LAMULUNGU LA KANJEDZA – B.
“Adapita ndi Yesu kuti akampachike.”
MTHENGA WABWINO (KU M’DIPITI): MAWU A MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 11: 01 – 10. (Ngwodala amene alikudza m’dzina la Ambuye).
Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankayandikira ku Yerusalemu, kufupi ndi ku Betefage ndi Betaniya, midzi ya phiri la Olivi, Iye adatuma awiri mwa ophunzirawo, nawauza kuti, “pitani m’mudzi mukuwonawo. Mukangolowamo, mukapeza mwana wa bulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule nkubwera naye. Wina akakakufunsani kuti, ‘inu, nchiyani chimenecho?’ Inu mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito, akangothana naye amtumiza konkuno nthawi yomweyo.’” Ophunzira aja adapitadi, nakapeza mwanawabuluyo ali chimangire pa khomo m’mbali mwa mseu, ndipo adayamba kummasula. Anthu amene adaali pamenepo adawafunsa kuti, “inu nchiyani chimenecho, buluyo mukummasuliranji?” Ophunzirawo adawayankha monga momwe adaawauzira Yesu. Tsono anthuwo adawalola kuti ammasule. Ophunzira aja adabwera naye mwanawabuluyo kwa Yesu. Adayala zovala zao mu mseu, ena nkumayalika nthambi zamasamba zomwe ankakazithyola ku thengo. Anthu amene adaali patsogolo, ndi amene adaali m’mbuyo, adayamba kufuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu. Ngwodala amene alikudza m’dzina la Ambuye. Udalitsidwe Ufumu wa atate athu Davide umene ulikudza tsopano. Ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
Mthenga wa Ambuye.......Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
---------------------------------------
MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA M’NENERI YESAYA: YESAYA 50: 04 – 07. (Sindidawabisire nkhope ondinyoza. Ndikudziwa kuti Chauta sadzandichititsa manyazi).
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziwe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M’mawa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira. Ambuye Chauta anditsekula makutu, ndipo sindidawanyoze kapena kuwapandukira. Ndidaperekera msana wanga kwa ondimenya, ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu. Sindidawabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu. Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziwa kuti sadzandichititsa manyazi.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 22: 08 – 09, 17 – 20, 23 – 24.
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
Onse ondiwona amandiseka,
Amandikwenzulira ndi kupukusa mitu yao,
Amati, “unkadalira Chauta, Chauta yemweyo akupulumutse,
Akulanditsetu tsono, popeza kuti amakukonda.”
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
Anthu ankhanza andizinga ngati mimbulu,
Aboola manja anga ndi mapazi anga,
Mafupa anga akuwonekera, koma anthu aja akungondiyang’anitsitsa,
Akukondwera poona kuti ndikuvutika.
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
Agawana zovala zanga, ndipo achitira malaya anga maere,
Koma Inu Chauta musakhale kutali,
Inu, mphamvu zanga, fulumirani kudzandithandiza.
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu,
Ndidzatamanda dzina lanu pa msonkhano wa anthu anu,
Ndidzati, “Inu omvera Chauta, mtamandeni Iye,
Inu nonse ana a Yakobe mlemekezeni Iye,
Ino nonse ana a Israele, mchitireni Iye ulemu.”
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A MKALATA YA FILIPI: FILIPI 02: 06 – 11. (Ali munthu choncho adadzichepetsa, koma Mulungu adamkweza kopambana).
Abale, Yesu Khristu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadaone kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphawi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lililonse. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza. Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – AFILIPI 02: 08 – 09.
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Ambuye, adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Nchifukwa chake chimene Mulungu adamkweza kopambana nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: KUSAUKA KWA YESU KHRISTU AMBUYE ATHU MONGA ADALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 14: 01 – 15:47.
W – Wowerenga; Y – Yesu; M – Munthu; A – Anthu ena.
01. ATSOGOLERI A AYUDA ADAPANGANA ZA KUPHA YESU.
W. Kudangotsala masiku awiri kuti chifike chikondwerero cha Pasaka ndi chikondwerero cha masiku odya buledi wosafufumitsa. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti amgwirire Yesu mochenjera, nkumupha. Koma ankati:
A: Zimenezi tisadzachite pa nthawi ya chikondwerero, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.
