Saturday, March 2, 2024

LAMULUNGU LA 03 MUNYENGO YA LENTI – B.

LAMULUNGU LA 03 MUNYENGO YA LENTI – B

“Mungationetse chizindikiro Chotani?”

 

MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA EKSODO: EKSODO 20: 01 -17. (Malamulo a Mulungu anaperekedwa kudzera mwa Mose).

 

Mulungu adalankhula mau onsewa, adati, “Ine ndine Chauta Mulungu wako, amene ndidakutulutsa mu ukapolo ku dziko la Ejipito. “Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha. “Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m’madzi a pansi pa dziko. Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai. Komatu anthu ambirimbiri a mibadwo yosawerengeka amene amandikonda, namatsata malamulo anga, ndimawakonda ndi chikondi chosasinthika. “Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Mulungu yo sadzamleka aliyense wotchula pachabe dzina lakelo. “Uzikumbukira tsiku la sabata, uzilisunga loyera. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito zako zonse. Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoweta zako, kapena mlendo amene amakhala m’mudzi mwako. Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam’menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera. “Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m’dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.

“Usaphe.”

“Usachite chigololo.”

“Usabe.”

“Usachite umboni womnamizira mnzako.”

“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mzako.”

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

---------------------------------------

 

NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 19: 07 – 10.

 

Inu, Mulungu, uthenga wanu ndi wopatsa moyo.

 

Mau a Chauta ngangwiro,

Amapatsa munthu moyo watsopano.

Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika,

Umawapatsa nzeru amene alibe.

 

Inu, Mulungu, uthenga wanu ndi wopatsa moyo.

 

Malangizo a Chauta ndi olungama,

Amasangalatsa mtima.

Malamulo a Chauta ndi olungama,

Amapatsa mtima womvetsa.

 

Inu, Mulungu, uthenga wanu ndi wopatsa moyo.

 

Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro,

Chimakhala mpaka muyaya,

Chiweruzo cha Chauta nchoona,

Ncholungama nthawi zonse.

 

Inu, Mulungu, uthenga wanu ndi wopatsa moyo.

 

Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide,

Ngakhale golide wambiri wamtengowapatali,

Nzotsekemera kupambana uchi,

Ngakhale uchi wozuna kwambiri.

 

Inu, Mulungu, uthenga wanu ndi wopatsa moyo.

------------------------------------------------

 

MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 01: 22 – 25. (Ife timalalika Khristu amene adapachikidwa pa mtanda…. mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru ya Mulungu).

 

Abale, Ayuda amafuna kuwona zozizwitsa, pamene Agriki amafunafuna nzeru. Koma ife timalalika Khristu amene adapachikidwa pa mtanda. Kwa Ayuda mau amenewa ndi okhumudwitsa, pamene kwa anthu a mitundu ina mauwa ndi opusa. Koma amene Mulungu adawaitana, kaya ndi Ayuda kaya ndi Agriki, onsewo amazindikira kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru ya Mulungu. Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu.

 

Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.

--------------------------------------

 

NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 17:05.

 

Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso wowapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.

--------------------------------------

 

MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA YOHANE WOYERA: YOHANE 02: 13 – 25. (Gwetsani nyumba ya Mulungu ino, Ine ndidzaimanganso masiku atatu).

 

Itayandikira nthawi ya Pasaka, chikondwerero cha Ayuda, Yesu adanyamuka kupita ku Yerusalemu. Kumeneko adalowa m’Nyumba ya Mulungu napezamo anthu akugulitsa ng’ombe, nkhosa ndi nkhunda. Munalinso anthu osinthitsa ndalama. Apo Yesu adapanga mkwapulo wazingwe nayamba kuwatulutsira onse kunja, pamodzi ndi nkhosa ndi ng’ombe zao zomwe. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama aja, nawamwazira ndalama zao. Ndipo adalamula ogulitsa nkhunda aja kuti, “izi zitulutseni muno. Nyumba ya Atate anga musaisandutse nyumba yochitiramo malonda.” Ophunzira ake adakumbukira Malembo aja akuti, “changu chomwe ndimachitira nyumba yanu chidzandiphetsa.” Pamenepo akuluakulu a Ayuda adamufunsa kuti, “kodi mungatiwonetse chizindikiro chotani chakuti muli ndi ulamuliro wochitira zimenezi?” Yesu adawayankha kuti, “Gwetsani nyumba ya Mulungu ino, ine ndidzaimanganso masiku atatu.” Apo iwo adati, “Nyumba ya Mulunguyi idatenga zaka 46 kuti aimange, tsono Inu nkuimanga masiku atatu chabe?” Koma Yesu ankanena za thupi lake mophiphiritsa, pamene adatchula Nyumba ya Mulungu. Iye atauka kwa akufa, ophunzira ake adadzakumbukira kuti adanena zimenezi, nakhulupirira Malembo ndiponso mau amene Yesu adaanenawo. Pamene Yesu anali m’Yerusalemu pa chikondwerero cha Paska, anthu ambiri adayamba kuika chikhulupiriro chao pa Iye, poona zozizwitsa zimene ankachita. Koma Yesu sadaikepo chikhulupiriro pa iwowo, popeza kuti Iye ankawadziwa anthu onse. Sankalira kuti wina achite chomuuza za munthu aliyense. Pakuti mwiniwakeyo ankadziwa za m’mitima mwa anthu.

 

Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.

--------------------------------------

 

Mapemphero a Akhristu.

 

Abale, pakuti Yesu Khristu ali nafe mommuno, tiyeni titembenukire kwa Mulungu ndi kupempha madalitso ake mokhulupirira:

 

1.     Eklezia apitirize ntchito yake younikira anthu onse powasonyeza chifundo cha Mulungu chofuna kuwapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.

2.     Akulu olamulira maiko ayendetse anthu ao m’njira ya mtendere ndi chilungamo potsata malamulo ochokera kwa Mulungu Mwini.
Tikupemphani, mutivomereze.

3.     Akatekumeni akhale ndi chikhulupiriro cholimba potsata Yesu Khristu, mpaka nawonso adzasanduke ana a Mulungu polandira ubatizo.
Tikupemphani, mutivomereze.

4.     Ife tomwe timange moyo wathu pa Yesu Khristu, ndipo timtsimikizire Iye chikondi chathu pakusunga bwino malamulo ake.
Tikupemphani, mutivomereze.

 

Atate, potula mapemphero athuwa m’manja mwanu, tikukuyamikani chifukwa mwatikhazikitsa m’chikhulupiriro chenicheni. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Amen.

 

#Pax_et_Gaudium_in_Domino.

Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295

Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/

No comments:

Post a Comment

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C

Chaka cha Ukaristia [Corpus Christi]—C “Muzichita zimenezi kuti mundikumbukire.”   MAWU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS (...