Saturday, December 21, 2024

LAMULUNGU LA 4 MU NYENGO YA ADVENTI – C

LAMULUNGU LA 4 MU NYENGO YA ADVENTI – C.

“Ndiwe odala kuti ukukhulupirira.”

 

MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI MIKA: MIKA 5:1-4. (Mwa iwe ndidzatulutsa munthu amene adzakhala wolamulira Israele).

 

Tsopano konzekani m’magulu ankhondo, inu a ku Yerusalemu. Atizinga ndi zithando zankhondo, akuthira nkhondo likulu la Israele. Za Mfumu yochokera ku Betelehemu Chauta akuti, koma iwe Betelehemu wa ku Efuruta, inde ndiwe wamn’gono pakati pa mafuko a Yuda, komabe mwa iwe ndidzatulutsa munthu amene adzakhala wolamulira Israele. Iyeyo chiyambi chake nchakalekale, cha masiku amakedzana. Nchifukwa chake Mulungu adzasiya Israele mpaka nthawi yoti achire mkazi amene adzabale mwana. Pamenepo, otsala a mtundu wake adzabwereranso kwa Aisraele anzao. Iye adzalimbikira, ndipo adzaweta nkhosa zake mwa mphamvu za Chauta ndi ulemerero wa dzina la Chauta, Mulungu wake. Ndipo iwo adzakhala mu mtendere, poti ukulu wake udzakhazikika pa dziko lonse lapansi.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 80:2-3,15-19.

 

Inu Mulungu, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.

 

Imvani, Inu Mbusa wa Israele,

Inu amene mumakhala pa akerubi,

Ngati pa mpando wanu wachifumu, Onetsani mphamvu zanu,

Ndipo mubwere kudzatipulumutsa.

 

Inu Mulungu, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.

 

Mutembenukirenso kwa ife, inu Mulungu Wamphamvuzonse,

Muyang’ane Inu okhala kumwamba, ndipo muwone,

Samalani mpesawo, mtengo woyambirira,

Umene Inu mudaubzala ndi dzanja lanu lamanja.

 

Inu Mulungu, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.

 

Ndi dzanja lanu muteteze anthu amene mudawasankha,

Anthu amene Inu nomwe mwawalimbikitsa,

Tsono sitidzakusiyaninso, tipatseni moyo,

Ndipo tidzatama dzina lanu mopemba.

 

Inu Mulungu, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.

---------------------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’KALATA KWA AHEBRI: AHAEBRI 10:5-10. (Ndabweratu kuti ndichite zimene mukufuna).

 

Abale, pamene Khristu adadza pansi pano, adati, Inu Mulungu simudafune nsembe kapena zopereka, koma thupi mudandikonzera. Nsembe zoocha kwathunthu ndi nsembe zoperekera machimo, simudakondwere nazo. Tsono ine ndidati, Inu Mulungu, ndabweratu kuti ndichite zimene mukufuna, paja zidalembedwa choncho ponena za Ine m’buku la Malamulo. Motero poyamba adati, nsembe kapena zopereka, nsembe zopsereza kwathunthu kapenanso nsembe zopereka machimo, simudazifune ndipo simudakondwere nazo. Zimenezi nzimene Malamulo adaanena kuti ziperekedwe. Koma pambuyo pake adati, ndabweratu, kuti ndichite zimene mukufuna. Motero Khristu adathetsa mphamvu za nsembe ya mtundu wachiwiriyo. Chifukwa chakuti Yesu Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – LUKA 1:38.

Alleluia, Alleluia Ndine Mtumiki wa Ambuye; zindichitikire monga mwaneneramo. Alleluia, Alleluia.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 1:39–44. (Ine ndine yani kuti inu, mai wa Ambuye anga, mudzandiyendere?)

 

Patapita masiku owerengeka, Maria adanyamuka napita mofulumira ku dera lamapiri, ku mudzi wina wa ku Yudeya. Adakalowa m’nyumba ya Zakariya, nalonjera Elizabeti. Pamene Elizabeti adamva malonje a Maria, mwana adayamba kutakataka m’mimba mwake. Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adalankhula mokweza mau kuti, “ndinu odala kupambana akazi ena onse, ngwodalanso Mwanu wanu. Ine ndine yani kuti inu, mai wa Ambuye anga, mudzandiyendere? Chifukwatu pamene ndidamva malonje anu, mwana anayamba kutakataka ndi chimwemwe m’mimba mwanga.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, mogwirizana ndi Amai Maria, tipempherere anthu onse, kuti chikondwerero cha Khrismasi chiwutse chikhulupiriro ndi chimwemwe m’mitima mwao:

1.     Atate, muwongolere Mpingo wanu woyera kuti upitirize ntchito yake pakulalikira anthu onse Mthenga Wabwino wa chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, muyanjanitse anthu a mafuko onse kuti mtendere wanu ukhazikike m'mitima ya anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, mupatse akazi onse amene ali ndi pakati chikhulupiriro cholimba, kuti ayembekeze ndi chikondi chachikulu kubadwa kwa ana ao.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate, mutithandize ife tomwe tili muno, kuti chikhulupiriro chathu chitsimikizike ndi ntchito zotumikira anzathu mwachifundo.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate achifundo, tikupemphani zimenezi mosaopa ndi mosakayika, chifukwa mwatikomera mtima kopambana potipatsa Mwana wanu wokondeka Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://business.facebook.com/latest/home?asset_id=109826477067295&business_id=1326098184199637&nav_ref=profile_plus_profile_left_nav_button

Blog: https://www.blogger.com/blog/posts/2477989519106302629?hl=en-GB

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...