W. Tsiku lina Yesu anali ku Betaniya, m’nyumba ya Simoni wotchedwa Wakhate. Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta enieni onunkhira, amtengowapatali, a mtundu wa narido. Maiyo adaphwanya nsupa ija, nayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu. Anthu ena pamenepo adaipidwa nazo nanena kuti:
A: “Chifukwa chiyani kuwasakaza mafuta onunkhirawa? Ndithu mafuta amenewa akadatha kuwagulitsa, pa mtengo wopitilira ndalama zasiliva mazana atatu, kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?”
W: Choncho anthuwo adamupsera mtima mai uja. Koma Yesu adati:
Y: “Mlekeni maiyu, mukumuvutiranji kodi? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri. Anthu osauka muli nawo nthawi zonse, kotero kuti pamene mufuna kuwachitira zachifundo, mungathe kuwachitira. Koma Ine simudzakhala nane nthawi zonse. Iyeyu wachita zimene akadatha kuchita. Wadzozeratu thupi langa ndi mafuta onunkhira, kuti alikonzeretu lisanaikidwe m’manda. Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwino pa dziko lonse lapansi, azidzafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.”
W: Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi awiri aja, adapita kwa akulu a ansembe kuti akapereke Yesu kwa iwo. Pamene iwo adamva zimenezi adakondwa, ndipo adamlonjeza kuti adzampatsa ndalama. Iyeyo tsono adayamba kufunafuna mpata kwa iwo.
Nyimbo
02: YESU ADACHITA OHWANDO LA PASAKA NAPANGA UKARISTIA.
W: Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Pasaka, ophunzira a Yesu adafunsa kuti:
A: Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Pasaka?
W: Yesu adatuma awiri mwa ophunzira ake, nawauza kuti:
Y: Pitani m’mudzimu. Mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire. Kunyumba kumene ati akalowe, mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda cha alendo choti Iwowo adzadyeremo phwando la Pasaka ndi ophunzira ao?’ Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham’mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M’menemo mukatikonzere chakudya.
W: Ophunzira aja adanyamuka nalowa mumzindamo. Adachipezadi monga momwe Yesu adaawauzira, ndipo adakonza za phwando la Pasaka. Kutada, Yesu adabwera ndi ophunzira ake khumi ndi awiri aja. Onse atakhala pansi nkumadya, Yesu adati:
Y: Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu, mnzanga wodya nane, andipereka kwa adani anga.
W: Ophunzirawo adamva chisoni, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti:
M: Monga nkukhala ine?
W: Yesu adawayankha kuti:
Y: Ndi wina ndithu mwa khumi ndi awirinu, yemwe akususa mkate m’mbalemu pamodzi ndi ine. Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthu. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.
W: Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati:
K: Kwayani, ili ndi thupi langa.
W: Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu, nkuchipereka kwa ophunzirawo, namwa onse. Ndipo adawauza kuti:
Y: Awa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi amenewa ndiwakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka. Kunena zoona, sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.
W: Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi. Pambuyo pake Yesu adauza ophunzira ake kuti:
Y: Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya. Paja Malembo akuti, ‘ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa zidzangoti balala.’ Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.
W: Petro adati:
M: Ngakhale onse akhumudwe nkukusiyani, ine ndekha ai.
W: Yesu adamuuza kuti:
Y: Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe usiku womwe uno, tambala asanalire kachiwiri, ukakhala utandikana katatu kuti Ine sundidziwa.
W: Apo Petro adanenetsanso kuti:
M: Ngakhale atati andiphere nanu kumodzi, ine sindingakukaneni konse kuti sindikudziwani.
W: Ophunzira ena onse aja nawonso adanena chimodzimodzi.
Nyimbo
03: YESU ADAKAPEMPHERA KU MUNDA WA GETSEMANI.
W: Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena, otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti:
Y: Inu bakhalani pano, Ine ndikukapemphera.
W: Adatengako Petro, Yakobo ndi Yohane. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima. Adawauza kuti:
Y: Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, koma mukhale masotu.
W: Adapita patsogolo pang’ono, nadzigwetsa pansi, nayamba kupemphera. Adati:
Y: Ngati nkotheka nthawi yoopsa ino indipitirire.
W: Adanenanso kuti:
Y: Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.
W: Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, nawapeza ali m’tulo. Tsono adafunsa Petro kuti:
Y: Simoni, uli m’tulo kodi iwe? Mongadi walephera kukhala maso ndi kanthawi kochepa komwe? Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m’zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.
W: Adachokanso nakapemphera ndi mau omwe aja. Pamene adabwerakonso, adawapeza ali m’tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera ndi tulo. Choncho iwowo adasowa choyankha. Pamene adabwerako kachitatu, adati:
Y: Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Basi tsopano. Nthawi ija yafika, Mwana wa Munthu akuperekedwa kwa anthu ochimwa. Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.
W: Yesu akulankhula choncho, nthawi yomweyo wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi awiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adawatuma ndi akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda. Wodzampereka uja anali atawauza chizindikiro kuti:
M: Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo. Mukamgwire nkupita naye, osamtaya.
W: Pamene Yudasi adabwera, adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti:
M: Aphunzitsi.
W: Atatero adamumpsompsona. Apo anthu aja adamugwira Yesu. Koma wina mwa ophunzira amene anali naye pamenepo, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu. Tsono Yesu adawafunsa anthu aja kuti:
Y: Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigawenga? Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m’Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira. Koma izi zatere kuti zipherezere zomwe Malembo adanena.
W: Pamenepo ophunzira ake onse aja adathawa, kumsiya yekha. Mnyamata wina ankatsatira Yesu, atangofundira nsalu yokha, opanda chovala china. Anthu aja adaati amgwire, koma iye adaikolopola nsalu ija, nkuthawa ali maliseche.
Nyimbo
04: ANTHU AJA ADAPITA NDI YESU KU BWALO LA AYUDA.
W: Tsono anthu aja adapita naye Yesu kwa mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana onse akulu a ansembe, akulu a Ayuda, ndi aphunzitsi a Malamulo. Petro ankamutsatira Yesu chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, nkumaotha nao moto. Akulu a ansembe aja ndi onse a m’Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni woneneza Yesu kuti amuphe, koma osaupeza. Ambiritu ankamuneneza zabodza, koma umboni wao sunkagwirizana. Ena adaimirira nayamba kumneneza zabodza. Adati:
A: ‘Munthu uyu ife tidamumva akunena kuti, ‘Ine ndidzapasula Nyumba ya Mulunguyi, yomangidwa ndi anthu chabe, ndipo patapita masiku atatu ndidzamanga ina yosamangidwa ndi anthu.’
W: Koma ngakhale aponso zokamba zaozo sizinali zogwirizana. Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira pamaso pao, nafunsa Yesu kuti:
M: Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuwa akukunenezazi?
W: Yesu adangokhala chete, osayankha kanthu. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adafunsanso kuti:
M: Kodi ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu Wolemekezeka?
W: Yesu adayankha kuti:
Y: Inde, ndinedi. Ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu Wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.
W: Apo mkulu wa ansembe uja adang’amba zovala zake, nati:
M: Kodi pamenepa tikusowanso mboni zina? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku. Tsono mukuganiza bwanji?
W: Onse adagamula kuti ayenera kuphedwa. Ena adayamba kumthira malovu, namuphimba m’maso nkumamuwomba makofi, namanena kuti:
A: Lotatu, wakumenya ndani?
W: Alonda aja nawonso adayamba kumumenya. Petro anali kunsi pa bwalo. Mtsikana wina, wantchito wa mkulu wa ansembe onse, adafika pomwepo. Ataona Petro akuwotha moto, adamuyang’anitsitsa, nati:
M: Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.
W: Koma Petro adakana, adati:
W: Zimenezo ine sindikuzidziwa, sindikuzimvetsa konse.
W: Ndipo adatuluka kumapita cha ku chipata. Pamenepo tambala adalira. Koma m’tsikana uja adamuwona, nayambanso kuuza amene anali pamenepo kuti:
M: Akulu amenewa anali m’gulu lomweli.
W: Koma Petro adakananso, patangopita kanthawi anthu amene adaali pamenepo adamuuza Petro kuti:
A: Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomwelo. Kodi kwanu si ku Galileya iwe?
W: Koma Petro adayamba kudzitemberera nkumalumbira kuti:
M: Mtheradi, munthu amene mukunenayu ine sindimdziwa.
W: Nthawi yomweyo tambala adalira kachiwiri. Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti: “Tambala asanalire kawiri, ukhala utakana katatu kuti sundidziwa.” Pomwepo Petro adayamba kulira misozi.
Nyimbo
05: AKULU A AYUDA ADAKATULA KWA PILATO.
W: M’mawa kutangocha, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi aphunzitsi a Malamulo, pamodzi ndi ena onse a m’Bwalo Lalikulu la Ayuda adapanga upo. Adammanga Yesu napita naye kwa Pilato. Pilatoyo adafunsa Yesu kuti:
M: Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?
W: Yesu adamuyankha kuti:
Y: Mwanena nokha.
W: Akulu a ansembe aja adayamba kumneneza zambiri. Pilato adamufunsanso kuti:
M: Kodi ulibe poyankha? Ona zonse zimene akukunenezazi.
W: Koma Yesu sadayankhenso kanthu, kotero kuti Pilato adadabwa. Pa nthawi ya chikondwelero cha Pasaka, bwanamkubwa ankawamasulira mkaidi mmodzi, yemwe Ayudawo ankapempha. Panali munthu wina, dzina lake Barabasi, amene anali m’ndende pamodzi ndi anthu ena chifukwa choukira Boma ndi kupha anthu. Tsono chikhamu cha anthu chidabwera, nkuyamba kupempha Pilato kuti awachitire zomwe adaazolowera. Pilato adawafunsa kuti:
M: Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayudayi?
W: Adatero chifukwa adaadziwa kuti Yesuyo akulu a ansembewo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe. Koma akulu ansembewo adasonkhezera anthu onse aja kuti apemphe kuwamasulira Barabasi. Tsono Pilato adawafunsanso kuti:
M: Nanga tsono mukuti ndichite naye chiyani uyu amene mukuti ndi Mfumu ya Ayudayu?
W: Anthuwo adafuula kuti:
A: Mpachikeni pa mtanda!
W: Pilato adawafunsa kuti:
M: Adalakwanji?
W: Koma iwo adafuula koposa kuti:
A: Mpachikeni pa mtanda!
W: Choncho Pilato, pofuna kukondwetsa anthuwo, adawamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda. Pamenepo asilikali adalowetsa Yesu m’bwalo, kunyumba kwa bwanamkumbwa, nasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao. Adamuveka chovala chofiirira, naluka nsangamutu yaminga nkuiika pamutu pake. Kenaka adayamba kumampatsa moni kuti:
A: Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.
W: Ankamumenya m’mutu ndi ndodo, namamthira malovu, nkumamugwadira monyodola. Atasewera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija, namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda.
Nyimbo
06: ASIRIKALI ADAPITA NAYE KU GOLOGOTA KUTI AKAMPACHIKE PA MTANDA.
W: Pa njira adakumana ndi munthu wina, amene ankadutsa pamenepo kuchokera ku midzi. Munthuyo anali Simoni wa ku Kirene, bambo wake wa Aleksandro ndi Rufu. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu. Iwowo adapita naye Yesuyo ku malo otchedwa Gologota, (ndiye kuti, “Malo a Chibade cha Mutu.”) Adaafuna kumpatsa vinyo wosanganiza ndi mure kuti amwe, koma Iye adakana. Atampachika pa mtanda, adagawana zovala zake. Adaachita maere kuti aone zimene aliyense atenge. Pamene adampachika pa mtanda, nkuti nthawi ili 9 Koloko m’mawa. Mau osonyeza mlandu womuphera, adaawalemba motere, “Mfumu ya Ayuda.” Pamodzi ndi Yesu adaapachikanso pa mitanda zigawenga ziwiri, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. Motero zidachitikadi zimene mau a Mulungu adanena kuti, “Adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo.” Anthu amene ankadutsa pamenepo ankamunyodola. Ankapukusa mitu nkumanena kuti:
A: Ha, suja iwe unkati, ‘Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu?’ Tadzipulumutsatu, tsika pamtandapo!
W: Nawonso akulu a ansembe ankamuseka, nkumauzana ndi aphunzitsi a Malamulo kuti:
A: Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye yemwe! Uja ankati ndi Mpulumutsi wolonjezedwayu, Mfumu ya Aisraele, atatsikatu tsopano pamtandapa, kuti tiwone ndi kumkhulupirira! Ndiponso amene adawapachika pamodzi naye aja ankamunyoza.
W: Nthawi itakwana 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko. Tsono nthawi ili 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti:
Y: Eloi, Eloi, lama sabakatani?
W: Ndiye kuti:
Y: Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?
W: Atamva mauwo, ena amene adaimirira pamenepo adati:
A: Tamverani, akuitana Eliya.
W: Motero wina adathamanga nakaviika chinkhupule m’vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe. Anzake wo adati:
M: Taima, tiwone ngati Eliyayo abweredi kudzamtsitsa.
W: Koma Yesu adafuula kwakukulu, natsirizika.
Onse agwade ndikukhala chete kwa kanthawi.
Chinsalu chotchinga chija cha m’Nyumba ya Mulungu chidang’ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Mkulu wa asilikali amene adaaimirira pomwepo kuyang’ana naye, ataona Yesu watsirizika akufuula chotere, adati:
M: Ndithudi, munthuyo adaalidi Mwana wa Mulungu. Patali poteropo padaali azimayi, akungoyang’anitsitsa. Ena mwa iwo anali Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobo wamng’ono uja ndi wa Yosefe, ndiponso Salome. Azimaiwa ankatsata Yesu pamene Iye anali ku Galileya, ndi kumamtumikira. Padalinso azimayi ena ambiri omwe adaabwera naye ku Yerusalemuko. Tsopano chisisira chinali chitagwa. Ndiye popeza kuti linali Lachisanu, tsiku lokonzekera Sabata, Yosefe wa ku Arimatea adafika. Adaali mkulu wodziwika ndithu, wa m’Bwalo Lalikulu la Ayuda. Nayenso ankayembekeza Ufumu wa Mulungu. Tsono iye adalimba mtima, napita kwa Pilato kukapempha kuti ampatsire mtembo wa Yesu. Pilato adadabwa kumva kuti Yesu wafa kale. Choncho adaitanitsa mkulu wa asilikali uja, anamfunsa kuti:
M: Kodi Yesu wafa kaledi?
W: Mkulu wa asilikaliyo atavomera, Pilato adamlola Yosefe kuti atenge mtembowo. Yosefeyo adagula nsalu yoyera yabafuta, natsitsa mtembo uja nkuukuta ndi nsaluyo. Adauika m’manda ochita chosema m’thanthwe, kenaka adagubuduzira chimwala pa khomo kutseka pamandapo. Maria uja wa ku Magadala, ndi Maria mai wa Yosefe, ankaona kumene Adamuika Yesu.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, poona umo Yesu adasaukira chifukwa cha ife, tikuzindikira kuti chikondi cha Mulungu ndi chozama kwambiri. Tiyeni, tipempherere anthu onse:
1. Akulu a Eklezia akhale a mtima wodzichepetsa: kuti athe kulamulira anthu ao moyenerera.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akulu olamulira maiko nawonso akhale a mtima wodzichepetsa: kuti athe kulamulira anthu ao moyenera.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Akhristu ndi akatekumeni a Parishi yathu ino, agwirizane pakukhala odzichepetsa, ndipo athe kutembenuza akunja ndi chitsanzo chao chabwino.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Makolo a ana ayesetse kulera bwino ana ao, pakuwapatsa zitsanzo zokoma ndi maphunzitso oyenera, kukokera anawo ku ntchito za Mulungu.
Tikupemphani, mutivomereze.
5. Ifeyo mutipatse chikondi, Atate, kuti pamene anzathu atichitira zoipa, tisawabwereze konse; choncho anzathu adzatha kutembenuka mtima.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, mwa chifundo chanu tcherani makutu ndi kutimvera ife amene tikukupemphani modzichepetsa. Mwa Yesu Khristu Ambuye Athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment