MAU WOYAMBA A M’BUKU LOYERA: MAWU A M’BUKU LA DEUTORONOMO: DEUTORONOMO 18:15 – 20. (Ndidzawatumizira mneneri ndipo adzalankhula m’dzina langa).
Mose adawauza anthu kuti: “Chauta adzakutumizirani mneneri wonga ine wochokera mwa inu amene, ndipo mudzayenera kumumvera iyeyo. Pa tsiku lija mudaasonkhana pa phiri la Horebuli, mudaapempha kuti, ‘tisamvenso Chauta, Mulungu wathu, akulankhula, ngakhale kuwonanso moto waukulu choterewu, kuti tingafe.’ Apo Chauta adaandiwuza kuti, ‘zonse zimene apemphazi anena mwanzeru. Ndidzawatumizira mneneri wonga iwe, wochokera mwa iwo amene. Ndidzamuuza zoti anene, ndipo iyeyo azidzauza anthu zonse zimene ndikumlamula. Mneneriyo akalankhula m’dzina langa, Ine ndidzalanga aliyense wosamvera mau angawo. Koma mneneri wina aliyense woyerekeza kulankhula m’dzina langa, Ine osamulamula kuti atero, aphedwe. Ndipo ayeneranso kuphedwa mneneri wina aliyense wolankhula m’dzina la milungu ina.’”
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
---------------------------------------
NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 95: 01 – 02, 06 – 09.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
Bwerani, timuimbire Chauta,
Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa,
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze,
Timuimbire nyimbo zotamanda.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
Bwerani, timpembedze ndi kumlambira,
Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu,
Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ndife anthu a pa busa lake,
Ndife nkhosa zodyera m’manja mwake.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
Lero mukadamverako mau ake!
Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja,
Monganso tsiku lija ku Masa m’chipululu muja,
Pamene makolo anu adandiputa mondiyesa
Ngakhale anali ataona ntchito zanga.
Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu.
------------------------------------------------
MAU ACHIWIRI A M’BUKU LOYERA: MAU A M’KALATA YOYAMBA YA PAULO WOYERA KWA AKORINTO: 01 AKORINTO 07: 32 – 35. (Mkazi wosakwatiwa, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m’mene angakondweretsere Ambuye).
Abale, ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhawa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye. Koma munthu wokwatira amateketseka ndi zapansi pano, kuganiza za m’mene angakondweretsere mkazi wake. Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangoteketseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m’thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansi pano, kuganiza za m’mene angakondweretsere mwamuna wake. Ndikunenatu zimenezi kufuna kuti ndikuthandizeni, osati ndikuletseni ufulu wanu ai. Makamaka ndifuna kuti muzichita zonse moyenera, ndipo kuti muzidzipereka kwathunthu potumikira Ambuye.
Mau a Ambuye.......Tithokoze Mulungu.
--------------------------------------
NYIMBO YA MTHENGA WABWINO – MATEYO 04:16,
Alleluia, Alleluia – Anthu okhala mu mdima aona kuwala kwakukulu. Anthu okhala m’dziko la mdima wabii wa imfa, kuwala kwawaonekera. – Alleluia, Alleluia.
--------------------------------------
MTHENGA WABWINO: MTHENGA WABWINO MONGA ANALEMBERA MARKO WOYERA: MARKO 01: 21 – 28. (Ankaphunzitsa moonetsa ulamuliro).
Pa nthawi yomweyo, onsewo ankapita ku Kapernao. Tsono litafika tsiku la sabata. Yesu adalowa m’nyumba yamapemphero, nayamba kuphunzitsa. Zophunzitsa zake anthu zidaawagwira mtima kwambiri, chifukwa ankaphunzitsa moonetsa ulamuliro, kusiyana ndi m’mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo. M’nyumba yamapempheroyo mudaalowa munthu wogwidwa ndi mzimu womuipitsa. Adalankhula mokuwa kuti, “kodi takuputani chiyani, Inu Yesu wa ku Nazerete? Kodi mwadzatiwononga? Ndakudziwani, ndinu Woyera uja wa Mulungu.” Koma Yesu adazazira mzimu woipawo, adati, “khala chete, tuluka mwa munthu yu.” Apo mzimu womuipitsa uja udamugwedeza kwamphamvu munthuyo, ndipo udakuwa koposa, nkutuluka. Anthu onse aja adazizwa kwambiri, mpaka kumafunsana kuti, “kodi zimenezi nzotani? Zophunzitsa zamtundutu zimenezi! Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu, ndipo ikumumveradi.” Mwansanga mbiri yake idawanda ponseponse ku dera lonse la ku Galileya.
Mthenga wa Ambuye…Ulemu kwa Inu Ambuye Yesu Khristu.
--------------------------------------
Mapemphero a Akhristu.
Abale, monga Mulungu walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake, ifenso tsopano timupemphe kudzera mwa Yesu Khristu yemweyo kuti alimbikitse chikhulupiriro chathu:
1. Atsogoleri a Mpingo alalike mau a Mulungu mokhulupirika ndi mopanda mantha, pokumbukira kuti alikupitiriza ntchito ya Yesu Khristu.
Tikupemphani, mutivomereze.
2. Akulu olamula maiko akhale otekeseka ndi ubwino wa anthu ao, asawapondereze kapena kuwalanda ufulu, koma awatsogolere m’njira ya mtendere.
Tikupemphani, mutivomereze.
3. Anzathu odwala ndi ena onse ovutika m’mitima mwao apeze mwa Yesu Khristu mphamvu zopirira mavuto pokhulupirira ntchito zake zowapulumutsa.
Tikupemphani, mutivomereze.
4. Ife tonse tili muno tidziwe kumanga moyo wathu pa chikondi cha Ambuye, pomatekeseka ndi ntchito zodzetsa ufumu wa Mulungu pakati pa anzathu.
Tikupemphani, mutivomereze.
Atate, potula mapemphero athuwa m’manja mwanu, tikuyamikani chifundo chanu chofuna kupulumutsa anthu onse. Mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
#Pax_et_Gaudium_in_Domino.
Facebook: https://www.facebook.com/Mawu-a-Lamulungu-Lililonse-a-Chikatolika-mu-Chichewa-109826477067295
No comments:
Post a Comment