LAMULUNGU LA 1 MU NYENGO YA ADVENTI – C.
“Tikonzekere Kubwera Kwa Ambuye.”
MAU OYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA MPROFETI YEREMIYA: YEREMIYA 33:14 – 16. (Ndidzaphukitsa nthambi yolungama kuchokera kubanja kwa Davide).
Chauta akutinso, “akubwera masiku pamene ndidzachitadi zimene ndidalonjeza anthu a ku Israele ndi aku Yuda. Masiku amenewo ndiponso pa nthawi yomweyo, ndidzaphukitsa nthambi zolungama kuchokera kubanja la Davide. Munthuyo adzachita zabwino ndi zolungama mdziko lonse. Nthawi imeneyo anthu a ku Yuda adzapulumuka, ndipo a ku Yerusalemu adzakhala pa mtendere. Motero mzindawo udzakhala ndi dzina loti, ‘Chauta ndiye chipulumutso chathu.’”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 24: 04 – 05, 08 – 09, 10, 14.
Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta.
Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta,
Mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu,
Munditsogolere m’choona chanu ndi kundilangiza,
Pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga,
Ndimadalira Inu Masiku onse.
Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta.
Chauta ndi wabwino ndi wolungama,
Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake,
Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama,
Amawaphunzitsa njira zake.
Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta.
Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika,
Nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake,
Chauta amapalana chibwenzi ndi anthu omvera Iye,
Ndipo amawadziwitsa chipangano chake.
Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta.
--------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA ATESALONIKA: 1 ATESALONIKA 03: 12 – 04. (Ambuye adzalimbitse mitima yanu kuti idzakhale yangwiro pamene Yesu adzabweranso).
Abale, Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira. Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabweranso pamodzi ndi oyera ake onse. Potsiriza tsono, abale, tifuna kukupemphani kanthu. Mudalandira kwa ife mau onena za m’mene muziyendera kuti mukondweretse Mulungu. Mukutsata mayendedwe otere kumene, koma tikukupemphani kolimba m’dzina la Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale. Pakuti mukudziwa malangizo amene tidakupatsani ochokera kwa Ambuye Yesu.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – SALIMO 85:8.
Alleluia, Alleluia – Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA LUKA WOYERA: LUKA 21: 25 – 28, 34 – 36 (Chipulumutso chanu chayandikira).
Pa nthawi yomweyo, Yesu anati kwa ophunzira ake: “padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, pa mwezi ndi pa Nyenyezi. Pansi pano anthu a mitundu yonse adzada nkhawa nkutha nzeru, pomva kukokoma kwa nyanja ndi mafunde ake. Ena adzakomoka ndi mantha poyembekezera zimene zikudza pa dziko lonse lapansi, pakuti mphamvu zonse zakuthambo zidzagwedezeka. Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire nkukweza mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira. Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhawa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa. Pajatu lidzawagwera ngati nsampha anthu onse a pa dziko lonse lapansi. Muzikhala maso tsono, ndipo muzipepemphera nthawi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Ambuye atiwuza kuti, tizikhala maso ndi kumapemphera nthawi zonse. Tiyeni tsono, tikweze mitima kumwamba, kuti Ufumu wa Mulungu udze m’dziko lonse lapansi:
1. Tipempherere Mpingo woyera wa Mulungu, kuti maphunzitso ake ndinso ntchito zake ziwutse chikhulupiriro, m’mitima ya anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Tipempherere anthu a mafuko onse kuti atsekule mitima yawo ndi kulandira Mthenga Wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Tipempherere anthu odwala ndi onse amene ali m’mavuto, kuti asataye mtima, koma apeze anzao achifundo owathandiza.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Tipempherere onse amene ali ndi ana, kuti ayesetse kuutsa chikhulupiriro m’mitima ya ana aowo, powafotokozera za kudza kwa Mpulumutsi.
Tikupemphani, mutivomereze.
5. Tidzipempherere ife tomwe tili muno, kuti Mulungu akulitsirekulitsire kukondana kwathu, ndiponso chikondi chathu cha pa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.
Mulungu Atate athu, mutiphunzitse kuyembekeza mosafookera kubwera kwa Mwana wanu, kuti akadzagogoda pakhomo pathu, adzatipeze tili maso ndikupemphera. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295