“Uyu ndi Mwana wanga amene ndimamukonda, mumumvere Iye.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 22: 01 – 02, 09 – 13, 15 – 18. (Lonjezo la Abrahamu, Tate wachikhulupiriro).
Pambuyo pake Mulungu adamuyesa Abrahamu. Adamuitana, adati, “Abrahamu!” Ndipo Abrahamu adayankha kuti, “Ee, Ambuye.” Mulungu adati, “tenga Isaki, mwana wako mmodzi yekha uja amene umamkonda kwambiri, upite ku dziko la Moriya. Kumeneko ukampereke ngati nsembe yopsereza pa phiri limene ndidzakuuza.” Atafika ku malo amene adamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo. Tsono adasolola mpeni kuti amuphe mwana wakeyo. Koma mngelo wa Chauta adamuitana kuchokera kumwamba, adati, “Abrahamu, Abrahamu!” Iye adayankha kuti, “Ee, Ambuye!” Mngeloyo adati, “usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziwa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo.” Abrahamu atayang’ana, adaona kuti pali nkhosa yamphongo yogwidwa nyanga zake m’ziyangoyango. Adapita kukaigwira, anaphia ngati nsembe yopsereza m’malo mwa mwana wake uja. Mngelo wa Chauta uja adamuitana Abrahamu kachiwiri kuchokera Kumwamba, adati, “Chauta akunena kuti, ‘ndikulumbira kuti ndidzakudalitsa kwambiri iwe chifukwa wachita zimenezo, osandimana mwana wako mmodzi yekha uja. Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zakumwamba, kapenanso ngati mchenga wa m’mbali mwa Nyanja. Zidzukulu zakozo zidzagonjetsa adani ao onse. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalandira madalitso kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa iwe wandimvera.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 116: 10, 15 – 19.
Ndidzayenda pamaso pa Chauta m’dziko la moyo.
Ndidakhulupirirabe ngakhale pamene ndinkati,
“Ndazunzika koopsa.”
Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta,
Ndi yamtengowapatali pamaso pake.
Ndidzayenda pamaso pa Chauta m’dziko la moyo.
Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni,
Inu mwamasula maunyolo anga,
Ndidzapereka kwa inu nsembe yothokozera,
Ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.
Ndidzayenda pamaso pa Chauta m’dziko la moyo.
Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta,
Pamaso pa anthu ake onse,
Ndidzadzipereka m’mabwalo a Nyumba ya Mulungu,
Mu mzinda wa Yerusalemu.
Ndidzayenda pamaso pa Chauta m’dziko la moyo.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YA PAULO WOYERA KWA AROMA: AROMA 08: 31b – 34. (Mulungu sadaumire ngakhale Mwana wakewake).
Abale, tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, angatsutsane nafe ndani? Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere? Ndani angawaimbe mlandu anthu amene Mulungu adawasankha? Mulungu mwini wake amawaona kuti ngolungama pamaso pake. Tsono palibe amene angawaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 17: 05.
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.” – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 09: 02 – 10. (Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda).
Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro ndi Yakobe ndi Yohane, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasintha iwo akuwona. Zovala zake zidasanduka zowala ndi zoyera kuti mbee, kupambana m’mene mmisiri wina aliyense angayeretsere nsalu pansi pano. Nthawi yomweyo ophunzira aja adaona Eliya ndi Mose, akukambirana ndi Yesu. Petro adauza Yesu kuti, “aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” Ankatero chifukwa chosowa chonena, pakuti iye ndi anzake aja anali atagwidwa ndi mantha aakulu. Tsono padafika mtambo, nuwaphimba, ndipo mumtambomo mudamveka mau akuti, “uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, muzimumvera.” Mwadzidzidzi ophunzirawo poyang’anayang’ana, adangoona kuti palibenso wina amene anali nawo pamenepo, koma Yesu yekha. Pamene ankatsika phirilo, Yesu adawaletsa kuti zimene adaaonazo asauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa. Iwo adasungadi chinsinsichi, koma ankafunsana okhaokha kuti, “kodi kuuka kwa akufa akunena Yesuku ndiye kuti chiyani?”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, pakuti Yesu alikutipempherera pokhala ku dzanja lamanja la Mulungu, tikweze mitima yathu kumwamba ndi kupempha chithandizo cha Ambuye:
1. Eklezia wa Mulungu akhale chizindikiro chosonyeza kuwala kwa Yesu Khristu kwa anthu a mafuko onse.
Tiwonetseni nkhope yanu Ambuye, ndipo tidzapulumuka.
2. Akhristu amene akuzunzika chifukwa cha Mthenga Wabwino alimbikire m’chikhulupiriro chao pophathana ndi Yesu Khristu.
Tiwonetseni nkhope yanu Ambuye, ndipo tidzapulumuka.
3. Apezeke anyamata ndi atsikana ambiri odzipereka ku ntchito ya Mulungu: asaope kupereka moyo wao ngati nsembe chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu.
Tiwonetseni nkhope yanu Ambuye, ndipo tidzapulumuka.
4. Ife tomwe tidziwe kulingalira m’mitima mwathu za masautso a Yesu Khristu pa nthawi ino ya Lenti, kuti timange moyo wathu pa chikondi chake.
Tiwonetseni nkhope yanu Ambuye, ndipo tidzapulumuka.
Atate, tikuyamika chifundo chanu, chifukwa simuleka kutipatsa zonse mwaulere, mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment