LAMULUNGU LA 01 MUNYENGO YA LENTI – B
“Tilape ndi kuyamba moyo watsopano.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA GENESIS: GENESIS 09: 08 – 15. (Tsopano ndikuchita nanu chipangano, pamodzi ndi zidzukulu zanu, ndi zamoyo zonse).
Mulungu adauza Nowa ndi ana ake kuti, “tsopano ndikuchita nanu chipangano, pamodzi ndi zidzukulu zanu, ndi zamoyo zonse, mbalame, zoweta, nyama zakuthengo, ndi zina zonse zimene zidatuluka nanu m’chombo. Chipanganocho ndi ichi: ‘ndikulonjeza kuti sindidzaononganso zamoyo zonse ndi chigumula. Ndithu chigumula sichidzaononganso dziko lapansi.’ Ndipo Mulungu adati, nachi chizindikiro cha chipangano chamuyaya chimene ndikuchiika pakati pa Ine ndi inu ndi cholengedwa chilichonse chimene chili ndi inu. Ndikuika utawaleza m’mitambo, ndipo udzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi dziko lapansi. Nthawi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga, ndipo pakuoneka utawaleza m’mitambomo, ndizidzakumbukira lonjezo langa limene ndidachita ndi inu ndi nyama zonse, kuti chigumula chisadzaonongenso zamoyo zonse.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 25: 04 – 09.
Njira zanu, Chauta, ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chanu.
Mundidziwitse njira zanu, Inu Chauta,
Mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu,
Munditsogolere m’choona chanu ndi kundilangiza,
Pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga.
Njira zanu, Chauta, ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chanu.
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu,
Ndi chikondi chanu chosasinthika,
Mundikomere mtima, Inu Chauta,
Chifukwa cha chikondi chanu.
Njira zanu, Chauta, ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chanu.
Chauta ndi wabwino ndi wolungama,
Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake,
Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama,
Amawaphunzitsa njira zake.
Njira zanu, Chauta, ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chanu.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PETRO WOYERA: 1 PETRO 03:18 – 22. (Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani).
Abale, Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m’malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo. Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m’ndende. Mizimuyi ndi ya anthu amene kale lija sadamvere pamene Mulungu adaadikira moleza mtima, pa nthawi imene Nowa ankapanga chombo. M’chombomo anthu owerengeka okha, asanu ndi atatu, adapulumuka ndi madzi. Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kumeneku si kuchotsedwa litsiro la m’thupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi mtima woona, kudzera mwa Yesu Khristu amene adapita Kumwamba, ndipo ali ku dzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko angelo ndi maulamuliro ndi zimphamvu zimamvera Iye.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – SALIMO 95: 08.
Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu. – Munthu sungakhale moyo ndi chakudya chokha, Koma ndi mau onse olankhula Mulungu. – Ulemerero ndi mayamiko kwa Inu, Khristu.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 01:12 – 15. (Yesuyo adakhala kumeneko masiku makumi anai, Satana anamuyesa, ndipo Angelo ankamutumikira).
Nthawi yomweyo Mzimu Woyera adapititsa Yesu ku chipululu. Yesuyo adakhala kumeneko masiku makumi anai, Satana akumuyesa. Komweko kunalinso nyama zakuthengo, ndipo angelo ankamutumikira. Yohane uja ataponyedwa m’ndende, Yesu adapita ku Galileya akulalika Uthenga Wabwino wonena za Mulungu. Ankati, “Nthawi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu.”
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati pa anthu. Tiyeni tipempherere anthu onse kuti alandire Mthenga Wabwino n’kuyambadi moyo watsopano.
1. Atsogoleri a Mpingo athandize anthu ao kuyenda m'njira ya ungwiro powaphunzitsa nzeru zolapira machimo.
Atate, mutikhululukire chifukwa tidakuchimwirani.
2. Akhristu ofooka adzidzimuke mumtima mwao pa nthawi ino ya Lenti, pokumbukira chifundo chozama cha Yesu Khristu Mpulumutsi.
Atate, mutikhululukire chifukwa tidakuchimwirani.
3. Akatekumeni nawonso ayesetse kusiya makhalidwe oipa n’kusanduka anthu atsopano poika chikhulupiriro chao chonse pa Yesu Khristu.
Atate, mutikhululukire chifukwa tidakuchimwirani.
4. Ife tomwe tilimbikire kuchita zolungama ndi kuwonetsa anthu onse mtima wachifundo, pokumbukira zomwe zija tidalonjeza pa ubatizo.
Atate, mutikhululukire chifukwa tidakuchimwirani.
Atate, mverani mapemphero athuwa ndipo mutiwongolere ndi Mzimu wanu Woyera, kuti ntchito zathu za nthawi ino ya Lenti zikhale zodzetsa ufumu wanu m'dziko lino lapansi. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
Blog: https://mkatolikamw.blogspot.com/
No comments:
Post a Comment