LAMULUNGU LA 26 PA CHAKA – B.
“Tileke Makhalidwe Akaduka ndi Akudzikonda.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA NUMERI: NUMERI 11: 25 – 29. (Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikadakondwa anthu onse a Chauta akadakhala aneneri).
Chauta adatsika mu mtambo nayamba kulankhula ndi Mose. Ndipo adatengapo mzimu umene unali pa Moseyo nauika pa akuluakulu makumi asanu ndi awiriwo. Koma sadapitirire kulosako. Anthu awiri adatsalira m’mahema, wina anali Elidadi, wina Meladi, ndipo mzimu udakhala pa iwowo. Anali nao m’gulu la olembedwa aja, koma sadapite nao ku chihema chamsonkhano, motero ankalosera m’mahema. Ndiye mnyamata wina adathamanga nakauza Mose kuti, “Elidadi ndi Meladi akulosa kumahemaku.” Apo Yoswa, mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose, mmodzi mwa anthu ake osankhidwa aja, adati, “Mbuyanga Mose, aletseni amenewo.” Koma Mose adamuuza kuti, “kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikadakondwa anthu onse a Chauta akadakhala aneneri, ndipo Chauta akadaika mzimu wake pa iwo.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 19: 08, 10, 12 – 14.
Malangizo a Chauta amasangalatsa mtima.
Malangizo a Chauta ndi olungama,
Amasangalatsa mtima,
Malamulo a Chauta ndi olungama,
Amapatsa mtima womvetsa.
Malangizo a Chauta amasangalatsa mtima.
Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro,
Chimakhala mpaka muyaya,
Chiweruzo cha Chauta nchoona,
Ncholungama nthawi zone.
Malangizo a Chauta amasangalatsa mtima.
Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu,
Powasunga ndimalandira mphotho yaikulu,
Nanga ndani angathe kudziwa zolakwa zonse?
Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika.
Malangizo a Chauta amasangalatsa mtima.
Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala,
Kulakwa koteroku ndisakutsate,
Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu.
Malangizo a Chauta amasangalatsa mtima.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA YAKOBE: YAKOBE 05: 01 – 06. (Chuma chanu chaola).
Mverani tsono, inu anthu achumanu. Lirani ndi kufuula chifukwa cha zovuta zimene zikudzakugwerani. Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza. Antchito okolola m’minda mwanu simudawalipire. Ndalama zamalipirozo zikulira mokutsutsani. Ndipo kufuula kwa okololawo kwamveka m’makutu a Chauta Mphambe. Mwakhala mukuchita maphwando, ndipo mwalidyera dziko lino lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lopha anthu. Mwamuweruza kuti ngwolakwa ndipo mwamupha munthu wolungama, iye osalimbalimba.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – Cf. YOHANE 17: 17b, 17a.
Alleluia, Alleluia – Mau anuwo ngoona zedi, Ambuye, mutipatule ndi mau anu kuti tikhale anthu anu. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 09: 38 – 43, 45, 47 – 48. (Wosatsutsana nafe, ndi wogwirizana nafe ameneyo).
Yohane adauza Yesu kuti, “aphunzitsi, ife tinaona munthu wina akutulutsa mizimu yoipa potchula dzina lanu, ndiye ife tinayesa kumletsa chifukwa sayenda nafe.” Koma Yesu adati, “musamletse ai, chifukwa munthu sangati atachita zamphamvu m’dzina langa, nthawi yomweyo nkundinyoza. Chifukwa wosutsana nafe, ndi wogwirizana nafe ameneyo. Aliyense amene akupatsani chikho cha madzi chifukwa chakuti ndinu ake a Khristu, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake. Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Inewa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m’khosi ndi kukamuponya m’nyanja. Tsono ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino kuti ukalowe ku moyo wosatha uli woduka dzanja, kupambana kuti ukalowe uli ndi manja onse awiri ku Gehena, kwa moto wosazimika. Ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino kuti ukalowe ku moyo wosatha uli woduka phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku Gehena uli ndi miyendo yonse. Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi bwino kuti ukalowe mu Ufumu wa Mulungu uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti akakuponye ku Gehena uli ndi maso onse awiri. Kumeneko mphutsi zowazunza sizifa, moto wakenso wowatentha suzima.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, tikweze mapemphero athu kwa Mulungu amene afuna kupulumutsa anthu onse, nagwira ntchito mu mtima wa aliyense:
1. Atate, musaleke kuyeretsa ndi kuwongolera Mpingo wanu kuti anthu ake akhale oyera mtima monga Inu nomwe Atate muli oyera.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Atate, mupatse atsogoleri onse mtima wodzichepetsa, kuti asenze udindo wao modziiwala, potsata ubwino wa anthu onse.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Atate, mufewetse mitima ya anthu opata kuti asaumirire chuma, koma adziwe kuthandiza anzao amene ali m’mavuto.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Atate, mutithandize ife tomwe kuleka maganizo a kunyada ndi a kudzikonda, kuti mayendedwe athu akhale ogwirizana ndi Mthenga Wabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate achifundo, muunike m’mitima ya anthu onse, muwaongolere ndi Mzimu wanu Woyera, kuti azindikire chipulumutso chanu. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295