwino kotheratu. Apo pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu mudzapezeka oyera mtima, ndi opanda cholakwa chilichonse. Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 3:4, 6.
Alleluia, Alleluia – Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo. Motero anthu onse adzaona chipulumutso chochokera kwa Mulungu. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 03:1–6. (Anthu onse adzaona chipulumutso chochokera kwa Mulungu).
Pa chaka cha khumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio, mfumu ya ku Roma, Ponsio Pilato anali bwanamkubwa ku Yudeya. Herode ankalamulira ku dera la Galileya. Filipo, m’bale wake, ankalamulira ku dera la Itureya ndi ku dera la Trakoniti. Lisaniasi ankalamulira ku dera la Abilene, ndipo Anasi ndi Kayafa anali akulu a ansembe onse. Pa nthawi imeneyo Mulungu adampatsira uthenga Yohane uja, mwana wa Zakariya, m’chipululu. Choncho Yohaneyo adayendera dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yordani, akulalika. Ankauza anthu kuti, “tembenukani mtima ndi kubatizidwa, kuti Mulungu akukhululukireni machimo anu.” Izi zidaachitika monga zidaalembedwera m’buku la mneneri Yesaya kuti, “Liwu la munthu wofuula m’chipululu: akunena kuti, Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo. Dzadzani chigwa chilichonse, chepetsani phiri lililonse ndi mtunda uliwonse. Ongolani njira zokhotakhota, salazani njira zazigolowondo. Motero anthu onse adzaona chipulumutso chochokera kwa Mulungu.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tiyeni, tikweze mapemphero athu kwa Mulungu Atate athu, pokumbukira zosowa zathu ndi za anthu onse:
1. Atate, mulimbitse atsogoleri a Mpingo kuti asaleke kuphunzitsa anthu ao za kulapa ndi kukonzera Mwana wanu njira yake.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atate, muunikire anthu a mafuko onse kuti aone chipulumutso chimene Mwana wanu Yesu Khristu adadzatipatsa.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Atate, muyang’ane ndi chifundo akaidi, odwala ndi onse amene ali m'mavuto: muutse chikhulupiriro m'mitima mwao pa masiku ano odikira Khrismasi.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Atate, muthandize akhristu onse ofooka ndi olowerera, kuti abwerere kwa Mpulumutsi wao ndi wolapa pokhulupirira chifundo chanu.
Tikupemphani, mutivomereze.
5. Atate, mulimbitse chikondi chanu m'mitima mwathu, kuti moyo wathu ukhale wodzaza ndi zipatso za chilungamo.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate achifundo, mwatisonkhanitsa pano kuti tikonze mseu woti Ambuye adzeremo. Mverani mapemphero athu ndi kutikhazikitsa M’chikhulupiriro chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment