LAMULUNGU LA 05 PA CHAKA – B.
“Ndine watsoka ngati sindilalika Mthenga Wabwino.”
MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA YOBU: YOBU 07: 01 – 04, 06 – 07. (Sindigona tulo, ndimangoti sadabusadabu mpaka m’bandakucha).
Yobu adayamba kulankhula, adati: “moyo wa munthu pa dziko lapansi ndi wantchito yakalavulagaga. Masiku ake ali ngati a munthu waganyu. Paja kapolo amalakalaka mthunzi, wantchito amayembekezera malipiro ake, ndiye inenso ndimangovutika nthawi zonse. Ngakhale usiku ndimapezabe mavuto. Ndikamagona ndimafunsa kuti, kodi kucha liti? Koma usiku ndi wautali, sindigona tulo, ndimangoti sadabusadabu mpaka m’bandakucha. Masiku anga ndi othamanga kupambana makina oombera nsalu, amatha opanda chikhulupiliro chilichonse. Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya. Masiku abwino sindidzawaonanso.”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 147: 01 – 06.
Tamandani Chauta amene amachiritsa mitima yosweka.
Tamandani Chauta!
Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu,
Nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera.
Tamandani Chauta amene amachiritsa mitima yosweka.
Chauta akumanga Yerusalemu, akusonkhanitsa Aisraele omwazika,
Akuchiritsa a mtima wachisoni, ndipo akumanga mabala ao,
Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi, zonse amazitcha maina ake.
Tamandani Chauta amene amachiritsa mitima yosweka.
Mbuye wathu ndi wamkulu, ndipo ndi wa mphamvu zambiri,
Nzeru zake nzopanda malire,
Amakweza oponderezedwa, koma amagwetsa pansi anthu oipa.
Tamandani Chauta amene amachiritsa mitima yosweka.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 09: 16 – 19, 22 – 23. (Tsoka kwa ine ngati sindiulalika Uthenga Wabwinowo).
Abale, pamene ndikulalika Uthenga Wabwino, apo pokha palibe ponyadira ai, popeza kuti ndi Ambuye amene adachita kundilamula zimenezo. Tsoka kwa ine ngati sindiulalika Uthenga Wabwinowo. Ngatitu ndikugwira ntchitoyi mofuna ine ndekha, ndiye kuti ndilandirapo mphotho. Koma ngati ndiigwira mosafuna ine dekha, ndiye kuti ntchitoyo ndi udindo umene Ambuye adandipatsa. Pamenepo tsono mphotho yanga ndi yotani? Mphotho yanga ndi yakuti ndikamalalika Uthenga Wabwino, ndizingoulalika mwaulere, osafuna kulandirapo malipiro aja amene ndikadayenera kulandira polalika Uthenga Wabwinowo.Ndine mfulu, osati kapolo wa munthu wina aliyense ai, komabe ndidadzisandutsa kapolo wa anthu onse, kuti ndikope anthu ambiri. Kwa amene ali ndi chikhulupiriro chofooka, ndidakhala ngati wachikhulupiriro chofooka, kuti ndiwakope ofookawo. Kwa anthu onse ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ngati nkotheka ndikope ena mwa iwo. Zonsezi ndimazichita chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti inenso ndilandire nao madalitso a Uthengawo.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 08:17.
Alleluia, Alleluia – Iye adatenga zofooka zathu, adasenza nthenda zathu. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 01: 29 – 39. (Yesu adachiritsa ambiri amene ankavutika ndi matenda osiyanasiyana).
Pa nthawi yomweyo, Yesu adachoka ku nyumba yamapemphero kuja, nakalowa pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane m’nyumba ya Simoni ndi Andrea. Apongozi a Simoni anali gone, akudwala malungo, ndipo nthawi yomweyo anthu adamufotokozera za matendawo. Yesu adapita nakawagwira pa dzanja amaiwo nkuwadzutsa, ndipo malungowo adatha. Pomwepo amai aja adayamba kukonzera anthu chakudya. Madzulo amenewo, dzuwa litalowa, anthu ada-bwera kwa Yesu ndi anzao onse ovutika, ndi ogwidwa ndi mizimu yoipa. Anthu a m’mudzi monsemo adaasonkhana pakhomopo. Yesu adachiritsa ambiri amene ankavutika ndi matenda osiyanasiyana, ndipo adatulutsa mizimu yoipa yambiri. Koma mizimuyo ankailetsa kuti isalankhule, chifukwa idaamzindikira. M’mamawa ndithu, kusanache, Yesu adadzuka napita kumalo kosapitapita anthu. Kumeneko adakapemphera. Simoni ndi anzake aja adamlondola komweko. Atampeza adamuuza kuti, “tiyeni tinke ku midzi ina kufupi konkuno, ndikalalike mau kumenekonso, pakuti ndizo ndidadzera.” Tsono adapita nalalika m’nyumba zamapemphero ku Galileya konseko, ndipo ankatulutsa mizimu yoipa.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, lero Yesu Khristu watiwonetsa kukoma mtima kwa Mulungu kofuna kupulumutsa anthu onse. Tiyeni tipemphere mogwirizana ndi mosakaika.
1. Atsogoleri a Mpingo apitirize kulalika Mthenga wa Yesu modzipereka, potsata chitsanzo cha Paulo Woyera.
Atate, tiwonetseni chifundo chanu, ndipo tidzapulumuka.
2. Akulu olamulira maiko okwera akhale otekeseka ndi ubwino wa anthu a m’maiko ena, pakuwagawirako zabwino zomwe Iwo akuzisowa.
Atate, tiwonetseni chifundo chanu, ndipo tidzapulumuka.
3. Anthu odwala asaleke kukhulupirira Mulungu ndi kulimba mtima polandira chisamaliro kuchokera kwa anzawo a chifundo.
Atate, tiwonetseni chifundo chanu, ndipo tidzapulumuka.
4. Ife tomwe tilimbikire kufalitsa Mthenga Wabwino wa chipulumutso, makamaka pothandiza anthu ovutika ndi poonetsa onse mtima waubale.
Atate, tiwonetseni chifundo chanu, ndipo tidzapulumuka.
Atate, popereka kwa Inu mapemphero athuwa, tikuyamika chifundo chanu chofuna kupulumutsa anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment