“Azatipulumutsa mwa chifundo chake.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LACHIWIRI LA MBIRI: 02 MBIRI 36: 14 – 16, 19 – 23. (Chauta adakwiyira anthu ake, ndipo panalibenso mankhwala ochiritsa).
Atsogoleri onse a ansembe, pamodzi ndi anthu omwe, adachita zosakhulupirika zambirimbiri potsata zoipa za mitundu ina ya anthu. Adaipitsa Nyumba ya Chauta imene Chautayo anali ataipatula kuti ikhale yake ku Yerusalemu. Chauta, Mulungu wa makolo ao, ankawatumira amithenga kawirikawiri, chifukwa chakuti ankawamvera chifundo anthu ake ndi makolo ake amene Iye ankakhala. Koma anthuwo ankapeputsabe amithengawo, namanyoza mau a Mulungu. Ndipo ankawaseka aneneri ake, mpaka Chauta adakwiyira anthu ake, ndipo panalibenso mankhwala ochiritsa. Ankhondo a ku Babiloni adatentha Nyumba ya Chauta, nagwetsa linga lonse la Yerusalemu. Adatenthanso nyumba zonse zaufumu, naononga ziwiya zonse zamtengowapatali. Anthu amene adapulumuka ku lupanga, adawatenga ukapolo kupita nawo ku Babiloni. Kumeneko adasanduka anthu oitumikira mfumuyo ndi ana ake, mpaka ufumu wa Persiya utakhazikitsidwa, kuti zipherezere zimene Chauta adaalankhula kudzera mwa Yeremiya, zakuti, dzikoli lidzakhala lopasuka kwa zaka 70, kuti masabata opuma amene sanachitike, akwaniritsidwe. Tsono chaka choyamba cha ufumu wa Kirusi, mfumu ya ku Persiya, Chauta adautsa mtima wa Kirusiyo, kuti alengeze ku maiko onse a ufumu wake mpaka kulemba kumene. Adachita choncho kuti zimene Chauta adaalankhula kudzera mwa Yeremiya zipherezere. Adati, “Kirusi, mfumu ya ku Persiya, akunena kuti, ‘Chauta Mulungu wakumwamba, wandipatsa ine maufumu onse pa dziko lapansi. Ndipo wandilamula kuti ndimmangire Nyumba ku Yerusalemu, ku Yuda. Aliyense mwa inu nonse amene ali munthu wa Chauta, Chauta Mulungu wakeyo akhale naye. Ndipo apite.’”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 137: 01 – 06.
Lilime langa likangamire ku mnakanaka m’kamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe.
M’mbali mwa mitsinje ya ku Babiloni,
Kumeneko tidakhala pansi nkumalira tikukumbukira Ziyoni,
Kumeneko tidapachika apangwe athu,
Pa mitengo ya misondodzi.
Lilime langa likangamire ku mnakanaka m’kamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe.
Kumeneko anthu otigwira ukapolo adatipempha,
Kuti tiimbe nyimbo,
Otizunza adatipempha kuti tisangalale,
Adati, “tatiimbiraniko nyimbo ya ku Ziyoni.”
Lilime langa likangamire ku mnakanaka m’kamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe.
Tsono ife tidati, “tingaimbe bwanji nyimbo ya Chauta,
Kuchilendo ngati kuno?”
Ndikakuiwala iwe Yerusalemu,
Dzanja langa lamanja liwume.
Lilime langa likangamire ku mnakanaka m’kamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe.
Lilime langa likangamire,
Ku mnakanaka m’kamwa mwanga,
Ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu,
Ndi kukuwona kuti ndiwe wondisangalatsa kwambiri.
Lilime langa likangamire ku mnakanaka m’kamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AEFESO: AEFESO 02: 04 – 10. (Pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu…kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudzakupulumutsani).
Abale, Mulungu ndi wachifundo chachikulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana. Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani. Popeza kuti tili mwa Khristu Yesu, Mulungu adachita ngati kutiwukitsa kwa akufa pamodzi naye, kuti choncho atipatse malo aulemu pamodzi naye m’dziko la Kumwamba. Adachita zimenezi kuti mwa chifundo chake chimene adatichitira mwa Khristu Yesu, aonetse kwa nthawi zonse zam’tsogolo kuti ngwokomadi mtima kopambana. Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ayi, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade. Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichita.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – YOHANE 03: 16.
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Mulungutu adawakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, Komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, Koma akhale ndi moyo wosatha. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 03: 14 – 21. (Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzawapulumutse).
Panthawi yomweyo, Yesu adati kwa Nikodemo, “monga momwe Mose adaapachikira njoka pa mtengo m’chipululu muja, momwemonso Mwana wa Munthu ayenera kudzapachikidwa, kuti aliyense wokhulupirira akhale ndi moyo wosatha mwa Iye. Mulungutu adawakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzawapulumutse. Munthu wokhulupirira Mwanayo, sazengedwa mlandu. Koma wosakhulupirira, wazengedwa kale, chifukwa sadakhulupirire Mwana mmodzi yekha uja wa Mulungu. Mlandu wake ndi uwu wakuti ngakhale kuwala kudadza pansi pano, anthu adakonda mdima, osati kuwalako, chifukwa zochita zao zinali zoipa. Aliyense wochita zoipa, amadana ndi kuwala. Saonekera poyera, kuwopa kuti zochita zakezo zingaonekere. Koma wochita zokhulupirika amaonekera poyera, ndipo zochita zake zimadziwika kuti wazichita momvera Mulungu.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, mwa Yesu Khristu, Mulungu adatiwonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse. Tsono tiyeni tipempherere mogwirizana ndi mosakayika:
1. Ansembe ndi atsogoleri a Mpingo aongolere anthu ao m’njira ya kulapa, pakuwasonyeza chifundo cha Mulungu chofuna kuwapulumutsa.
Tiwonetseni kukoma mtima kwanu, Ambuye.
2. Akhristu ofooka ndi otayika atembenukire kwa Yesu Khristu ndi mtima wolapa, poyang’anira mtanda umene Iye adapachikidwapo.
Tiwonetseni kukoma mtima kwanu, Ambuye.
3. Akatekumeni nawonso aphunzire kulapa ndi kusintha moyo wao, pozindikira chikondi chachikulu chomwe Yesu Khristu adawakonda nacho.
Tiwonetseni kukoma mtima kwanu, Ambuye.
4. Ife tonse a m’Parishi yathu ino tilimbikire kuchita ntchito zabwino pa nthawi ino ya Lenti, kusonyeza kuti tayambadi moyo watsopano.
Tiwonetseni kukoma mtima kwanu, Ambuye.
Atate, tikuyamika chifundo chanu chosasimbika, mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment