Saturday, March 16, 2024

LAMULUNGU LA 05 MUNYENGO YA LENTI – B

LAMULUNGU LA 05 MUNYENGO YA LENTI – B

“Mbeu ikagwa m’nthaka ndi kufa, imabala zipatso zambiri.”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LACHIWIRI LA YEREMIYA: YEREMIYA 31: 31 – 34. (Ndidzachita chipangano chatsopano ndi anthu a ku Israele ndi a ku Yuda. Sichidzakhalanso ngati chipangano chimene ndidachita ndi makolo ao).

 

Chauta akunena kuti, “akubwera masiku pamene ndidzachite chipangano chatsopano ndi anthu a ku Israele ndi a ku Yuda. Sichidzakhalanso ngati chipangano chija chimene ndidaachita ku dziko la Ejipito. Chipangano chimenecho iwo adaphwanya, ngakhale ndinali Mbuye wao. Koma chipangano chimene ndidzachite ndi anthu a ku Israele atatha masiku amenewo, ndi ichi; Ndidzaika malamulo anga mwa iwo, ndidzachita kuwalemba m’mitima mwao. Tsono Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga. Nthawi imeneyo wina sazidzachitanso kuphunzitsa mnzake kapena mbale wake kuti adziwe Chauta. Pakuti onsewo, ana ndi akulu omwe adzandidziwa, ndidzawakhululikira machimo ao, sindidzakumbukiranso machimo aowo,” akuterotu Chauta.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 137: 01 – 06.

 

Ndithudi, Inu mumakonda mtima woona.

 

Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,

Malinga ndi chikondi chanu chosasinthika,

Mundisambitse kwanthunthu pochotsa kulakwa kwanga,

Mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.

 

Ndithudi, Inu mumakonda mtima woona.

 

Ndithudi Inu mumakonda mtima woona,

Choncho Mundiphunzitse nzeru zanu,

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzakhala woyera.

 

Ndithudi, Inu mumakonda mtima woona.

 

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu,

Mulimbitse mwa ine mtima womvera,

Pamenepo ochimwa ndidzawaphunzitsa njira zanu,

Ndipo iwo adzabwerera kwa Inu.

 

Ndithudi, Inu mumakonda mtima woona.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA KWA AHEBRI: AHEBRI 05: 07 – 09. (Adaphunzira kumvera pakumva zowawa. Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha).

 

Yesu, pa nthawi imene anali munthu pansi pano, mofuula ndi molira misozi, adapereka mapemphero ndi madandaulo kwa Mulungu, amene anali nazo mphamvu zompulumutsa ku imfa. Ndiye popeza kuti Yesu adaadzipereka modzichepetsa, Mulungu adamvera mapemphero ake. Motero Yesu, ngakhale anali mwana wa Mulungu, adaphunzira kumvera pakumva zowawa. Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Ngati munthu anditumikira Ine, anditsatire,

Motero kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Munthu akanditumikira Ine, Atate anga adzamlemekeza.Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 12: 20 – 30. (Mbeu ya tirigu imakhalabe imodzi yomweyo ngati siigwa m’nthaka nkufa. Koma ikafa, imabala zipatso zambiri).

 

Panali Agriki ena pakati pa anthu amene adaakapembedza pa chikondwererocho. Iwowo adapita kwa Filipo, amene kwao kunali ku Betsaida wa ku Galileya, nakampempha kuti, “pepani bambo, timati tidzaone Yesu.” Filipo adakauza Andrea, ndipo Andrea pamodzi ndi Filipoyo adakauza Yesu. Yesu adati, “yafika nthawi yoti Mwana wa Munthu alandire ulemerero wake. Kunena zoona, mbeu ya tirigu imakhalabe imodzi yomweyo ngati siigwa m’nthaka nkufa. Koma ikafa, imabala zipatso zambiri. Munthu amene amakonda moyo wake, adzautaya, koma amene saikapo mtima pa moyo wake pansi pano, adzausungira ku moyo wosatha. Ngati munthu anditumikira Ine, anditsatire, motero kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Munthu akanditumikira Ine, Atate anga adzamlemekeza. Tsopano mtima wanga wavutika. Nanga ndinene chiyani? Kodi ndinene kuti, ‘Atate, mundipulumutse ku nthawi iyi?’ Iyai, kwenikweni ndidadzera nthawi imeneyi. Atate, onetsani ulemerero wa dzina lanu.” Pamenepo kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “ndauwonetsa ulemererowo ndipo ndidzauwonetsanso.” Panali khamu la anthu pamenepo. Tsono pamene adamva mauwo, adati, “kwagunda bingu.” Koma ena adati, “Mngelo walankhula naye.” Yesu adawauza kuti, “Mauwa amveka osati chifukwa cha Ine ayi, koma chifukwa cha inu.”

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Pamodzi ndi Yesu Khristu wansembe wamkulu, tipemphe Atate athu a Kumwamba amene ali ndi mphamvu zakutipulumutsa ku zoipa:

 

1.     Atate, mulimbikitse atsogoleri a Mpingo kuti asaope kusaukira akhristu ao powalondoloza pa njira ya chipulumutso.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Atate, muthandize anthu odwala ndi onse omva zowawa kuti asataye mtima, koma adziwe kupirira mavuto ao molumikizana ndi Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Atate, muunikire akatekumeni amene adzabatizidwa pa Pasaka, kuti adzipereke ndi mtima wonse ndi kumatsatira Yesu Khristu mokhulupirika.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Atate mudzutse akhristu ofooka ndi akugwa, kuti abwerere kwa Mpulumutsi wao ndipo ayambenso kubereka zipatso mu Mpingo mwanu.
Tikupemphani, mutivomereze.

5.     Atate, mutidalitse ife tomwe, kuti tiphathane ndi Yesu Khristu ndi kukondana naye kotheratu, pa masiku omwe ano odikira Pasaka.

Tikupemphani, mutivomereze.

Atate, popeza kuti Mwana wanu adagonja modzipereka, mudamvera mapemphero ake. Tsono tikukupemphani, mutivomereze chifukwa cha chifundo cha Yesu Khristu Ambuye athu.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...